N’chifukwa Chiyani Chidani Sichikutha?
N’chifukwa chiyani anthu akudana kwambiri padzikoli? Kuti tidziwe chifukwa chake, tiyenera kudziwa kaye kuti chidani n’chiyani, chifukwa chake anthu anayamba kudana, komanso chifukwa chake chidani chili ponseponse.
Kodi Chidani N’chiyani?
Chidani chimatanthauza kusakonda kapena kuipidwa kwambiri ndi munthu winawake kapenanso gulu linalake la anthu. Sichimangotanthauza kukwiyira munthu kwa nthawi yochepa chabe koma kuipidwa naye kwa nthawi yaitali.
N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU AMAYAMBA KUDANA?
Pali zifukwa zosiyanasiyana zimene zimachititsa anthu kuyamba kudana. Nthawi zambiri anthu amayamba kudana ndi anthu ena osati chifukwa chakuti alakwitsa zinazake, koma chifukwa chakuti ndi amtundu winawake. Choncho amadana nawo chifukwa amaganiza kuti anthu onse amtundu umenewo ndi oipa, oopsa ndiponso sangasinthe khalidwe lawo. Ena angayambe kuwaona ngati anthu otsika, kuyamba kuwaopa kapenanso kuwaganizira kuti angayambitse mavuto. Anthu amene amadana ndi anzawo nthawi zambiri amakhala kuti anakumanapo ndi zinthu zinazake zoipa monga zachiwawa, zopanda chilungamo kapenanso zinazake zomwe zinachititsa kuti chidani chikhazikike mumtima mwawo.
KODI CHIDANI CHIMAFALIKIRA BWANJI?
Nthawi zina munthu angayambe kudana ndi anthu ena ngakhale kuti sanakumanepo nawo. Mwachitsanzo, munthu wina angayambe kudana ndi anthu ena mosadziwa chifukwa chotengera anthu am’banja lake kapena anzake. Choncho chidanicho chimafalikira kwa anthu onsewo ndipo nawonso amayamba kudana ndi anthu amtundu winawo.
Tikamvetsa chifukwa chake chidani chimafalikira mosavuta, tidziwanso chifukwa chake anthu ambiri amayamba kudana ndi anthu ena. Komabe, kuti tithetse chidani chomwe chili ponseponse padzikoli, tiyenera kudziwa mmene chinayambira. Baibulo limafotokoza momveka bwino mmene chidani chinayambira.
BAIBULO LIMATIUZA MMENE CHIDANI CHINAYAMBIRA
MNGELO WOIPA NDI AMENE ANAYAMBITSA CHIDANI. Chidani chinayamba pamene mngelo wina yemwe anadzayamba kudziwika ndi dzina lakuti Satana Mdyerekezi, anapandukira Mulungu. Mdyerekezi “ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake.” Ndiponso “iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.” Choncho amalimbikitsa anthu kuti azidana ndi ena ndiponso kuwachitira zinthu zoipa. (Yohane 8:44; 1 Yohane 3:11, 12) Baibulo limafotokoza kuti iye ndi wankhanza, wokwiya komanso waukali.—Yobu 2:7; Chivumbulutso 12:9, 12, 17.
ANTHU AMADANA NDI ANZAWO CHIFUKWA CHAKUTI ANABADWA NDI UCHIMO. Munthu woyamba Adamu, anamvera Satana n’kuchimwa. Choncho iye anapatsira anthu onse uchimo. (Aroma 5:12) Kenako, Kaini yemwe anali mwana woyamba wa Adamu, anapha m’bale wake Abele chifukwa ankadana naye. (1 Yohane 3:12) N’zoona kuti anthu ambiri amakonda anzawo ndi kuwachitira chifundo. Komabe, chifukwa chakuti anabadwa ndi uchimo anthu ambiri amasonyeza makhalidwe amene amayambitsa chidani monga kudzikonda, nsanje ndiponso kunyada.—2 Timoteyo 3:1-5.
ANTHU AMADANA KWAMBIRI NGATI SALOLERANA. M’dzikoli anthu ambiri sachitira ena chifundo ndipo amawachitira zinthu zoipa. Zimenezi n’zimene zimachititsa kuti anthu azidana kwambiri. Zinthu monga tsankho, kunyozana, kuchitirana nsanje komanso kuwononga zinthu za ena, zili ponseponse masiku ano chifukwa chakuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo,” yemwe ndi Satana Mdyerekezi.—1 Yohane 5:19.
Komabe, Baibulo silimangotiuza mmene chidani chinayambira, m’malomwake limatiuzanso mmene tingachithetsere.