Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kugwira ntchito mwakhama kuli ngati kuchita masewera olimbitsa thupi. Kungakuthandizeni panopa komanso mukadzakula

ACHINYAMATA

11: Kulimbikira Ntchito

11: Kulimbikira Ntchito

ZIMENE ZIMACHITIKA

Anthu olimbikira ntchito sakhala a manja lende. Koma amakhala akhama kuti apeze zofunika pa moyo wawo komanso kuti akwanitse kuthandiza ena, ngakhale ntchitoyo itakhala yonyozeka.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUGANIZIRA NKHANIYI N’KOFUNIKA?

Kuti tipeze zofunika pa moyo timafunika kugwira ntchito basi. Ngakhale kuti anthu ambiri sasangalala ndi kugwira ntchito, munthu amene ndi wakhama zimamuyendera bwino.​—Mlaliki 3:13.

Reyon ananena kuti: “Ndimaona kuti munthu wakhama pa ntchito amakhala wosangalala komanso amakhala ndi mtendere wamumtima. Zimenezi zimandichititsa kuti ndizikonda kwambiri kugwira ntchito. Ndipotu anthu amalemekeza munthu amene amagwira ntchito bwino.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kugwira ntchito iliyonse kumapindulitsa.”​—Miyambo 14:23.

ZIMENE MUNGACHITE

Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kuti kugwira ntchito kuzikusangalatsani.

Muziyesetsa kugwira bwino ntchito yanu. Kaya mukugwira ntchito yolembedwa, ya pakhomo kapena kulemba homuweki, muziikirapo mtima kwambiri. Mukamaliza kugwira ntchitoyo, muziganizira zimene mungachite kuti nthawi ina mudzaigwire mwachangu komanso mwaluso. Mukamachita zimenezi mudzakhala osangalala kwambiri.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kodi wamuona munthu waluso pa ntchito yake? Iye adzaima pamaso pa mafumu. Sadzaima pamaso pa anthu wamba.”​—Miyambo 22:29.

Muziganizira mmene ntchitoyo ingathandizire ena. Nthawi zambiri mukamakwaniritsa udindo wanu zimathandizanso anthu ena. Mwachitsanzo, mukamagwira ntchito zapakhomo mwakhama, mumachepetsako ntchito za anthu ena pakhomopo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

Muzichita zoposa zimene mumafunika kuchita. M’malo mogwira ntchito yokhayo yomwe mwauzidwa, muzionanso zina zomwe mungawonjezere pa ntchitoyo. Mukatero mumasonyeza kuti ndinu munthu wodziimira panokha chifukwa simuchita kukakamizidwa kuti mugwire ntchito yowonjezerayo.​—Mateyu 5:41.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Chabwino chimene ungachite chisakhale chokukakamiza, koma uchite mwa kufuna kwa mtima wako.”​—Filimoni 14.

Muzikhala ndi malire. Anthu olimbikira ntchito sakhala aulesi komanso sikuti amangokhalira kugwira ntchitoyo mpaka kufika pofuna kufa nayo. Amakhala ndi nthawi yogwira ntchito komanso yopumako.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”​—Mlaliki 4:6.