Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudzilemekeza

Kudzilemekeza

N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZILEMEKEZA N’KOFUNIKA?

Anthu amene amadzilemekeza amakhala olimba mtima akamakumana ndi mavuto ndipo sataya mtima msanga.

  • Kafukufuku amasonyeza kuti anthu amene samadziona moyenera akhoza kuvutika ndi nkhawa, matenda ovutika maganizo kapena matenda ovutika kudya. Akhozanso kuyamba kuledzera kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.

  • Anthu amene amadzilemekeza amapewa kudziyerekezera ndi ena zomwe zimawachititsa kuti azikhala bwino ndi anthu ndipo pamapeto pake amakhala mabwenzi awo a pamtima. Pomwe anthu amene sadzilemekeza sakhala bwino ndi anthu ndipo maubwenzi awo amasokonekera.

  • Anthu amene amadzilemekeza amakhalabe opirira ngakhale pamene akukumana ndi mavuto ndipo salola kuti zofooketsa ziwalepheretse kukwaniritsa zolinga zawo. Pomwe anthu amene sadzilemekeza amaona mavuto ang’onoang’ono kukhala aakulu kwambiri. Zimenezi zingawachititse kuti ataye mtima mosavuta.

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZIDZILEMEKEZA

Muzisankha anzanu amene angamakulimbikitseni. Muzicheza ndi anthu aulemu amene angakhale ofunitsitsa kuti zinthu zikuyendereni bwino ndipo angakulimbikitseni.

“Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse, ndipo ndi m’bale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

Muzithandiza ena. Mukakhala okoma mtima n’kumachitira ena zabwino kuphatikizapo amene sangakubwezereni, mudzakhala osangalala kwambiri chifukwa chopatsa. Mudzakhalabe osangalala ngakhale ena asaone zabwino zimene mukuchitazo.

“Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.

Muzithandiza ana anu kuti azidzilemekeza. Njira imodzi imene mungachitire zimenezi ndi kuwalola kuti azithana ndi mavuto paokha mogwirizana ndi msinkhu wawo. Zimenezi zimathandiza anawo kuphunzira mmene angathetsere mavuto awo. Akaphunzira zimenezi amayamba kudzilemekeza ndipo zinthu zimawayendera bwino akadzakula.

“Phunzitsa mwana kuti aziyenda m’njira imene akuyenera kuyendamo. Ngakhale akadzakalamba sadzachoka m’njira imeneyo.”—Miyambo 22:6.

ZIMENE TIKUCHITA POTHANDIZA ANTHU KUTI AZIDZILEMEKEZA

Misonkhano ya Mboni za Yehova komanso pulogalamu yawo yophunzitsa Baibulo, imathandiza anthu kuti asinthe moyo wawo komanso azidzilemekeza.

MISONKHANO YATHU YA MLUNGU ULIWONSE

Pamisonkhano yathu ya mlungu uliwonse, timamvetsera nkhani za m’Baibulo zimene nthawi zambiri zimakhala ndi malangizo otithandiza kuti tizidzilemekeza. Misonkhano yathu ndi yaulere ndiponso aliyense ndi wolandiridwa. Mwachitsanzo, ku misonkhano yathu mudzaphunzira . . .

  • chifukwa chake Mulungu amakuonani kuti ndinu wofunika kwambiri

  • zimene mungachite kuti mudziwe cholinga chenicheni cha moyo

  • zimene mungachite kuti mupeze anzanu abwino komanso muzigwirizana nawo kwambiri

Mudzapezanso anzanu enieni omwe ‘amasamalirana.’—1 Akorinto 12:25, 26.

Kuti mudziwe zambiri zokhudza misonkhano yathu, fufuzani vidiyo yamutu wakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? pa jw.org.

PHUNZIRO LA BAIBULO

Timaphunzira Baibulo ndi anthu kwaulere pogwiritsa ntchito buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. M’bukuli muli malemba ambiri, limafotokoza mfundo momveka bwino, muli mafunso othandiza kuganiza, mavidiyo okopa chidwi komanso zithunzi zokongola. Kuphunzira Baibulo kumathandiza anthu kuti azidzipatsa ulemu komanso asinthe moyo wawo.

Kuti mudziwe mmene kuphunzira Baibulo kungakuthandizireni fufuzani vidiyo yamutu wakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? pa jw.org.