Kodi Malangizo a M’Baibulo ndi Othandizabe Masiku Ano?
ENA ANGAYANKHE KUTI AYI. Mwachitsanzo, dokotala wina ananena kuti kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo kuli ngati kugwiritsa ntchito buku la sayansi la m’ma 1920 pophunzitsa anthu sayansi masiku ano. Komanso munthu amene sakhulupirira Baibulo angaone kuti kutsatira malangizo a m’Baibulo panopa n’kosathandiza. Angaone kuti kuchita zimenezi kuli ngati kugwiritsa ntchito buku la malangizo la kompyuta yakalekale, pofuna kudziwa mmene kompyuta yamakono imagwirira ntchito. Zimenezi zikusonyeza kuti anthu ena amaona kuti Baibulo ndi losathandiza chifukwa malangizo ake ndi achikale.
Koma kodi ndi nzeru kugwiritsa ntchito buku lakalekale ngati limeneli masiku ano pamene kuli zipangizo zambiri zamakono? Ndipotu masiku ano kuli mawebusaiti ambiri amene ali ndi malangizo atsopano othandiza anthu kudziwa zoyenera kuchita pa nkhani zosiyanasiyana. Komanso pali akatswiri ambiri amene amapereka malangizo okhudza zinthu zosiyanasiyana pa TV. Palinso mabuku ambiri amalangizo omwe munthu angathe kugula.
Popeza masiku ano pamapezeka malangizo oti angolembedwa tsiku lomwelo, kodi n’kupanda nzeru kutsatira mfundo za m’Baibulo zomwe zinalembedwa zaka 2000 zapitazo? Kodi anthu amene sakhulupirira Baibulo amanena zoona kuti kutsatira malangizo a m’Baibulo kuli ngati kugwiritsa ntchito buku lakalekale pophunzitsa sayansi? Nanga ndi zoona kuti kuli ngati kugwiritsa ntchito buku la malangizo la kompyuta yakalekale pofuna kudziwa mmene kompyuta yamakono imagwirira ntchito? Yankho la mafunso onsewa ndi lakuti ayi. Sayansi komanso luso la zopangapanga zimasinthasintha, koma zimene anthu amafunikira pa moyo wawo sizisintha. Mwachitsanzo, kuyambira kale anthu amafuna kudziwa cholinga cha moyo komanso zimene zingawathandize kuti azikhala osangalala ndiponso otetezeka. Amafunanso kudziwa zimene angachite kuti akhale ndi banja labwino komanso anzawo abwino.
Ngakhale kuti Baibulo ndi lakale kwambiri, lili ndi mfundo zothandiza pa nkhani zimenezi. Baibulo limanenanso kuti linauziridwa ndi Mulungu yemwe anatilenga. Limanenanso kuti lili ndi malangizo amene angatithandize pa nkhani iliyonse komanso vuto lililonse. (2 Timoteyo 3:16, 17) Kuwonjezera pamenepo, Baibulo limanenanso kuti malangizo ake sangakalambe kapena kutha ntchito. Baibulo limati: “Mawu a Mulungu ndi amoyo.”—Aheberi 4:12.
Kodi zimene Baibulo limanenazi ndi zoona? Kodi panopa linatha ntchito, kapena lidakali buku lothandiza kwambiri kuposa mabuku ena onse? Cholinga cha Nsanja ya Olonda imeneyi, yomwe ndi yoyamba pa Nsanja za Olonda zapadera zomwe zizituluka m’tsogolomu, ndi kukuthandizani kupeza mayankho a mafunso amenewa.