KODI TINGATHETSE BWANJI CHIDANI?
4 | Mulungu Angakuthandizeni Kuthetsa Mtima Wachidani
Baibulo Limati:
“Makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndiwo chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa.”—AGALATIYA 5:22, 23.
Zimene Lembali Limatanthauza:
Mulungu angatithandize kuthetsa chidani. Mzimu wake woyera ungatithandize kukhala ndi makhalidwe amene patokha sitingakwanitse kukhala nawo. Choncho, m’malo moyesetsa kulimbana ndi kuthetsa mtima wachidani patokha, tingachite bwino kudalira Mulungu kuti atithandize. Tikachita zimenezi tidzafanana ndi Paulo yemwe analemba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afilipi 4:13) Komanso tidzanena kuti: “Thandizo langa lichokera kwa Yehova.”—Salimo 121:2.
Mmene Lembali Lingakuthandizireni:
“Yehova wandithandiza kuti ndisinthe khalidwe langa lokonda zachiwawa moti panopa ndine munthu wokonda mtendere.”—WALDO
Muzipemphera kwa Yehova moona mtima kuti akupatseni mzimu wake woyera. (Luka 11:13) Muzimupempha kuti akuthandizeni kukhala ndi makhalidwe abwino. Muziphunzira Baibulo kuti mudziwe makhalidwe amene angakuthandizeni kuthetsa chidani monga chikondi, mtendere, kuleza mtima ndi kudziletsa. Muziyesetsa kuganizira zimene mungachite kuti mukhale ndi makhalidwe amenewa pa moyo wanu. Ndiponso muzicheza ndi anthu omwe akuyesetsa kukhala ndi makhalidwe amenewa. Anzanu oterewa ‘adzakulimbikitsani pa chikondi ndi ntchito zabwino.’—Aheberi 10:24.