ZOCHITIKA PADZIKOLI
Nkhani Zokhudza Anthu
Pa nkhani zokhudza banja, kodi mumaona kuti malangizo a m’Baibulo ndi othandiza kapena ndi osathandiza kwenikweni? Tiyeni tione zotsatira za kafukufuku waposachedwapa ndipo tiyerekeze ndi zimene Baibulo limanena.
India
Kafukufuku amene anachitika mu 2014 anasonyeza kuti, ku India achinyamata 61 pa 100 alionse azaka za pakati pa 18 mpaka 25 amaona kuti kugonana asanalowe m’banja “kulibe vuto lililonse.” Dokotala wina wamumzinda wa Mumbai anauza nyuzipepala ina kuti iyeyo amaona kuti “achinyamata akakhala pa chibwenzi sizitanthauza kuti ali ndi maganizo odzakwatirana. Komanso kaya akufuna kungogonana tsiku limodzi kapena kumangokhala limodzi, palibe chifukwa choti agwirizane kaye kuti adzakwatirana.”
MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA: Kodi ndi anthu ati amene amakonda kutenga matenda opatsirana pogonana komanso amene amakhala ndi vuto lovutika maganizo? Okwatirana kapena amene amagonana asanalowe m’banja?—1 Akorinto 6:18.
Denmark
Anthu ambiri azaka 35 mpaka 50, amene amakangana pafupipafupi ndi anthu am’banja lawo, amakhala pangozi yoti akhoza kufa msanga. Ochita kafukufuku apayunivesite ina anagwiritsa ntchito anthu azaka zimenezi okwana 10,000. Patatha zaka 11, anapeza kuti amene ankakangana pafupipafupi akhoza kufa msanga kusiyana ndi amene sankakanganakangana. Amene analemba zotsatira za kafukufukuyu anati kukambirana mwamtendere pakakhala mavuto “kungathandize kuti munthu asafe msanga.”
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Aliyense wosalankhulapo mawu ake ndi wodziwa zinthu, ndipo munthu wozindikira amakhala wofatsa.”—Miyambo 17:27.
United States
Kafukufuku wina amene anachitika pa mabanja atsopano okwana 564 a ku Louisiana, anasonyeza kuti mabanja a anthu amene chibwenzi chawo chinkatha n’kuyambiranso, akhoza kutha pasanathe zaka 5. Mabanja oterewa amakonda kukangana komanso anthu ake sakhutira ndi banja lawo.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Mateyu 19:6.