Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI TINGAPEWE BWANJI MATENDA?

Dzitetezeni ku Matenda

Dzitetezeni ku Matenda

MIZINDA yambiri yakale inkazunguliridwa ndi mpanda kuti ikhale yotetezeka. Ngati adani awononga mbali ina ya mpandawo ndiye kuti mzinda wonse unkakhala wosatetezeka. Thupi lanu lili ngati mzinda wokhala ndi mpanda. Kuti mukhale wathanzi, muyenera kusamalira kwambiri chitetezo cha thupi lanu. Tiyeni tione zinthu 5 zimene zikhoza kubweretsa matenda komanso mmene mungadzitetezere.

1 MADZI

VUTO: Tizilombo toyambitsa matenda tikhoza kulowa m’thupi lanu ngati mutamwa madzi oipa.

MMENE MUNGADZITETEZERE: Njira yabwino yodzitetezera ndi kusamalira malo amene mumatungapo madzi. Ngati mwakayikira kuti madzi anu aipitsidwa, pali zinthu zimene mungachite musanayambe kuwagwiritsa ntchito. * Muzivindikira madzi anu akumwa ndipo muzitunga ndi chinthu choyera kapena muziwasunga m’chinthu chokhala ndi mpope n’kumagwiritsa ntchito mpopewo. Musamapisilire madzi abwinobwino oti mugwiritsanso ntchito. Ngati zingatheke, muyenera kukhala m’dera limene anthu ake ali ndi zimbudzi kuwopera kuti madzi angaipitsidwe ndi zonyansa.

2 CHAKUDYA

VUTO: Tizilombo toyambitsa matenda tikhoza kupezeka m’chakudya chathu.

MMENE MUNGADZITETEZERE: Chakudya chomwe chingakudwalitseni chikhoza kumaoneka ngati chabwinobwino. Choncho nthawi zonse muyenera kutsuka zipatso ndiponso ndiwo zamasamba. Mukamakonza chakudya, muzionetsetsa kuti zinthu monga ziwiya zakukhitchini, malo ophikira ndiponso manja anu ndi zoyera. Chakudya china chimafunika kuphikidwa mokwanira kuti tizilombo toyambitsa matenda tife. Muyenera kusamala ndi chakudya chimene chayamba kusintha mtundu, kakomedwe kake kapena chimene chayamba kununkha. Zimenezi zingakhale zizindikiro zoti m’chakudyacho muli tizilombo toyambitsa matenda. Chakudya chimene chatsala, muyenera kuchisunga mwamsanga m’firiji. Ndipo ngati mukudwala, simuyenera kukonzera anthu ena chakudya. *

3 TIZILOMBO TOULUKA

VUTO: Tizilombo tina touluka timakhala ndi majeremusi moti tikhoza kukudwalitsani.

MMENE MUNGADZITETEZERE: Kuti mudziteteze ku tizilomboti, muyenera kukhala m’nyumba nthawi imene tizilomboti timauluka kwambiri kapena kuvala zovala zazitali manja kapena thalauza. Muzigona m’masikito onyikidwa m’mankhwala ndiponso kudzola mafuta othamangitsa tizilombo. Muzionetsetsa kuti pafupi ndi nyumba yanu palibe madzi oti samayenda chifukwa m’pamene udzudzu ungaswanirane. *

4 ZIWETO KOMANSO NYAMA ZINA

VUTO: Nyama zina zimakhala ndi tizilombo m’thupi mwawo tomwe si toopsa kwa nyamazo koma tikhoza kukhala toopsa kwa ifeyo. Ngati mwalumidwa kapena kukandidwa ndi nyama iliyonse kapena kukhudza ndowe zake, mukhoza kudwala.

MMENE MUNGADZITETEZERE: Anthu ena salola kuti ziweto zizilowa m’nyumba poopa kuti zikhoza kuwapatsira matenda. Muzisamba m’manja mukagwira chiweto ndipo muzipewa kugwira kapena kukhudzana ndi nyama zakutchire. Ngati mwalumidwa kapena kukandidwa, muzitsuka bwinobwino balalo ndipo muzipita kuchipatala. *

5 ANTHU

VUTO: Majeremusi ena akhoza kulowa m’thupi mwanu ngati munthu wina atakutsokomolerani kapena kukuyetsemulirani. Anthu angapatsiranenso majeremusi pokumbatirana kapena kugwirana manja. Anthu akhoza kusiya majeremusi pazinthu zimene anthu amazigwiragwira monga handulo ya chitseko, telefoni kapena kompyuta.

MMENE MUNGADZITETEZERE: Musamabwerekane zinthu monga malezala, miswachi kapena zodzipukutira. Muzipewa kukhudza magazi, mamina kapena malovu a anthu ena ndiponso a nyama. Komanso musamaiwale kuti kusamba m’manja ndi sopo pafupipafupi kumathandiza kwambiri kupewa matenda.

Ngati mukudwala, ndi bwino kukhala pakhomo kuti musapatsire ena matendawo. Bungwe la ku United States loona za kupewa matenda linanena kuti ndi bwino kutsokomolera kapena kuyetsemulira pakansalu osati m’manja.

Baibulo limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Mawuwa ndi othandiza kwambiri masiku ano popeza kuti matenda oopsa ali paliponse. Choncho muyenera kutsatira malangizo amene azaumoyo angapereke ndiponso kuyesetsa kukhala aukhondo. Mukamachita zonse zimene mungathe kuti thupi lanu likhale ndi chitetezo champhamvu, mukhoza kupewa matenda ambiri.

^ ndime 6 Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse limavomereza njira zambiri zimene anthu paokha angatsatire posamalira madzi. Zina mwa njirazi ndi kuthira mankhwala opha majeremusi, kusefa ndiponso kuwiritsa madziwo.

^ ndime 9 Kuti mumve zambiri pa nkhani yosamala chakudya, onani Galamukani! ya June 2012, tsamba 3-9.

^ ndime 12 Kuti mumve malangizo ambiri opewera malungo, onani Galamukani! ya July 2015, tsamba 14 ndi 15.

^ ndime 15 Ndi bwino kupita kuchipatala mwamsanga ngati mwalumidwa ndi chinthu chapoizoni.