Kodi Mulungu Wachita Zinthu Ziti?
Ngati mukufuna kumudziwa bwino munthu, zimathandiza ngati mwadziwa zimene anachita, mavuto amene anakumana nawo komanso mmene anawathetsera. N’chimodzimodzinso ndi Mulungu. Ngati mukufuna kumudziwa bwino, muyenera kudziwa zinthu zimene wachita. Mungadabwe kuona kuti zimene anachita m’mbuyomu zimatithandiza panopa komanso zikhoza kudzatithandiza m’tsogolo.
ANALENGA ZINTHU ZONSE KUTI ZIZITITHANDIZA
Yehova Mulungu ndi Mlengi Wamkulu ndipo ‘chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe ake osaoneka ndi maso akuonekera bwino m’zinthu zimene anapanga.’ (Aroma 1:20) Iye ndi “amene anapanga dziko lapansi ndi mphamvu zake, amene mwanzeru zake anakhazikitsa dziko limene anthu amakhalamo. Iye ndi amenenso anayala kumwamba mwa kuzindikira kwake.” (Yeremiya 10:12) Zimene Mulungu analenga zimasonyeza kuti amatikonda.
Mwachitsanzo, taganizirani mmene anatilengera mwapadera kwambiri. Iye anatilenga “m’chifaniziro chake.” (Genesis 1:27) Zimenezi zikutanthauza kuti anatilenga m’njira yoti, pang’ono pokha, tizitha kusonyeza makhalidwe ake apamwamba. Anatilenganso m’njira yoti tizitha kudziwa mfundo zake za makhalidwe abwino komanso maganizo ake, ngakhale kuti sitingamvetse zonse. Tikamayesetsa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi zimenezi, timasangalala kwambiri komanso timaona kuti moyo wathu ndi waphindu. Chofunikanso kwambiri n’chakuti, anatilenga m’njira yoti tingathe kukhala naye pa ubwenzi.
Zinthu zimene Mulungu analenga padziko lapansili zimasonyezanso kuti amatikonda. Mtumwi Paulo ananena kuti Mulungu ‘sanangokhala wopanda umboni wakuti anachita zabwino. Anatipatsa mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zathu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yathu ndi chakudya komanso chimwemwe.’ (Machitidwe 14:17) Sikuti Mulungu anatipatsa zinthu zongoti bola tikhale ndi moyo. Anatipatsa zinthu zambiri komanso zosiyanasiyana kuti tizisangalala ndi moyo. Komatu zimenezi ndi zochepa chabe tikayerekezera ndi zinthu zimene ankafuna kuti tikhale nazo.
Salimo 115:16; Yesaya 45:18) Kodi ankafuna kuti padzikoli pakhale anthu otani, komanso akhale kwa nthawi yaitali bwanji? Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.
Yehova analenga dzikoli kuti anthu azikhalamo mpaka kalekale. Baibulo limati: “Dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu” ndipo ‘sanalilenge popanda cholinga koma analiumba kuti anthu akhalemo.’ (Mogwirizana ndi zimenezi, Yehova analenga Adamu ndi Hava, omwe anali anthu oyamba, ndipo anawaika m’munda wokongola “kuti aziulima ndi kuusamalira.” (Genesis 2:8, 15) Mulungu anawapatsa zochita. Anawauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire.” (Genesis 1:28) Choncho Adamu ndi Hava anali ndi mwayi woti akanakhala padzikoli mpaka kalekale. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anasankha kusamvera Mulungu ndipo anataya mwayi wokhala m’gulu la anthu “olungama” amene ‘adzalandire dziko lapansi.’ Komabe, monga tionere, zochita zawozo sizinachititse kuti cholinga cha Mulungu chokhudza dzikoli chisinthe. Koma tiyeni tikambirane kaye chinthu china chimene Mulungu anachita.
ANATIPATSA MAWU AKE
Baibulo limatchulidwanso kuti Mawu a Mulungu. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anatipatsa Baibulo? Chifukwa chachikulu ndi choti litithandize kuphunzira za iye. (Miyambo 2:1-5) N’zoona kuti Baibulo siliyankha funso lililonse lokhudza Mulungu limene tingakhale nalo, ndipo palibe buku limene lingachite zimenezi. (Mlaliki 3:11) Komabe zimene zili m’Baibulo zimatithandiza kuti tithe kumudziwa Mulungu. Timatha kudziwa kuti ndi wotani tikaona mmene amachitira zinthu ndi anthu. Timadziwanso kuti amakonda anthu otani, nanga sagwirizana ndi anthu otani. (Salimo 15:1-5) Timathanso kudziwa maganizo ake pa nkhani ya kulambira, makhalidwe abwino komanso zinthu zakuthupi. Komanso Baibulo limatithandiza kudziwa bwinobwino kuti Yehova ndi wotani kudzera mu zimene Mwana wake, Yesu Khristu ananena komanso kuchita.—Yohane 14:9.
Chifukwa china chimene Yehova anatipatsira Baibulo ndi choti tidziwe zimene tingachite kuti tikhale ndi moyo wosangalala. Kudzera m’Baibulo, Yehova amatiuza zimene tingachite kuti tizikhutira ndi zimene tili nazo komanso kuti tikhale ndi banja losangalala. Amatiuzanso zoyenera kuchita tikakhala ndi nkhawa. Ndipo monga tionere m’magazini yomweyi, m’Baibulo mulinso mayankho a mafunso ofunika kwambiri, monga akuti: N’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri chonchi? Nanga m’tsogolomu muchitika zotani? Limafotokozanso zimene Mulungu wachita poonetsetsa kuti cholinga chake chidzakwaniritsidwe.
Pali zinthu zinanso zambiri zosonyeza kuti Baibulo ndi buku lapadera ndipo ndi lochokeradi kwa Mulungu. Panatenga zaka 1,600 kuti Baibulo amalize kulilemba ndipo linalembedwa ndi anthu pafupifupi 40. Koma chifukwa choti Mlembi wake wamkulu ndi Mulungu, zimene limanena n’zogwirizana ndipo mfundo yake yaikulu ndi imodzi. (2 Timoteyo 3:16) Mosiyana ndi mabuku ena akale, Baibulo lakhala lilipobe mpaka pano ndipo uthenga wake sunasinthidwe. Umboni wa zimenezi ndi mipukutu yambirimbiri ya Baibulo imene anthu anapeza. Komanso Baibulo lakhalapo mpaka pano ngakhale kuti panali anthu ambiri amene ankafuna kuti lisamasuliridwe, lisafalitsidwe komanso lisamawerengedwe. Ndipotu panopa Baibulo limafalitsidwa kwambiri komanso lamasuliridwa m’zilankhulo zambiri kuposa buku lina lililonse. Mfundo yoti Baibulo lidakalipo mpaka pano, ndi umboni wakuti “mawu a Mulungu wathu adzakhala mpaka kalekale.”—Yesaya 40:8.
ANACHITA ZINTHU ZOTHANDIZA KUTI CHOLINGA CHAKE CHISADZALEPHEREKE
Mulungu anachita chinthu china chapadera poonetsetsa kuti cholinga chake chidzakwaniritsidwe. Monga tafotokozera kale, Mulungu ankafuna kuti anthu akhale padzikoli kwamuyaya. Koma pamene Adamu anasankha kusamvera Mulungu n’kuchita tchimo, anataya mwayi wokhala ndi moyo wosatha, osati wake wokha komanso wa ana ake. ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’ (Aroma 5:12) Apa kuchimwa kwa Adamu kukanatha kuchititsa kuti cholinga cha Yehova chilephereke. Ndiye kodi Yehova anatani?
Zimene Yehova anachita zinali zogwirizana ndi makhalidwe ake. Mwachilungamo anaweruza Adamu ndi Hava n’kuwapatsa chilango, koma mwachikondi Genesis 3:15) Njira yopulumutsira anthu ku uchimo ndi imfa inali yoti idzaperekedwa kudzera mwa Mwana wake, Yesu Khristu. Kodi zimenezi zinachitika bwanji?
anakonza njira yopulumutsira ana awo. Mwanzeru zake Yehova anapeza njira yabwino yothetsera vutoli ndipo nthawi yomweyo anatchula njirayo. (Kuti awombole anthu ku zotsatira za uchimo wa Adamu, Yehova anatumiza Yesu padzikoli kudzaphunzitsa anthu njira yopezera moyo komanso “kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” a (Mateyu 20:28; Yohane 14:6) Yesu anatha kupereka dipo chifukwa choti anali wangwiro ngati Adamu. Koma mosiyana ndi Adamu, Yesu anakhalabe wokhulupirika mpaka analolera kufa. Popeza Yesu sanachite zinthu zoyenera kuphedwa, Yehova anamuukitsa ndipo anabwerera kumwamba. Yesu anatha kuchita zimene Adamu analephera. Anapangitsa kuti anthu omvera akhale ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha. “Pakuti monga mwa kusamvera kwa munthu mmodziyo, ambiri anakhala ochimwa, momwemonso kudzera mwa kumvera kwa munthu mmodziyu, ambiri adzakhala olungama.” (Aroma 5:19) Kudzera mu nsembe ya dipo ya Yesu, Mulungu adzakwaniritsa cholinga chake choti anthu akhale padzikoli kwamuyaya.
Timadziwa zambiri zokhudza Yehova tikaganizira zimene anachita Adamu atasonyeza kusamvera. Timaona kuti palibe chimene chingamulepheretse kukwaniritsa zomwe wayamba ndipo mawu ake “adzakwaniritsadi” zimene iye akufuna. (Yesaya 55:11) Timaonanso kuti Yehova amatikonda kwambiri anthufe. “Mulungu anatisonyeza ife chikondi chake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzera mwa iye. Chikondi chimenechi chikutanthauza kuti ife sitinakonde Mulungu, koma iye ndi amene anatikonda ndi kutumiza Mwana wake monga nsembe yophimba machimo athu.”—1 Yohane 4:9, 10.
Mulungu “sanaumire ngakhale Mwana wake koma anamupereka m’malo mwa ife tonse.” Choncho tili ndi chikhulupiriro kuti ‘adzatipatsanso mokoma mtima zinthu zina zonse’ zimene walonjeza. (Aroma 8:32) Kodi watilonjeza zinthu ziti? Pitirizani kuwerenga magaziniyi kuti muzidziwe.
KODI MULUNGU WACHITA ZINTHU ZITI? Yehova analenga anthu kuti akhale padzikoli kwamuyaya. Anatipatsa Baibulo kuti litithandize kuphunzira za iye. Kudzera mwa Yesu Khristu, Yehova anapereka dipo pofuna kuonetsetsa kuti cholinga chake chidzakwaniritsidwe
a Kuti mudziwe zambiri zokhudza dipo, onani phunziro 27 m’buku lakuti, Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Bukuli ndi lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo likupezekanso pa webusaiti ya www.pr418.com/ny.