KODI TINGATHETSE BWANJI CHIDANI?
1 | Muziyesetsa Kupewa Tsankho
Baibulo Limati:
“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—MACHITIDWE 10:34, 35.
Zimene Lembali Limatanthauza:
Yehova * Mulungu samatiweruza potengera mtundu wathu, mmene khungu lathu limaonekera kapenanso chikhalidwe chathu. Mulungu amaona zinthu zofunika kwambiri monga zomwe timaganiza komanso zimene timalakalaka mumtima mwathu. Baibulo limanenanso kuti munthu amaona zooneka ndi maso “koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”—1 Samueli 16:7.
Mmene Lembali Lingakuthandizireni:
Ngakhale sitingadziwe zimene zili mumtima mwa munthu, tingatsanzire Mulungu pokhala anthu opanda tsankho. Muziyesetsa kuona munthu wina aliyense payekha m’malo momuweruza potengera mtundu wake. Ngati mukuona kuti muli ndi maganizo olakwika okhudza anthu ena chifukwa cha mtundu wawo, mungachite bwino kupemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni kuthetsa maganizo amenewo. (Salimo 139:23, 24) Ngati mungapemphere kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima kuti akuthandizeni kukhala opanda tsankho, iye adzayankha pemphero lanu ndipo adzakuthandizani.—1 Petulo 3:12.
^ ndime 6 Yehova ndi dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.
“Ndinali ndisanakhalepo mwamtendere ndi mzungu . . . Tsopano zinali zotheka chifukwa ndili mu m’gulu la anthu okondana kwambiri lapadziko lonse.”—TITUS