NSANJA YA OLONDA Na. 1 2023 | Matenda Amaganizo—Mmene Baibulo Lingakuthandizireni
Padziko lonse lapansi, anthu mamiliyoni ambiri amakhudzidwa ndi matenda ovutika maganizo. Anthu osiyanasiyana, ana ndi akulu omwe, akulimbana ndi matenda ovutika maganizo. Iwo akukumana ndi zimenezi posatengera kuti ndi olemera kapena osauka, maphunziro, chipembedzo, mtundu kapena chikhalidwe chawo. Kodi matenda ovutika maganizo ndi chiyani? Nanga amakhudza bwanji anthu? Magaziniyi ikufotokoza kufunika kopeza thandizo loyenerera la kuchipatala komanso ikufotokoza njira zosiyanasiyana za mmene Baibulo lingathandizire anthu amene akuvutika ndi matendawa.
Matenda Ovutika Maganizo Ndi Vuto la Padziko Lonse
Matenda ovutika maganizo akhoza kukhudza munthu wina aliyense posatengera msinkhu kapena kochokera. Onani mmene malangizo a m’Baibulo angakuthandizireni ngati muli ndi matendawa.
Mulungu Amasamala za Inu
N’chiyani chingakutsimikizireni kuti Yehova Mulungu amamvetsa maganizo anu komanso mmene mukumvera mumtima mwanu kuposa wina aliyense?
1 | Pemphero—‘Muzimutulira Nkhawa Zanu Zonse’
Kodi muyeneradi kupemphera kwa Mulungu n’kumuuza nkhawa zanu? Kodi pemphero lingathandize bwanji anthu amene akuvutika ndi nkhawa?
2 | ‘Malemba Angakulimbikitseni’
Uthenga wa m’Baibulo umatipatsa chiyembekezo chodalirika chakuti posachedwapa ululu wonse wamumtima udzatheratu.
3 | Zitsanzo za M’Baibulo Zingakuthandizeni
M’Baibulo muli zitsanzo za amuna ndi akazi omwe anali anthu ngati ife tomwe. Zitsanzozi zingatithandize kuti tisamadzimve kuti tili tokhatokha pamene tasokonezeka maganizo.
4 | Baibulo Lingakupatseni Malangizo Othandiza
Onani mmene kuganizira mavesi a m’Baibulo komanso kukhala ndi zolinga zomwe tingadzikwaniritsedi kungatithandizire kuti tipirire mavuto obwera chifukwa cha matenda amaganizo.
Mmene Mungathandizire Amene Akudwala Matenda Amaganizo
Kuthandiza mnzanu yemwe akuvutika ndi matenda amaganizo kungasinthe zinthu pa moyo wake.