ZOCHITIKA PADZIKOLI
Nkhani za ku North ndi South America
Nkhani za kumayiko a ku North ndi South America zikusonyeza kuti mfundo za m’Baibulo n’zolondola komanso zothandiza.
Mungachepetse Nkhawa Mukasiya Kumaona Maimelo Pafupipafupi
Pa kafukufuku wina yemwe anachitika mumzinda wa Vancouver, ku Canada, anapeza kuti anthu amene amaona maimelo katatu kokha patsiku sakhala ndi nkhawa kwambiri poyerekezera ndi anthu omwe amaona maimelo atsopano pafupipafupi. Munthu yemwe ankatsogolera pa kafukufukuyu, dzina lake Kostadin Kushlev, ananena kuti: “Zimavuta kuti anthu asiye kumaona maimelo pafupipafupi koma zingawathandize kuti achepetseko nkhawa.”
ZOTI MUGANIZIRE: Popeza tikukhala mu ‘nthawi yovuta,’ ndi bwino kuti tiziyesetsa kuchepetsa nkhawa.—2 Timoteyo 3:1.
Nsomba Zayambanso Kuchuluka
Bungwe lina loteteza nyama zakutchire linanena kuti: “Zikuoneka kuti nsomba komanso zamoyo zina zayamba kuchuluka m’madera amene boma likuletsa kuti anthu asamaphe nsomba” ku Belize ndi m’madera ena a ku Caribbean. Bungweli linanenanso kuti: “Pangatenge zaka zochepa kuti nsomba komanso zamoyo zina ziyambenso kuchuluka m’madera amene amaletsa kupha nsomba kusiyana ndi m’madera amene saletsa. Komabe pangatenge zaka zambiri . . . kuti nsombazi zichuluke ngati mmene zinalili poyamba.” Mtsogoleri wina wa m’bungweli dzina lake Janet Gibson ananena zokhudza dziko la Belize kuti: “Zikuoneka kuti kuletsa anthu kuti asamaphe nsomba m’madera ena kukhoza kuthandiza kuti nsomba komanso zamoyo zina ziyambenso kuchuluka m’maderawo.”
ZOTI MUGANIZIRE: Kodi mfundo yakuti zinthu zachilengedwe zikhoza kubwereranso mmene zinalili poyamba sikusonyeza kuti pali wina wanzeru amene anazilenga?—Salimo 104:24, 25.
Zachiwawa KU Brazil
Bungwe la boma lofalitsa nkhani ku Brazil linanena kuti zachiwawa zikuchuluka kwambiri m’dzikolo. Mwachitsanzo, mu 2012, unduna wa zaumoyo unapeza kuti anthu oposa 56,000 anaphedwa ndi anthu anzawo. Chiwerengerochi ndi chokwera kwambiri poyerekezera ndi cha zaka zam’mbuyo. Munthu wina woona za chitetezo m’dzikoli ananena kuti kuchuluka kwa anthu ophedwawa kukusonyeza kuti makhalidwe a anthu afika poipa kwambiri. Iye ananenanso kuti anthu akangosiya kulemekeza malamulo a dziko “amayamba kuchita zachiwawa nthawi iliyonse imene akufuna zinazake.”
KODI MUKUDZIWA? Baibulo linaneneratu kuti idzafika nthawi pamene anthu ambiri adzasiya kumvera malamulo komanso kuti chikondi cha anthu ambiri “chidzazirala.”—Mateyu 24:3, 12.