Mtendere wa M’maganizo
Baibulo limatilangiza kuti tizipewa makhalidwe omwe angativulaze monga kupsa mtima. Limatilimbikitsanso kuti tizikhala ndi makhalidwe abwino.
KUPSA MTIMA
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu.”—Miyambo 16:32.
ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Timapindula kwambiri tikamayesetsa kuugwira mtima. N’zoona kuti nthawi zina tonsefe tikhoza kukwiya pazifukwa zomveka, koma kulekerera mkwiyo kwa nthawi yaitali kungatibweretsere mavuto aakulu. Ochita kafukufuku a masiku ano amanena kuti munthu amene amalephera kuugwira mtima amatha kulankhula kapena kuchita zinthu zimene pambuyo pake amanong’oneza nazo bondo.
ZIMENE MUNGACHITE: Musamalole kuti mkwiyo uzikulamulirani. Ena amaganiza kuti anthu amene sachedwa kupsa mtima ndi amphamvu, koma kunena zoona anthu amenewa ndi ofooka. Tikutero chifukwa Baibulo limati: “Munthu wosaugwira mtima ali ngati mzinda umene mpanda wake wagumulidwa, n’kuusiya wopanda mpanda.” (Miyambo 25:28) Chimene chingakuthandizeni kuti muziugwira mtima ndi kumvetsa kaye nkhani yonse musanachitepo kanthu. Pa nkhani imeneyi Baibulo limati: “Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake.” (Miyambo 19:11) Tingachite bwino kumvetsa mbali zonse za nkhaniyo zomwe zingatithandize kubweza mkwiyo wathu.
KUYAMIKIRA
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.”—Akolose 3:15.
ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Anthu amanena kuti munthu amene amakonda kuyamikira ena ndi amene amakhala wosangalala. Ngakhale anthu amene m’bale wawo wamwalira kapena zinthu zawo
zonse zawonongeka, amavomereza mfundo imeneyi. Anthuwa amanena kuti chimene chimawathandiza kupirira ndi kuyamikira zinthu zabwino zimene ali nazo m’malo momangoganizira zomwe zawachitikira.ZIMENE MUNGACHITE: Tsiku lililonse muzilemba kapena kuganizira zinthu zabwino zimene zakuchitikirani. Ndipo sizifunikira kuti zichite kukhala zinthu zikuluzikulu. Zikhoza kukhala zinthu zazing’ono ngati kutuluka kwa dzuwa, mmene mwachezera ndi munthu wina kapena chifukwa choti mwadzukanso ndi moyo. Zinthu zimenezi zingakuthandizeni kukhala wosangalala ngati mutamaziganizira komanso kuziyamikira.
Zimakhalanso zothandiza kwambiri mukamaganizira komanso kuyamikira kuti muli ndi banja komanso anzanu abwino. Anthu ena akachita zabwino kapena akasonyeza khalidwe linalake limene lakuchititsani chidwi, mungachite bwino kuwauza mmene mukumvera kaya powalembera kalata, imelo kapena meseji. Zimenezi zingathandize kuti muzigwirizana nawo kwambiri ndipo inuyo mungamasangalale chifukwa chokhala wopatsa.—Machitidwe 20:35.
MFUNDO ZINA ZA M’BAIBULO
MKANGANO UKABUKA MUZICHOKAPO.
“Chiyambi cha mkangano chili ngati kuboola damu kuti madzi atulukemo. Choncho mkangano usanabuke, chokapo.”—MIYAMBO 17:14.
MUSAMANGOKHALIRA KUDERA NKHAWA ZAM’TSOGOLO.
“Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.”—MATEYU 6:34.
MUZIGANIZA KAYE M’MALO MONGOCHITA ZINTHU CHIFUKWA CHA MMENE MUKUMVERA.
“Kuganiza bwino kudzakuyang’anira, ndipo kuzindikira kudzakuteteza.”—MIYAMBO 2:11.