MFUNDO ZAKALE KOMA ZOTHANDIZABE MASIKU ANO
Musamade Nkhawa
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Lekani kudera nkhawa moyo wanu.”—Mateyu 6:25.
Kodi mfundoyi imatanthauza chiyani? Yesu anayankhula mawuwa pa ulaliki wina womwe unachitikira paphiri. Buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo, linanena kuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “kudera nkhawa,” angatanthauze “zimene munthu amachita akamakumana ndi mavuto monga umphawi komanso njala.” Kuwonjezera pamenepa nthawi zambiri anthu amada nkhawa akaganizira zimene zidzawachitikire m’tsogolo. N’zoona kuti si kulakwa kumaganizira kwambiri za achibale athu ndiponso mmene tingapezere ndalama zogulira zinthu zofunika. (Afilipi 2:20) Komabe, Yesu ananena mawu akuti “lekani kudera nkhawa,” chifukwa sankafuna kuti otsatira ake azida nkhawa ndi zinthu zomwe sizinachitike n’komwe kuopera kuti angamakhale osasangalala.—Mateyu 6:31, 34.
Kodi mfundoyi ndi yothandiza masiku ano? Malangizowa ndi othandiza kwambiri ngakhale masiku ano. Tikunena zimenezi chifukwa mabuku ena amanena kuti munthu amene amangokhalira kuda nkhawa amadwaladwala. Amadwala matenda monga “zilonda za m’mimba, matenda a mtima komanso chifuwa cha mphumu [kapena kuti asima].”
Yesu anatchula chifukwa chimene chingatithandize kuti tisamade nkhawa. Anasonyeza kuti kuda nkhawa sikungatithandize chilichonse. Iye anafunsa kuti: “Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha mwa kuda nkhawa?” (Mateyu 6:27) Zimenezi n’zoona chifukwa zinthu zina zimene timada nazo nkhawa sizingachitike n’komwe. Katswiri wina wa maphunziro anati: “Kumangodera nkhawa zam’tsogolo n’kutaya nthawi. Mwina zimene tikudera nkhawazo sizichitika n’komwe.”
Kodi tingatani kuti tisamangokhalira kuda nkhawa? Choyamba, tiyenera kumadalira kwambiri Mulungu. Baibulo limanena kuti Mulungu amadyetsa mbalame komanso amaveka maluwa. Choncho sangalephere kuthandiza anthu amene amamulambira kuti azipeza zinthu zofunikira pa moyo. (Mateyu 6:25, 26, 28-30) Chachiwiri, ngati mwakumana ndi vuto linalake, musamakhale ndi nkhawa kuti vutolo lidzachitikanso mawa. Yesu anati: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.” Mwina nanunso mumavomereza mfundo yakuti, “zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.”—Mateyu 6:34.
Choncho taona kuti kutsatira malangizo a Yesu kungatithandize kuti tisamadwaledwale chifukwa cha nkhawa. Kuwonjezera pamenepa timakhala ndi mtendere wa mumtima womwe Baibulo limautchula kuti “mtendere wa Mulungu.”—Afilipi 4:6, 7.