NKHANI YA PACHIKUTO | KODI BAIBULO NDI LOCHOKERADI KWA MULUNGU?
Baibulo Limanena Zinthu Molondola
Ndi Lolondola pa Nkhani za Sayansi
NGAKHALE kuti Baibulo si buku lophunzitsa zasayansi, likamafotokoza zinthu za m’chilengedwe, limanena zolondola. Mwachitsanzo, tiyeni tione zomwe limanena pa nkhani zokhudza nyengo ndi chibadwa cha zinthu zamoyo.
ZOKHUDZA NYENGO—MMENE MVULA IMAPANGIKIRA
Baibulo limanena kuti: “[Mulungu] amakoka madontho a madzi. Madonthowo amasefeka n’kutsika ngati mvula ndi nkhungu, moti mitambo imakha.”—Yobu 36:27, 28.
Palembali, Baibulo likunena zinthu zitatu zomwe zimachitika kuti mvula ipangike. Choyamba, Mulungu “amakoka madontho a madzi” pogwiritsa ntchito dzuwa lomwe anapanga. Chachiwiri, madzi omwe amakokedwa kupita kumwamba amakapanga mitambo. Ndipo chachitatu, mitamboyo imasintha n’kukhala mvula kapena nkhungu yomwe imagwa padzikoli. Mpaka pano akatswiri a zanyengo samvetsa bwinobwino zonse zomwe zimachitika kuti mvula ipangike. N’zochititsa chidwi kuti Baibulo limafunsa kuti: “Ndani angamvetse mmene mitambo imatambasukira?” (Yobu 36:29) Mulungu amene analenga chilengedwechi amadziwa zimene zimachitika kuti mvula ipangike ndipo ndi amene anachititsa kuti anthu amene analemba Baibulo, afotokoze molondola zimene zimachitika. Ndipotu anathandiza anthuwo kulemba mfundo zimenezi kalekale kwambiri asayansi asanazitulukire n’komwe.
ZOKHUDZA CHIBADWA—MMENE MWANA AMAPANGIKIRA M’MIMBA
Mfumu Davide yemwe analemba nawo Baibulo anauza Mulungu kuti: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu.” (Salimo 139:16) Davide analemba lembali ngati ndakatulo ndipo anafotokoza zimene zimachitika m’mimba kuti mwana apangike. Kuti mwana apangike komanso kukula, zimakhala ngati pali malangizo a “m’buku” linalake omwe amatsatiridwa. Komatu Mfumu Davide analemba zimenezi pafupifupi zaka 3,000 zapitazo.
Koma ndi cham’katikati mwa zaka za m’ma 1800, pamene wasayansi wina wa ku Austria dzina lake Gregor Mendel, anatulukira zimene zimachitika kuti mwana azitha kutengera chibadwa cha makolo ake. Ndipo mu April 2003, m’pamenenso asayansi anamaliza kuchita kafukufuku wofuna kudziwa zonse zimene zimachitika kuti munthu apangike. Asayansi amanena kuti malangizo okhudza mmene munthu adzakhalire akadzabadwa omwe amapezeka m’maselo, ali ngati buku lomwe linalembedwa potsatira zilembo za afabeti. Ndipo chilembo chilichonse chimakhala ndi malangizo ofotokoza mmene mwanayo adzakhalire. Zinthu ngati ubongo, mtima ndi ziwalo zina ngati manja ndi miyendo, zimapangika potsatira malangizo okhudza chibadwa cha munthu ndipo chilichonse chimapangika pa nthawi yake komanso mosaphonyetsa. Mogwirizana ndi zimene Baibulo linanena zija, asayansiwa anatchulanso malangizo okhudza chibadwa cha munthu amenewa kuti “buku la moyo.” Kodi zinatheka bwanji kuti Davide alembe molondola zimene zimachitikazi? Mfumuyo inafotokoza chifukwa chake kuti: “Mzimu wa Yehova unandilankhulitsa, ndipo mawu ake anali palilime langa.” *—2 Samueli 23:2.
Likaneneratu Zam’tsogolo Zimadzachitikadi
NDI ZOVUTA kwambiri ndiponso n’zosatheka kudziwa kuti kudzakhala ufumu kapena mzinda winawake komanso kudziwa nthawi imene ufumu kapena mzindawo udzathe. N’zosathekanso kufotokoza mwatsatanetsatane kuti ufumu kapena mzindawo udzagwa bwanji. Komatu nthawi ina Baibulo linaneneratu za kuwonongedwa kwa maulamuliro ndi mizinda ina ikuluikulu komanso mmene zidzachitikire. Tiyeni tione zitsanzo ziwiri zomwe linaneneratu.
KUWONONGEDWA KWA MZINDA WA BABULO
Mzinda wakale wa Babulo unali likulu la ufumu wamphamvu kwambiri ndipo ufumuwo unalamulira mayiko akumadzulo kwa Asia kwa zaka zambiri. Ndipo nthawi ina, mzindawu ndi umene unali waukulu kwambiri padziko lonse. Komabe kudakali zaka 200, Mulungu anagwiritsa ntchito Yesaya kulemba zoti munthu wina dzina lake Koresi adzawononga mzindawo ndipo simudzakhalanso anthu mpaka kalekale. (Yesaya 13:17-20; 44:27, 28; 45:1, 2) Kodi zimenezi zinachitikadi?
Mu October chaka cha 539 B.C.E., Koresi anagonjetsa mzinda wa Babulo usiku umodzi wokha. Patapita nthawi, ngalande zomwe zinkagwiritsidwa ntchito pa ulimi wothirira zinaumiratu chifukwa choti panalibenso wozisamalira. Pofika mu 200 C.E., n’kuti kudera lonseli kulibiretu anthu moti mpaka pano pamalo pomwe panali mzinda wa Babulo pali mabwinja okhaokha. Mzindawu unakhaladi ndendende ngati mmene Baibulo linaneneratu kuti “dziko lonselo lidzakhala bwinja.”—Yeremiya 50:13.
Kodi Yesaya anakwanitsa bwanji kulemba nkhaniyi kudakali zaka zambirimbiri izi zisanachitike? Baibulo limayankha mmene zinakhalira kuti: “Uwu ndi uthenga wokhudza Babulo, umene Yesaya mwana wa Amozi anaona m’masomphenya.”—Yesaya 13:1.
NINEVE ADZAKHALA “DZIKO LOPANDA MADZI NGATI CHIPULULU”
Mzinda wa Nineve unali likulu la ufumu wa Asuri ndipo unali ndi zinthu zambiri zopangidwa mwaluso. Mzindawu unalinso wotchuka chifukwa kunali zinthu zambiri zochititsa chidwi monga minda ya maluwa, misewu, akachisi ndi nyumba zikuluzikulu. Komabe nthawi ina mneneri Zefaniya ananeneratu kuti mzinda wamphamvuwo udzakhala “dziko lopanda madzi ngati chipululu.”—Zefaniya 2:13-15.
Mzinda wa Nineve unawonongedwa wonse mu 600 B.C.E. ndi asilikali a ku Babulo mogwirizana ndi asilikali a Amedi. Buku lina linafotokoza kuti panadutsa zaka 2,500 anthu asakukumbukiranso zoti kunali mzinda wa Nineve. Palibe aliyense amene ankatchulanso za mzindawu mpaka cha m’ma 1800 pamene akatswiri ofukula zinthu zakale anafukula mabwinja ake. Panopa zinthu zambiri zapamalowa zikuwonongeka komanso kubedwa moti bungwe lina linachenjeza kuti: “Ngati sitingasamale, m’tsogolomu zinthu zakale za mzinda wa Nineve sizidzapezekanso.”—Global Heritage Fund.
Kodi Zefaniya anakwanitsa bwanji kuneneratu zimenezi? Mneneriyu ananena kuti “Yehova analankhula kudzera mwa [iye].”—Zefaniya 1:1.
Baibulo Lili ndi Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri
BAIBULO lili ndi mayankho ogwira mtima a mafunso ofunika omwe timakhala nawo. Tiyeni tione ena mwa mafunsowa komanso zimene Baibulo limanena.
N’CHIFUKWA CHIYANI PADZIKOLI PALI ZINTHU ZOIPA KOMANSO MAVUTO AMBIRI?
M’Baibulo muli Malemba ambiri amene amanena za zinthu zoipa komanso mavuto omwe anthufe timakumana nawo. Mwachitsanzo, limafotokoza kuti:
-
“Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”—Mlaliki 8:9.
Maboma a anthu omwe ndi achinyengo komanso osadalirika amachititsa kuti anthu azivutika kwambiri.
-
“Nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.”—Mlaliki 9:11.
Zinthu zosayembekezereka ngati matenda aakulu, ngozi kapenanso masoka, zikhoza kuchitikira aliyense, kulikonse komanso pa nthawi iliyonse.
-
‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo.’—Aroma 5:12.
Adamu ndi Hava atangolengedwa, anali anthu angwiro ndipo imfa kunalibe. Komabe uchimo ‘unalowa m’dziko,’ anthu oyambirirawo atasankha kuti asamvere Mulungu.
Mulungu analonjeza anthu kudzera m’Baibulo kuti adzathetsa zoipa zonse komanso kuti “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
KODI CHIMACHITIKA N’CHIYANI MUNTHU AKAMWALIRA?
Baibulo limafotokoza kuti munthu akamwalira sadziwa chilichonse ndiponso sangathe kuchita chilichonse. Lemba la Mlaliki 9:5 limati: “Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.” Munthu akafa, zonse zomwe ‘amaganiza zimatheratu.’ (Salimo 146:4) Choncho munthu akamwalira, ubongo wake sugwira ntchito, sangathe kuganiza chilichonse ndipo thupi lake silingathenso kumva kalikonse.
Baibulo limafotokozanso zinthu zosangalatsa zomwe zidzachitike kutsogolo. Limanena kuti anthu omwe anamwalira adzaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo.—Hoseya 13:14; Yohane 11:11-14.
KODI MULUNGU ANALENGERANJI ANTHU?
Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi. (Genesis 1:27) Adamu, yemwe anayambirira kulengedwa, amatchulidwanso kuti “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Mulungu analenga anthu ndi cholinga choti akhale naye pa ubwenzi. Anafunanso kuti anthuwo abereke ana n’kumakhala mosangalala. Analenganso anthu kuti azimutumikira moti atawalenga anawapatsa mtima wofuna kudziwa zambiri zokhudza iyeyo. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyu 5:3.
Ndipotu Baibulo limanena kuti: “Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.” (Luka 11:28) Baibulo limatiphunzitsa kuti tiyandikire Mulungu kapena kuti kukhala naye pa ubwenzi komanso limatithandiza kudziwa zomwe tingachite kuti tizikhala osangalala panopo ndiponso kuti tidzapeze moyo wosatha m’tsogolo.
Baibulo Limatithandiza Kuti Timudziwe Bwino Mulungu
ANTHU mamiliyoni ambiri atafufuza maumboni a nkhani zomwe Baibulo limaphunzitsa, afika potsimikiza kuti si buku wamba. Aona kuti mfundo zake n’zothandizabe masiku ano ngakhale kuti linalembedwa kalekale. Atsimikiziranso kuti Baibulo linauziridwa ndi Mulungu ndiponso ndi njira imene Mulunguyo anasankha kuti tidziwe maganizo ake. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amafuna kuti timudziwe n’kukhala naye pa ubwenzi. Limanena kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.
Mukamawerenga Baibulo mwakhama mudzamvetsa zinthu zina zochititsa chidwi. Mwachitsanzo, mukamawerenga buku linalake mumatha kudziwa mmene munthu amene analemba bukulo amaganizira. Zimenezi ndi zimene zimachitikanso mukamawerenga Baibulo. Mumatha kumvetsa maganizo a Mulungu. Ndiye tangoganizirani mmene mungasangalalire mutakhala kuti mukudziwa maganizo a Mulungu. M’Baibulo mungapezemonso zinthu ngati izi:
-
Dzina la Mulungu komanso makhalidwe ake.
-
Chifukwa chake Mulungu analenga anthu.
-
Zimene mungachite kuti mukhale pa ubwenzi ndi Mulungu.
Kodi mukufuna mutamvetsa mfundo zimenezi komanso nkhani zina? A Mboni za Yehova akhoza kukuthandizani. Angathe kumaphunzira nanu Baibulo kwaulere ndipo zimenezi zingakuthandizeni kuti mukhale pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova Mulungu amene ndi mwiniwake wa Baibulo.
M’nkhanizi taona maumboni osonyeza kuti Baibulo ndi louziridwadi ndi Mulungu. Kuti mudziwe zambiri zokhudza Baibulo, werengani mutu 2 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bukuli ndi lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo mungalipeze pawebusaiti ya www.pr418.com/ny kapena mukachita sikani kachidindo aka
Mungaonerenso vidiyo yakuti Kodi Analemba Baibulo Ndi Ndani?, pawebusaiti ya www.pr418.com/ny
Onani pomwe alemba kuti MABUKU > MAVIDIYO
^ ndime 10 M’Baibulo, Mulungu amadziwika ndi dzina lakuti Yehova.—Salimo 83:18.