Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | BAIBULO—BUKU LOMWE LINAPULUMUKA M’ZAMBIRI

N’chifukwa Chiyani Baibulo Linapulumuka

N’chifukwa Chiyani Baibulo Linapulumuka

Masiku ano mukhoza kupeza ndiponso kuwerenga Baibulo mosavuta. Ndipo ngati mwasankha Baibulo lomwe linamasuliridwa molondola, m’posavuta kutsimikizira kuti uthenga wake ndi wochokeradi m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo. * M’nkhani zapitazi taona kuti Baibulo linapulumuka ngakhale kuti likanatha kuwola, anthu ena ankalitsutsa, komanso ankafuna kusintha uthenga wake. Koma n’chifukwa chiyani linapulumuka modabwitsa chonchi?

“Panopa sindikukayika ngakhale pang’ono kuti Baibulo lomwe ndili nalo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu”

Anthu ambiri amene akuphunzira Baibulo amavomereza zomwe mtumwi Paulo analemba kuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Anthuwa amakhulupirira kuti Baibulo linapulumuka chifukwa chakuti ndi Mawu a Mulungu komanso Iye analiteteza. Faizal yemwe watchulidwa m’nkhani yoyambirira, anaganiza zoyamba kuphunzira Baibulo pofuna kutsimikizira zimenezi. Iye anadabwa ataona kuti zinthu zambiri zimene anthu amaphunzitsa m’matchalitchi awo sizichokera m’Baibulo. Faizal anachita chidwi kwambiri ataphunzira cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansi kuchokera m’Baibulo.

Iye ananena kuti: “Panopa sindikukayika ngakhale pang’ono kuti Baibulo lomwe ndili nalo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Komanso ngati Mulungu yemwe ndi Wamphamvuyonse anakwanitsa kulenga chilengedwechi, kodi angalephere kutipatsa buku ndi kuliteteza kuti tiziliwerenga? Munthu yemwe angatsutse zimenezi ndiye kuti akuderera mphamvu za Mulungu, yemwe ndi Wamphamvuyonse, nanga ine ndani kuti ndichite zimenezi?”Yesaya 40:8.

^ ndime 3 Onani nkhani yakuti, “Kodi Mungadziwe Bwanji Baibulo Lomasuliridwa Bwino?” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2008.