Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulemekeza Ena

Kulemekeza Ena

N’CHIFUKWA CHIYANI KULEMEKEZA ENA N’KOFUNIKA?

Kulemekeza ena kumathandiza kuti zinthu zisaipe kwambiri pakakhala kusamvana kwinakwake.

  • Mwambi wina wa m’Baibulo umanena kuti: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Kulankhula kapena kuchita zinthu mopanda ulemu kumangokolezera moto ndipo nthawi zambiri zotsatirapo zake zimakhala zoipa kwambiri.

  • Yesu ananena kuti: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.” (Mateyu 12:34) Kulankhula mopanda ulemu kwa ena, kungasonyeze kuti tili ndi vuto lalikulu. Kungasonyeze kuti timaona molakwika anthu amene timasiyana nawo mtundu, chikhalidwe, kochokera kapena omwe timasiyana nawo zochita.

    Kafukufuku yemwe anachitika posachedwapa kwa anthu oposa 32,000 ochokera m’mayiko 28, anthu 65 pa 100 alionse ananena kuti mosiyana ndi kale, panopa m’pamene anthu alibiretu ulemu.

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZILEMEKEZA ENA

Kaya muli kusukulu kapena kuntchito, muzilemekeza anthu onse ngakhale amene amaona zinthu mosiyana ndi inu. Muziganizira zinthu zimene nonse mumaziona mofanana. Zimenezi zingakuthandizeni kuti musamawaone molakwika komanso kuti muzipewa kuwaweruza.

“Siyani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe.”—Mateyu 7:1.

Muzichitira ena zinthu zimene mumafuna kuti akuchitireni. Ngati mumaganizira ena komanso kuwachitira zinthu mokoma mtima nawonso adzakuchitirani zomwezo.

“Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”—Luka 6:31.

Muzikhululuka. Musamafulumire kuganiza kuti munthu winawake walankhula kapena wachita zinthu zinazake mwadala n’cholinga choti akukhumudwitseni.

“Kuzindikira kumachititsa kuti munthu abweze mkwiyo wake, ndipo kunyalanyaza cholakwa kumamʼchititsa kukhala wokongola.”—Miyambo 19:11.

ZIMENE TIKUCHITA POLEMEKEZA ENA

A Mboni za Yehova amalemekeza ena m’madera amene amakhala komanso kumene amagwira ntchito.

Timaphunzira Baibulo kwaulere ndi anthu onse koma sitiwakakamiza kutsatira zimene timakhulupirira kapena maganizo athu. M’malomwake, timayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti tikamauza ena uthenga wathu, tizichita zimenezo “mofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.”—1 Petulo 3:15; 2 Timoteyo 2:24.

Sitisala anthu ndipo kumisonkhano yathu timalandira aliyense amene akufuna kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa. Timayesetsa kukhala ololera komanso “kuchitira ulemu anthu onse.”—1 Petulo 2:17, Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu.

Timamvera akuluakulu aboma amene amatilamulira. (Aroma 13:1) Timamvera malamulo komanso timakhoma misonkho. Ngakhale kuti sitilowerera ndale, timalemekeza ufulu wa aliyense woti asankhe zimene akufuna pa nkhani zandale.