Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI TINGATHETSE BWANJI CHIDANI?

2 | Musamabwezere

2 | Musamabwezere

Baibulo Limati:

“Musabwezere choipa pa choipa. . . . Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere. Musabwezere, . . . pakuti Malemba amati: ‘“Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine, watero Yehova.’”​AROMA 12:17-19.

Zimene Lembali Limatanthauza:

Ngakhale kuti mwachibadwa anthufe timakwiya munthu wina akatilakwira, Mulungu safuna kuti tizibwezera. M’malomwake, iye amafuna kuti tizimuyembekezera moleza mtima chifukwa posachedwapa adzathetsa zinthu zonse zopanda chilungamo.​—Salimo 37:7, 10.

Mmene Lembali Lingakuthandizireni:

Popeza kuti anthufe tinabadwa ndi uchimo, tikamabwezera zoipa zimene anthu ena atichitira, zimangochititsa kuti chidani chizipitirira. Choncho, musamabwezere munthu wina akakulakwirani kapena akakuchitirani zoipa. Muziyesetsa kuugwira mtima komanso kuyankha modekha. Nthawi zinanso ndi bwino kungoisiya nkhaniyo. (Miyambo 19:11) Komabe, ngati pali zifukwa zomveka, nthawi zina mungachite bwino kuuza ena zomwe zakuchitikirani. Mwachitsanzo, ngati munthu wina wakuchitirani nkhanza zoopsa, mungasankhe kukanena nkhaniyo kupolisi kapena kwa akuluakulu ena m’dera lanu.

Anthu amene amakonda kubwezera amangodziika m’mavuto

Mungatani ngati zikukuvutani kuthetsa nkhaniyo mwamtendere? Nanga mungatani ngati mwayesapo kale kuthetsa nkhaniyo mwamtendere koma zikuvutabe? Musamabwezere. Zili choncho chifukwa kubwezera kungangokulitsa vutolo. Koma mukasankha kusabwezera mungathandize kuti chidani chisapitirire. Muzidalira Mulungu ndipo muzikhulupirira kuti iye ali ndi njira yabwino yothetsera mavuto. Baibulo limati: “Umudalire ndipo iye adzachitapo kanthu.”​—Salimo 37:3-5.