Mbalame Zokongola Kwambiri
AKATSWIRI ofufuza zinthu a ku Europe anafika ku Central komanso ku South America cha m’ma 1400, ndipo anachita chidwi kwambiri ndi mtundu winawake wa mbalame. Gulu la mbalamezi likamauluka, m’nkhalango mumakongola kwambiri. Mbalamezi zomwe zimakhala ndi chipsepse chachitali, zili m’gulu la mbalame zotchedwa zinkhwe kapena kuti mapaloti ndipo zimapezeka kumadera otentha a ku America. Patadutsa nthawi yochepa chifikireni ofufuza aja, zithunzi za mbalamezi zinayamba kujambulidwa pa mapu a m’maderawa.
Mbalame zazimuna ndi zazikazi zomwe zimakhala ndi mitundu yosiyanasiyana, ndipo zimenezi sizichitika kawirikawiri ndi mitundu ina ya mbalame. Mbalamezi ndi zanzeru, zimakonda kukhala m’magulu ndipo zimalira mwaphokoso kwambiri. M’mamawa, zimachoka m’zisa zawo kukasaka zakudya zili m’magulu moti pagulu lililonse zimatha kukhalapo pafupifupi 30. Zikapeza zakudya zimapalasa kenako n’kutola ndi milomo yomwe ndi ikuluikulu komanso yopindika ndipo zimathanso kuswa mtedza ndi milomoyi. Zikamaliza kudya, zimapita m’mbali mwa mtsinje kukadya dongo. Dongoli limathandiza mbalamezi pochotsa poizoni m’zakudya zomwe zadya ndiponso limapereka zinthu zina zofunika m’thupi la mbalamezi.
“Chilichonse [Mulungu] anachipanga chokongola ndiponso pa nthawi yake.”
Yaimuna ndi yaikazi zimakhala limodzi kwa moyo wonse ndipo zimathandizana posamalira ana. Mitundu ingapo ya mbalamezi, imakhala
m’mabowo a m’mitengo, m’mayenje a m’mbali mwa mitsinje, komanso a pachulu. Kawirikawiri mbalame yaimuna ndi yaikazi zimakonda kukonzana nthenga. Ana a mbalamezi amakhala atakula akatha miyezi 6, koma amakhalabe ndi makolo awo kwa zaka zitatu. Mbalamezi zimafika zaka zapakati pa 30 ndi 40. Koma zikakhala zoweta, zimatha kukhala ndi moyo zaka zoposa 60. Mbalamezi zilipo zamitundu 18 ndipo mitundu ina ndi iyi.