Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 17

NYIMBO NA. 111 Tili Ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala

Musachoke M’Paradaiso Wauzimu

Musachoke M’Paradaiso Wauzimu

“Kondwerani ndipo muzisangalala mpaka kalekale ndi zimene ndikulenga.”​—YES. 65:18.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiphunzira mmene timapindulira chifukwa chokhala m’paradaiso wauzimu komanso zimene tingachite pothandiza ena kuti alowe m’paradaisoyu.

1. Kodi paradaiso wauzimu n’chiyani, nanga tiyenera kukhala otsimikiza kuchita chiyani?

 MASIKU ano padzikoli pali paradaiso yemwe muli anthu ambiri omwe atanganidwa ndi kuchita zinthu zabwino. M’paradaisoyu muli anthu mamiliyoni ambiri omwe ali pamtendere weniweni. Anthu amene ali m’paradaisoyu safuna kuchokamo. Iwo akufuna kuti anthu enanso ambiri alowemo. Ameneyutu ndi paradaiso wauzimu. a

2. Kodi chochititsa chidwi ndi paradaiso wauzimu n’chiyani?

2 N’zochititsa chidwi kuti Yehova wakonza paradaiso wabata ameneyu m’dziko limene Satana wachititsa kuti pakhale chidani komanso muli anthu oipa ndi oopsa. (1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:12) Mulungu wathu wachikondi amadziwa mavuto omwe ali m’dzikoli ndipo amatiteteza kuti tipitirize kumutumikira mosangalala. Mawu ake amafotokoza kuti paradaiso wauzimuyu ndi “malo othawirako” otetezeka komanso ali ngati “dimba lothiriridwa bwino.” (Yes. 4:6; 58:11) Mothandizidwa ndi Yehova, anthu omwe ali m’paradaisoyu amakhala osangalala komanso amadzimva kuti ndi otetezeka m’masiku otsiriza ovutawa.​—Yes. 54:14; 2 Tim. 3:1.

3. Kodi lemba la Yesaya 65 linakwaniritsidwa bwanji m’nthawi ya Aisiraeli?

3 Yehova anafotokoza kudzera mwa mneneri Yesaya mmene moyo wa anthu omwe adzakhale m’paradaisoyu udzakhalire. Muchaputala 65 cha buku la Yesaya mungapezemo zimene anafotokoza zokhudza paradaisoyu, zomwe zinakwaniritsidwa koyamba mu 537 B.C.E. Pa nthawiyo, Ayuda omwe analapa anamasulidwa ku ukapolo ku Babulo ndipo anabwerera kwawo. Yehova anadalitsa anthu ake ndipo anawathandiza kukonzanso mzinda wa Yerusalemu kuti ukhalenso wokongola komanso kuti amangenso kachisi yemwe anali likulu la kulambira koona.​—Yes. 51:11; Zek. 8:3.

4. Kodi lemba la Yesaya 65 likukwaniritsidwa bwanji masiku ano?

4 Kukwaniritsidwa kwachiwiri kwa ulosi wa Yesayawu kunayamba mu 1919 pamene atumiki a Yehova a masiku ano anamasulidwa ku ukapolo wa Babulo Wamkulu. Kenako paradaiso wauzimu anayamba kufalikira padziko lonse. Olalikira Ufumu akhama anakhazikitsa mipingo yambiri ndipo ankasonyeza makhalidwe abwino. Amuna ndi akazi omwe poyamba anali achiwawa komanso ankasonyeza makhalidwe ngati a zinyama, anayamba ‘kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.’ (Aef. 4:24) N’zoona kuti madalitso ambiri omwe Yesaya anafotokoza adzakwaniritsidwa m’tsogolo m’dziko latsopano. Komabe panopa pali madalitso ambiri omwe timapeza. Tiyeni tione mmene timapindulira chifukwa chokhala m’paradaiso wauzimu komanso chifukwa chake sitiyenera kuchokamo.

MMENE ZINTHU ZILILI M’PARADAISO WAUZIMU

5. Mogwirizana ndi lonjezo la pa Yesaya 65:13, kodi ndi zinthu ziti zimene timasangalala nazo m’paradaiso wauzimu?

5 Anthu ndi athanzi komanso amatsitsimulidwa. Ulosi wa Yesaya umasonyeza kuti pali kusiyana kwambiri pakati pa anthu omwe ali m’paradaiso wauzimu ndi amene sali m’paradaisoyu. (Werengani Yesaya 65:13.) Yehova amapereka mowolowa manja kwa atumiki ake zonse zomwe amafunikira kuti apitirize kukhala naye pa ubwenzi. Amatipatsa mzimu woyera, Mawu ake komanso chakudya chauzimu chochuluka n’cholinga choti ‘tizidya, . . . tizimwa, . . . [komanso] tizisangalala.’ (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 22:17.) Koma anthu omwe amakhala kunja kwa paradaisoyu ‘amakhala ndi njala . . . , amakhala ndi ludzu . . . , [komanso] amachita manyazi.’ Iwo sapeza zinthu zimene zingawathandize kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.​—Amosi 8:11.

6. Kodi lemba la Yoweli 2:21-24 limatchula zinthu ziti zomwe Yehova watipatsa, nanga zimatipindulitsa bwanji?

6 Mu ulosi wake, Yoweli anagwiritsa ntchito zinthu zofunika pa moyo monga tirigu, vinyo komanso mafuta a maolivi pofuna kusonyeza kuti Yehova amapereka mowolowa manja kwa anthu ake zinthu zimene amafunikira, kuphatikizapo chakudya chauzimu. (Yow. 2:21-24) Iye amachita zimenezi kudzera m’Baibulo, mabuku ofotokoza Baibulo, webusaiti yathu, misonkhano yampingo, yadera komanso yachigawo. Tingathe kudya chakudya chauzimuchi tsiku lililonse ndipo zotsatira zake n’zakuti timakhala athanzi komanso timatsitsimulidwa.

7. Kodi n’chiyani chomwe chimachititsa kuti tikhale ndi “chimwemwe mumtima”? (Yesaya 65:14)

7 Anthu amasangalala komanso amakhala okhutira. Anthu a Mulungu ‘amafuula mosangalala’ chifukwa choyamikira zimene Yehova wawachitira. (Werengani Yesaya 65:14.) Timakhala ndi “chimwemwe mumtima” chifukwa cha mfundo zolimbitsa chikhulupiriro, malonjezo opezeka m’Mawu a Mulungu komanso chiyembekezo chomwe chimatheka chifukwa cha nsembe ya dipo ya Khristu. Timasangalala kwambiri tikamakambirana zimenezi ndi abale ndi alongo athu.​—Sal. 34:8; 133:1-3.

8. Kodi ndi makhalidwe ofunika awiri ati omwe amapezeka m’paradaiso wauzimu?

8 Chikondi komanso mgwirizano pakati pa anthu a Yehova ndi makhalidwe akuluakulu amene amapezeka m’paradaiso wauzimu. Mgwirizano umenewu umasonyeza mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano, pamene atumiki a Yehova azidzakondana kwambiri komanso kugwirizana kuposa panopa. (Akol. 3:14) Mlongo wina anafotokoza zimene anaona atakumana koyamba ndi anthu a Yehova. Iye anati: “Ndinali ndisanakhalepo wosangalala ngakhale m’banja langa. Nthawi imene ndinaona anthu akusonyezana chikondi chenicheni ndi pamene ndinakumana ndi a Mboni za Yehova.” Aliyense amene akufuna kukhala wosangalala komanso wokhutira ayenera kulowa m’paradaiso wauzimu. Kaya anthu amaganiza zotani zokhudza atumiki a Yehova, iwo ali ndi mbiri yabwino kwa Yehovayo komanso onse amene amamulambira.​—Yes. 65:15.

9. Kodi lemba la Yesaya 65:16, 17 limalonjeza chiyani za mavuto amene timakumana nawo?

9 Anthu ake amakhala osatekeseka komanso odekha. Lemba la Yesaya 65:14 limanena kuti amene amasankha kukhala kunja kwa paradaiso wauzimu, ‘amalira chifukwa chopwetekedwa mtima ndipo amalira mofuula chifukwa chosweka mtima.’ Koma bwanji za zinthu zonse zomwe zimachititsa anthu a Mulungu kuti azimva kupweteka komanso azivutika? Posachedwapa zimenezi ‘zidzaiwalika ndipo zidzabisidwa kuti [Mulungu] asazionenso.’ (Werengani Yesaya 65:16, 17.) Yehova adzachotsa mavuto onse ndipo pakapita nthawi sitidzakumbukiranso ululu wonse womwe tinkamva chifukwa cha mavutowo.

10. N’chifukwa chiyani timayamikira kukhala ndi abale ndi alongo athu? (Onaninso chithunzi.)

10 Ngakhale panopa mitima yathu imakhala m’malo tikapezeka kumisonkhano komwe timakaiwala mavuto omwe tikukumana nawo m’dziko loipali. Timathandiza kuti onse mumpingo azikhala osatekeseka tikamasonyeza makhalidwe monga chikondi, chimwemwe, mtendere, kukoma mtima komanso kufatsa, amene ndi makhalidwe omwe timakhala nawo mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu. (Agal. 5:22, 23) Ndi mwayitu waukulu kukhala m’gulu la Mulungu. Anthu onse amene akupitiriza kukhala m’paradaiso wauzimu adzaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu lokhudza “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.”

Ndi mwayi waukulu kukhala m’banja la Mulungu m’paradaiso wauzimu (Onani ndime 10) c


11. Mogwirizana ndi Yesaya 65:18, 19, kodi timamva bwanji tikaganizira za paradaiso wauzimu amene Yehova anatikonzera?

11 Anthu ake amakhala oyamikira. Yesaya anapitiriza kufotokoza chifukwa chake tiyenera ‘kukondwera ndiponso kusangalala’ m’paradaiso wauzimu. Yehova ndi amene wakonza paradaisoyu. (Werengani Yesaya 65:18, 19.) N’chifukwa chake akutigwiritsa ntchito kuti tithandize anthu kuti atuluke m’mabungwe a m’dzikoli omwe sakuthandiza anthu kuti akhale pa ubwenzi ndi iye, n’kulowa m’paradaiso wauzimu wokongolayu. Timasangalala chifukwa cha madalitso amene timapeza chifukwa chokhala m’choonadi ndipo izi zimatilimbikitsa kuti tiziuza ena zokhudza madalitsowa.​—Yer. 31:12.

12. Kodi timamva bwanji chifukwa cha lonjezo la pa Yesaya 65:20-24, nanga n’chifukwa chiyani?

12 Timayamikiranso chiyembekezo chimene tili nacho chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo timakhala osangalala. Tangoganizani zimene tidzaone komanso kuchita m’dziko latsopano la Mulungu. Baibulo limalonjeza kuti: “Sikudzakhalanso mwana wakhanda amene adzangokhala ndi moyo masiku ochepa okha, kapena munthu wachikulire amene sadzakwanitsa zaka zimene munthu amafunika kukhala ndi moyo.” ‘Tidzamanga nyumba nʼkumakhalamo, ndipo tidzadzala minda ya mpesa nʼkudya zipatso zake.’ Anthu “sadzagwira ntchito mwakhama pachabe” chifukwa ‘adzadalitsidwa ndi Yehova.’ Iye akutilonjeza kuti tidzakhala ndi moyo wabwino ndiponso otetezeka. ‘Asanamuitane,’ Mulungu adzadziwa zimene aliyense akufunikira ndipo ‘adzakwaniritsa zolakalaka za chamoyo chilichonse.’​—Yes. 65:20-24; Sal. 145:16.

13. Kodi lemba la Yesaya 65:25 limafotokoza kuti anthu amasintha bwanji akayamba kutumikira Yehova?

13 Anthu amakhala mwamtendere komanso otetezeka. Mzimu wa Mulungu wathandiza anthu ambiri omwe poyamba anali ndi makhalidwe ngati a zinyama kuti asinthe. (Werengani Yesaya 65:25.) Iwo anayesetsa kusiya makhalidwe oipa omwe anali nawo kale. (Aroma 12:2; Aef. 4:22-24) Komabe anthu a Mulungu si angwiro, choncho amalakwitsabe zinthu zina. Ngakhale zili choncho, Yehova akuthandiza “anthu a mitundu yonse” kuti akhale ogwirizana ndipo zotsatira zake n’zakuti amakondana komanso ali pamtendere. (Tito 2:11) Izi ndi zodabwitsa zimene Mulungu yekha, yemwe ndi wamphamvu zonse, angakwanitse kuchita.

14. Kodi zimene zinachitikira m’bale wina zinakwaniritsa bwanji lemba la Yesaya 65:25?

14 Kodi anthu angathedi kusintha makhalidwe? Taganizirani chitsanzo ichi. Wachinyamata wina pamene ankakwanitsa zaka 20 anali atamangidwapo maulendo angapo ndipo ankachita zachiwawa komanso makhalidwe ena oipa. Anali atamangidwapo chifukwa choba galimoto, kuthyola nyumba za anthu komanso kupalamula milandu ina ikuluikulu. Sankachedwanso kuyambitsa ndewu. Atamva kwa nthawi yoyamba zokhudza choonadi cha m’Baibulo, anayamba kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova. Anatsimikiza kuti wapeza chifukwa chokhalira ndi moyo, chomwe ndi kulambira Yehova m’paradaiso wake wauzimu. Atabatizidwa n’kukhala wa Mboni, nthawi zambiri ankaganizira mmene lemba la Yesaya 65:25 limamukhudzira. Iye anasintha n’kuchoka pokhala wachiwawa ngati mkango n’kufika pokhala munthu wokonda mtendere ngati kamwana ka nkhosa.

15. N’chifukwa chiyani timafuna kuitana ena kuti alowe m’paradaiso wauzimu, nanga tingachite bwanji zimenezi?

15 Lemba la Yesaya 65:13 limayamba ndi mawu akuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti.” Vesi 25 limamaliza ndi mawu akuti “akutero Yehova.” Izi zikusonyeza kuti mawu ake amakwaniritsidwa nthawi zonse. (Yes. 55:10, 11) Panopa paradaiso wauzimu alipo kale. Yehova wakonza ubale wapadera kwambiri. Anthu ake amakhala mwamtendere komanso motetezeka ngakhale kuti ali m’dziko lodzadza ndi chiwawa. (Sal. 72:7) Pa chifukwa chimenechi, timafuna kuthandiza anthu ambiri mmene tingathere kuti alowe m’banja lauzimuli. Tingachite zimenezi pogwira ntchito yophunzitsa anthu.​—Mat. 28:19, 20.

ZIMENE TINGACHITE KUTI ENA ALOWE M’PARADAISO WAUZIMU

16. N’chiyani chingathandize anthu kuti alowe m’paradaiso wauzimu?

16 Aliyense wa ife ali ndi udindo wothandiza anthu kuti azikopeka ndi paradaiso wauzimu. Kuti tithe kuchita zimenezi, tiyenera kutsanzira Yehova. Iye sakakamiza anthu kuti alowe m’paradaisoyu, m’malomwake ‘amawakoka’ mwachikondi. (Yoh. 6:44; Yer. 31:3) Anthu a mitima yabwino omwe aphunzira za Yehova komanso makhalidwe ake abwino amayamba kukhala naye pa ubwenzi. Kodi tingatani kuti makhalidwe athu abwino azikopa ena kuti alowe m’paradaiso wauzimu?

17. Kodi tingathandize bwanji ena kuti azikopeka ndi paradaiso wauzimu?

17 Njira imodzi imene ingatithandize kuti tikope ena kuti alowe m’paradaiso wauzimu ndi kukonda komanso kukomera mtima Akhristu anzathu. Anthu atsopano akafika pamisonkhano ya mpingo timafuna kuti azimva ngati mmene anamvera osakhulupirira omwe ayenera kuti anafika pamisonkhano ku Korinto. Iwo anati: “Zoonadi Mulungu ali pakati panu.” (1 Akor. 14:24, 25; Zek. 8:23) Choncho tiyenera kupitiriza kutsatira malangizo akuti ‘tizikhala mwamtendere pakati pathu.’ ​—1 Ates. 5:13.

18. Kodi n’chiyani chingakope anthu kuti alowe m’gulu lathu?

18 Nthawi zonse tiziyesetsa kuona abale ndi alongo athu ngati mmene Yehova amawaonera. Tingachite zimenezi poona makhalidwe abwino amene ali nawo osati oipa, omwe pakapita nthawi amawasiya. Tingathetse kusamvana kulikonse mwachikondi ngati nthawi zonse ‘timakomerana mtima, kusonyezana chifundo chachikulu komanso kukhululukirana ndi mtima wonse.’ (Aef. 4:32) Ndiyeno anthu amene amafuna kuchitiridwa zimenezi adzakopeka n’kulowa m’paradaiso wauzimu. b

MUSACHOKE M’PARADAISO WAUZIMU

19. (a) Mogwirizana ndi bokosi lakuti “ Anachoka, Kenako Anabweranso,” kodi ena anena chiyani atabwereranso m’paradaiso wauzimu? (b) Kodi tiyenera kukhala otsimikiza mtima kuchita chiyani? (Onaninso chithunzi.)

19 Timayamikira kwambiri kukhala m’paradaiso wauzimu. Panopa paradaisoyu ndi wokongola kwambiri kuposa kale ndipo muli anthu ambiri amene akulambira Yehova. Tidzapitiriza kuyamikira Yehova mpaka kalekale chifukwa cha paradaiso amene watikonzerayu. Aliyense amene akufuna kukhala ndi moyo wabwino, kutsitsimulidwa, kukhala wosatekeseka ndiponso wotetezeka ayenera kulowa m’paradaisoyu ndipo sayenera kutulukamo. Komabe tiyenera kukhala osamala chifukwa Satana amafunitsitsa kutichotsamo. (1 Pet. 5:8; Chiv. 12:9) Tisalole kuti iye achite zimenezo. Tiyeni tizichita zonse zomwe tingathe kuti paradaiso wauzimuyu akhalebe woyera, wokongola komanso wamtendere.

Anthu omwe apitirize kukhala m’paradaiso wauzimu adzasangalalanso m’paradaiso akubwerayo (Onani ndime 19)


KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi paradaiso wauzimu n’chiyani?

  • Kodi timapeza madalitso otani m’paradaiso wauzimu?

  • Kodi tingathandize bwanji ena kuti alowe m’paradaisoyu?

NYIMBO NA. 144 Yang’ananibe Pamphoto

a TANTHAUZO LA MAWU ENA: Mawu akuti “paradaiso wauzimu” amanena za chitetezo chimene olambira Yehova amakhala nacho. M’paradaiso wauzimuyu timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso Akhristu anzathu.

b Onerani pa jw.org vidiyo yakuti Ali Kuti Pano? Alena Žitníková: Zomwe Ndinkalakalaka Zinakwaniritsidwa kuti muone madalitso omwe mlongo wina anapeza chifukwa chokhala m’paradaiso wauzimu.

c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pamene abale ndi alongo akucheza pamisonkhano, m’bale wina wakhala payekha.