Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Angelo

Angelo

Angelo amaonetsedwa m’mafilimu ndipo zithunzi zawo zimapezekanso m’mabuku ndi m’zinthu zina zopangidwa mwaluso. Koma kodi angelo ndi ndani, nanga amagwira ntchito yotani?

Kodi angelo ndi ndani?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

 

Mulungu asanalenge dziko lapansili ndi anthu, anali atalenga kale zolengedwa zina zanzeru kwambiri kuposa anthu. Zolengedwazi ndi zamphamvunso kwambiri kuposa anthu ndipo zimakhala kumwamba kumene kuli Mulungu. Anthufe sitingathe kuona zolengedwazi ndipo sitingafike kumene zimakhala. (Yobu 38:4, 7) Baibulo limazitchula kuti “mizimu” kapena angelo.​—Salimo 104:4. *

Kodi angelo alipo angati? Alipo ochuluka kwambiri. Angelo omwe ali kumpando wachifumu wa Mulungu alipo “10,000 kuchulukitsa ndi ma 10,000” kapena kuti “masauzande kuchulukitsa ndi masauzande.” (Chivumbulutso 5:11; mawu am’munsi) Zimenezi zikungosonyeza kuti angelowa alipo mamiliyoni mahandiredi ambiri.

“Ndinaona . . . angelo ambiri atazungulira mpando wachifumu. . . . Chiwerengero chawo chinali miyanda kuchulukitsa ndi miyanda ndiponso masauzande kuchulukitsa ndi masauzande.”—Chivumbulutso 5:11.

Kodi angelo ankagwira ntchito yotani kalelo?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

 

Nthawi zambiri angelo ankagwira ntchito ngati olankhula m’malo mwa Mulungu kapena opereka uthenga wochokera kwa Mulungu. * Baibulo limasonyezanso kuti angelo ankachita zozizwitsa pogwiritsa ntchito mphamvu za Mulungu. Mwachitsanzo, nthawi ina Mulungu anatumiza mngelo kuti akadalitse Abulahamu komanso kukamuletsa kuti asapereke mwana wake Isaki nsembe. (Genesis 22:11-18) Nthawi inanso mngelo anaonekera kwa Mose pakati pa chitsamba choyaka moto kukamuuza uthenga wa zimene Mulungu ankafuna kuti Moseyo achite. (Ekisodo 3:1, 2) Komanso nthawi ina, mneneri Danieli ataponyedwa m’dzenje la mikango, ‘Mulungu anatumiza mngelo wake kukatseka pakamwa pa mikango.’​—Danieli 6:22.

“Kenako mngelo wa Yehova anaonekera kwa [Mose] pakati pa chitsamba chaminga.”—Ekisodo 3:2.

Kodi angelo amachita chiyani masiku ano?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

 

Sitingathe kudziwa zonse zomwe angelo akuchita panopo. Komabe Baibulo limasonyeza kuti angelo akuthandiza anthu a mtima wabwino kuti adziwe zambiri zokhudza Mulungu.​—Machitidwe 8:26-35; 10:1-22; Chivumbulutso 14:6, 7.

Nthawi ina Yehova anachititsa Yakobo kulota maloto. M’malotowo Yakobo anaona angelo akukwera komanso kutsika “pamakwerero” ochokera padzikoli n’kufika kumwamba. (Genesis 28:10-12) N’kutheka kuti Yakobo atalota malotowo, anadziwa kuti Yehova Mulungu amatumiza angelo padziko lapansi kudzathandiza anthu ake okhulupirika pa nthawi imene akufunika thandizo.​—Genesis 24:40; Ekisodo 14:19; Salimo 34:7.

“Anaona makwerero ochokera pansi mpaka kumwamba. Angelo a Mulungu anali kukwera ndi kutsika pamakwereropo.”​—Genesis 28:12.

^ ndime 6 Baibulo limanena kuti zolengedwa zina zauzimu zinapandukira ulamuliro wa Mulungu. Zolengedwazi zimadziwika kuti “ziwanda.”​—Luka 10:17-20.

^ ndime 11 Mawu oyambirira Achiheberi komanso Achigiriki omwe Baibulo linagwiritsa ntchito ponena za “mngelo,” amatanthauza “wopereka uthenga.”