Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Oyamba

Mawu Oyamba

Makhalidwe 6 Amene Muyenera Kuphunzitsa Ana Anu

Kodi mumafuna kuti mwana wanu azidzadziwika ngati munthu wotani akadzakula?

  • Wodziletsa?

  • Wodzichepetsa?

  • Wopirira?

  • Wodalirika?

  • Woganiza bwino?

  • Wokhulupirika?

Ana sangakhale ndi makhalidwe amenewa paokha. Amafunika kuti inuyo makolo muwathandize.

Magaziniyi yafotokoza makhalidwe ofunika 6 omwe muyenera kuphunzitsa ana anu kuti adzakhale anthu odalirika.