“Mfundozi Zindithandiza Kwambiri”
MPHUNZITSI wa pa sukulu ina yasekondale ku South Korea dzina lake Soo-jeong, amagwiritsa ntchito mavidiyo apawebusaiti ya jw.org pophunzitsa. Iye ananena kuti: “Ana a m’kalasi mwanga amasangalala kwambiri akaonera vidiyo yakuti, Kodi Mnzako Weniweni Ungamudziwe Bwanji? Ana ambiri akamaliza kuonera amanena kuti, ‘Sindinaganizirepo mfundo zimenezi ndikamasankha anzanga. Mfundozi zindithandiza kwambiri.’ Ana ena ananena kuti azipita pawebusaitiyi akafuna malangizo pa nkhani zosiyanasiyana.” Soo-jeong ananenanso kuti: “Ndinauzanso aphunzitsi ena za vidiyoyi ndipo akusangalala chifukwa imawathandiza kwambiri akamaphunzitsa.”
Vidiyo inanso imene ana a sukulu ambiri ku South Korea amaona kuti ndi yothandiza ndi yakuti, Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani? Munthu wina wa m’bungwe lothandiza kupewa zachiwawa pakati pa ana anaonetsapo vidiyoyi kwa ana ena a sukulu. Iye ananena kuti: “Ana ambiri amaikonda vidiyoyi chifukwa cha zithunzi zake zosangalatsa. Imathandizanso ana kudziwa zimene angachite akamavutitsidwa ndiponso mmene angapewere kuvutitsidwa.” Bungweli linapempha chilolezo kuti lizionetsa vidiyoyi kwa ana a m’masukulu osiyanasiyana apulayimale ndipo linaloledwa. Nawonso apolisi akumagwiritsa ntchito mavidiyo apawebusaiti ya jw.org.
Tikukulimbikitsani kuti mupite pawebusaitiyi. Ndi yosavuta kugwiritsa ntchito ndipo mungapange dawunilodi zinthu zongomvetsera, mavidiyo, Mabaibulo ndiponso mabuku ena popanda kulipira chilichonse.