Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mukamayesetsa kuteteza mbiri yanu mudzakhalabe olimba pokumana ndi mavuto okhala ngati chimphepo

ACHINYAMATA

9: Mbiri Yanu

9: Mbiri Yanu

ZIMENE ZIMACHITIKA

Kudziwa munthu sikutanthauza kungomudziwa dzina kapena maonekedwe ake. Koma zimakhudza mbiri yomwe munthuyo ali nayo pa nkhani ya khalidwe lake, zimene amakhulupirira komanso mmene amachitira zinthu ndi ena.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUGANIZIRA NKHANIYI N’KOFUNIKA?

Munthu amene amateteza mbiri yake, amayesetsa kutsatira zimene amakhulupirira ndipo salola kuti anzake azingomusankhira zochita.

Adrian ananena kuti: “Anthu ambiri amakhala ngati zidole za m’mashopu zomwe zimachita kudalira munthu wina kuti azisankhire zovala.”

Courtney ananena kuti: “Ndimaona kuti ndi bwino kuchita zinthu zoyenera ngakhale zitakhala zovuta. Ndimatha kudziwa anzanga enieni ndikaona zimene amachita komanso poona mmene ndimamasukira nawo.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Musamatengere nzeru za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu.”​—Aroma 12:2.

ZIMENE MUNGACHITE

Muyenera kudzifufuza kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani panopa komanso kuti mukufuna kudzakhala munthu wotani. Mungachite zimenezi poona zimene mumachita bwino, zimene mumalephera komanso zimene mumakhulupirira. Mafunso otsatirawa angakuthandizeni.

Zimene mumachita bwino: Kodi ndili ndi luso lotani? Kodi ndi zinthu ziti zomwe ndimachita bwino? (Mungaganizire zinthu monga: Kusunga nthawi, kudziletsa, kugwira ntchito mwakhama kapenanso kukhala opatsa) Nanga kodi panopa ndi zinthu ziti zabwino zomwe ndikuchita?

TAYESANI IZI: Ngati panokha mukulephera kupeza zinthu zabwino zomwe mumachita kapena kulankhula, funsani makolo anu kapena mnzanu wodalirika kuti akuuzeni.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Koma aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake, osati modziyerekezera ndi munthu wina.”​—Agalatiya 6:4.

Zimene mumalephera: Kodi ndi zinthu ziti zomwe ndikufunika kuyesetsa kukonza? Kodi ndi pa nthawi iti imene ndimayesedwa kuti ndichite zoipa? Kodi ndiyenera kukhala wodziletsa kwambiri pa zinthu ziti?

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Tikanena kuti: ‘Tilibe uchimo,’ ndiye kuti tikudzinamiza ndipo mwa ife mulibe choonadi.”​—1 Yohane 1:8.

Zimene mumakhulupirira: Kodi ndimagwiritsa ntchito mfundo zotani, nanga n’chifukwa chiyani ndimayendera mfundozi? Kodi ndimakhulupirira Mulungu? N’chiyani chimandipangitsa kukhulupirira kuti alipodi? Ndi zinthu ziti zomwe ndimaona kuti ndi zopanda chilungamo, nanga n’chifukwa chiyani ndimaona choncho? Kodi ndimakhulupirira kuti kutsogoloku kudzachitika zotani?

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kuganiza bwino kudzakuyang’anira, ndipo kuzindikira kudzakuteteza.”​—Miyambo 2:11.