Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | Kodi Baibulo Ndi Lochokeradi Kwa Mulungu?

Kodi Baibulo ‘Linauziridwadi Ndi Mulungu’?

Kodi Baibulo ‘Linauziridwadi Ndi Mulungu’?

KODI mumakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu ochokeradi kwa Mulungu? Kapena mumaona kuti ndi buku lomwe munangolembedwa maganizo a anthu?

Akhristu ambiri ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani imeneyi. Mwachitsanzo mu 2014, kafukufuku amene bungwe lina linachita ku United States anasonyeza kuti anthu ambiri amaona kuti mwina Baibulo linachokeradi kwa Mulungu. Komanso munthu mmodzi pa anthu 5 omwe anafunsidwawo ananena kuti amaona kuti Baibulo “ndi buku lanthano, longofotokoza mbiri ya anthu akale komanso lolembedwa ndi anthu.” Popeza anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhaniyi, ndi bwino kufufuza ngati Baibulo linauziridwadi ndi Mulungu.​—2 Timoteyo 3:16.

KODI ‘KUUZIRIDWA’ KUMATANTHAUZA CHIYANI?

Baibulo linapangidwa ndi mabuku ang’onoang’ono 66 omwe analembedwa ndi anthu 40 kwa zaka zoposa 1,600. Ndiye ngati Baibulo linalembedwa ndi anthu, zingatheke bwanji kuti likhale buku ‘louziridwa ndi Mulungu’? Mwachidule, mawu akuti Baibulo ‘linauziridwa ndi Mulungu,’ amatanthauza kuti uthenga womwe anthu analembawo, unkachokera kwa Mulungu. Baibulo limanena lokha kuti: “Anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” (2 Petulo 1:21) Mulungu ankapereka uthenga kwa olemba Baibulowo pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera womwe ndi mphamvu yake yosaoneka. Zimenezi n’zofanana ndi zimene bwana angachite pouza wantchito wake kuti amulembere kalata. Mwiniwake wa kalatayo ndi bwanayo chifukwa chakuti uthenga umene uli m’kalatayo ndi wake osati wa wantchito wakeyo.

Anthu ena omwe analemba nawo Baibulo ankamva Mulungu akuwalankhula pogwiritsa ntchito mngelo. Ena ankaona masomphenya ochokera kwa Mulungu. Nthawi zina Mulungu ankawauzanso uthenga kudzera m’maloto. Ngakhale kuti Mulungu ankalola anthuwo kusankha mawu oti agwiritse ntchito polemba, nthawi zina ankachita kuwauza mawu enieni oti alembe. Kaya uthengawo unkawafika bwanji, zomwe anthuwo analemba zinali zochokera kwa Mulungu osati m’maganizo awo.

Koma kodi tingatsimikize bwanji kuti zimene anthuwo analemba m’Baibulo zinalidi zouziridwa ndi Mulungu? Tikambirana zinthu zitatu zomwe zingatitsimikizire kuti uthenga wa m’Baibulo unachokeradi kwa Mulungu.