Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Yesu ankasiyana bwanji ndi Arabi pochita zinthu ndi anthu akhate?

Kale Ayuda ankachita mantha kwambiri ndi matenda a khate omwe amatchulidwa m’Baibulo. Matendawa anali oopsa chifukwa ankagwira mitsempha yotumiza uthenga ku ubongo ndipo zinkachititsa kuti munthu alumale. Pa nthawiyi kunalibe mankhwala a khate. Ndipo odwala matendawa ankawaika kwaokha komanso ankayenera kuchenjeza ena za matenda awowo.Levitiko 13:45, 46.

Atsogoleri achiyuda anakhazikitsa malamulo okhwima komanso osagwirizana ndi zomwe Mawu a Mulungu ankanena zokhudza anthu akhate. Zimenezi zinkachititsa kuti anthuwa azivutika kwambiri. Mwachitsanzo, arabi anakhazikitsa malamulo akuti munthu aliyense akaona wakhate azitalikirana naye mamita awiri. Komanso ankanena kuti ngati kukuwomba mphepo, azitalikirana naye mamita 45. Buku la malamulo ndi miyambo ya Ayuda (Talmud), linati lamulo la m’Baibulo loti akhate “azikhala kunja kwa msasa,” linkatanthauza kuti sayenera kukhala mumzinda uliwonse wampanda. Arabi akaona wakhate ali mumzinda, ankamugenda n’kumuuza kuti: “Pita kumalo ako, usapatsire anthu ena matenda akowo!”

Komatu Yesu ankachita zinthu zosiyana kwambiri ndi atsogoleriwa. Iye sankathamangitsa akhate, koma ankafunitsitsa kuwakhudza ndiponso kuwachiritsa.Mateyu 8:3.

Kodi atsogoleri achipembedzo chachiyuda ankalola kuti mwamuna asiye mkazi wake pa zifukwa ziti?

Kalata yothetsera ukwati ya zaka za m’ma 71 kapena 72 C.E.

Kale atsogoleri achipembedzo chachiyuda ankasiyana maganizo pa nkhani ya zifukwa zomwe mwamuna angathetsere ukwati. Mwachitsanzo, nthawi ina Afarisi anafunsa Yesu kuti: “Kodi n’kololeka kuti mwamuna asiye mkazi wake pa chifukwa chilichonse?”Mateyu 19:3.

Chilamulo cha Mose chinkalola mwamuna kusiya mkazi wake ngati “wam’peza ndi vuto linalake.” (Deuteronomo 24:1) M’nthawi ya Yesu, kunali sukulu ziwiri zomwe ankaphunzitsirako arabi kapena kuti aphunzitsi achiyuda. Kusukuluzi ankaphunzitsa mfundo zosiyana zokhudza lamuloli. Mwachitsanzo, kusukulu ya Shammai ankaphunzitsa mfundo zokhwima ndipo ankati ukwati ukhoza kutha pokhapokha ngati wina wachita chigololo. Pomwe kusukulu ya Hillel ankaphunzitsa kuti mwamuna akhoza kusiya mkazi wake chifukwa cha vuto lina lililonse la m’banja ngakhale laling’ono. Mwachitsanzo, ankaphunzitsa kuti mwamuna akhoza kuthetsa ukwati ngati mkazi wake sanaphike bwino chakudya kapenanso akaona mkazi wina wokongola.

Kodi Yesu anayankha bwanji funso la Afarisi? Iye ananena mosabisa mawu kuti: “Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.”Mateyu 19:6, 9.