Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”​—Yakobo 4:8.

Kodi Mulungu Amamva Mapemphero Athu?

Kodi Mulungu Amamva Mapemphero Athu?

Kodi munayamba mwadzifunsapo ngati Mulungu amamva mukamapemphera? Ngati zili choncho, si inu nokha. Anthu ambiri anapemphapo Mulungu kuti awathandize pa mavuto enaake koma mavutowo sanathe. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu amanyalanyaza mapemphero athu? Ayi ndithu. Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu amamvetsera tikamapemphera kwa iye m’njira yoyenera. Tiyeni tione zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.

MULUNGU AMAMVETSERA

“Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.”​—Salimo 65:2.

Anthu ena amanena kuti amamva bwino akamapemphera ngakhale kuti sakhulupirira zoti winawake akumvetsera. Koma cholinga cha kupemphera si kungotikhazika mtima pansi tikakumana ndi mavuto. Baibulo limatitsimikizira kuti “Yehova * ali pafupi ndi onse oitanira pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’choonadi . . . Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”​—Salimo 145:18, 19.

Choncho palibe chifukwa chokayikirira kuti Yehova Mulungu amamva mapemphero a anthu amene amamulambira. Iye amanena mwachikondi kuti: “Mudzaitanira pa ine komanso mudzabwera ndi kupemphera kwa ine ndipo ine ndidzakumvetserani.”​—Yeremiya 29:12.

MULUNGU AMAFUNA KUTI MUZIPEMPHERA KWA IYE.

“Limbikirani kupemphera.”​—Aroma 12:12.

Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tizipemphera kosalekeza’ komanso ‘tizipemphera pa chochitika chilichonse.’ Apa zikuonekeratu kuti Yehova Mulungu amafuna kuti tizipemphera kwa iye.​—Mateyu 26:41; Aefeso 6:18.

N’chifukwa chiyani Mulungu amafuna kuti tizipemphera kwa iye? Taganizirani izi: Kodi pali bambo amene sangafune kuti mwana wake anene kuti, “Kodi bambo mungandithandizeko”? N’zoona kuti mwina bamboyo amadziwa kale zimene mwana wake amafunikira. Koma akamva mwanayo akupempha thandizo, zimasonyeza kuti mwanayo amadalira komanso kukonda bambo wakeyo. Mofanana ndi zimenezi, tikamapemphera kwa Mulungu timasonyeza kuti timamudalira komanso timafuna kugwirizana naye.​—Miyambo 15:8; Yakobo 4:8.

MULUNGU AMAKUKONDANI.

‘Muzimutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’​—1 Petulo 5:7.

Mulungu amafuna kuti tizipemphera kwa iye chifukwa amatikonda komanso kutidera nkhawa. Iye amadziwa bwino nkhawa zathu ndipo amafuna kutithandiza.

Nthawi zonse, Mfumu Davide ankapemphera kwa Yehova pofuna kupempha thandizo komanso kumuuza maganizo ake ndiponso mmene ankamvera mumtima mwake. (Salimo 23:1-6) Ndiye kodi Mulungu ankamuona bwanji Davide? Iye ankamukonda ndipo ankamvetsera mapemphero ake onse. (Machitidwe 13:22) Mulungu amamvetseranso mapemphero athu chifukwa amatikonda.

“MTIMA WANGA NDI WODZAZA NDI CHIKONDI CHIFUKWA YEHOVA AMAMVA MAWU ANGA”

Mawuwa ananenedwa ndi munthu wina amene analemba nawo masalimo a m’Baibulo. Iye sankakayikira kuti Mulungu ankamva mapemphero ake. Zimenezi zinkamuthandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu komanso kupirira mavuto amene ankakumana nawo.​—Salimo 116:1-9.

Tikamakhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu amamva mapemphero athu, tidzapitiriza kupemphera pafupipafupi. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Pedro amene amakhala kumpoto kwa dziko la Spain. Mwana wake wazaka 19 anafa pa ngozi yapamsewu. Pedro anamva chisoni kwambiri ndipo anauza Mulungu zamumtima mwake zonse. Ankamupemphanso mobwerezabwereza kuti azimulimbikitsa ndiponso kumuthandiza. Ndiye n’chiyani chinachitika? Pedro anati: “Yehova anayankha mapemphero anga pogwiritsa ntchito Akhristu anzathu kuti azitilimbikitsa komanso kutithandiza ine ndi mkazi wanga.”

Nthawi zambiri Mulungu amayankha mapemphero athu pogwiritsa ntchito anzathu kuti azitilimbikitsa komanso kutithandiza

N’zoona kuti mapemphero sanathandize kuti mwana wa Pedro akhalenso ndi moyo, koma anathandiza Pedro ndi banja lake m’njira zina zofunika. Mkazi wake dzina lake María Carmen anati: “Kupemphera kunkandithandiza kupirira chisoni chimene ndinali nacho. Ndinkadziwa kuti Yehova Mulungu akundimvetsa chifukwa ndikapemphera kwa iye mtima wanga unkakhala m’malo.”

Baibulo komanso zitsanzo za anthu ena zimasonyeza kuti Mulungu amamva mapemphero athu. Koma pali mapemphero ena amene Mulungu sayankha. N’chifukwa chiyani Mulungu amayankha mapemphero ena koma ena ayi?

^ ndime 5 Yehova ndi dzina la Mulungu.​—Salimo 83:18.