Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Ulusi wa Nkhono Yam’madzi

Ulusi wa Nkhono Yam’madzi

MOFANANA ndi tinyama tina tam’madzi, nkhono zinazake zam’madzi zimamatirira kumiyala, mitengo kapena sitima zam’madzi. Koma mosiyana ndi tinyama tina timene timamatirira thupi lonse kuchinachake, nkhonozi zimagwiritsa ntchito timaulusi tinatake tomwe timamata kuchinthucho. Izi zimathandiza kuti nkhonozi zizitha kusuntha komanso kupeza zakudya kwinaku zitamatirira kuchinachake. Komabe timaulusiti timaoneka ngati tosalimba moti munthu angaganize kuti tikhoza kuduka mosavuta ndi mafunde. Koma kodi timaulusi timeneti timathandiza bwanji kuti nkhonozi zimatirirebe kuchinachake osakokoloka ndi mafunde?

Taganizirani izi: Timaulusiti timakhala tolimba mbali imene imamata pachinthucho koma mbali imene kuli nkhonoyo imakhala yofewa komanso imatha kutanuka. Asayansi atulukira kuti chomwe chimathandiza kuti nkhonozi zimatirire kwambiri kuchinthu n’chakuti mbali yaikulu ya timaulusiti ndi yolimba pomwe mbali yochepa ndi yofewa. Chifukwa cha zimenezi, nkhonozi zimatha kumatirirabe bwinobwino pachinthu ngakhale zitamakankhidwa ndi mafunde amphamvu.

Pulofesa wina dzina lake Guy Genin ananena kuti zomwe asayansi anapezazi “n’zodabwitsa kwambiri.” Iye ananenanso kuti: “Chochititsa chidwi ndi nkhonozi ndi mmene mbali yofewa ya timaulusiti imalumikizirana ndi mbali yolimba.” Akatswiri a sayansi amakhulupirira kuti akhoza kupanga zinthu zambiri potengera mmene timaulusiti tinapangidwira. Mwachitsanzo, amanena kuti akhoza kupeza njira yosavuta yomatira zinthu pakhoma la nyumba komanso pasitima zam’madzi. Amanenanso kuti akhoza kupeza njira yabwino yolumikizira minyewa kumafupa komanso yotsekera mabala a opaleshoni. Pulofesa wina wa pa yunivesite ya California ku Santa Barbara m’dziko la United States, dzina lake J. Herbert Waite, ananena kuti: “Pali zambiri zomwe tingaphunzire m’chilengedwe pa nkhani ya luso lopanga zinthu zomatira.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti nkhonozi zizitulutsa timaulusiti kapena pali winawake amene anazilenga ndi luso limeneli?