3 | Zitsanzo za M’Baibulo Zingakuthandizeni
BAIBULO LIMAFOTOKOZA ZA . . . Amuna ndi akazi okhulupirika amene anavutikapo ndi nkhawa ndipo anali ‘anthu ngati ife tomwe.’—YAKOBO 5:17.
Tanthauzo Lake
M’Baibulo muli zitsanzo zambiri zimene zinachitikadi za amuna ndi akazi amene anavutikapo ndi nkhawa zosiyanasiyana. Tikamawerenga nkhani zimenezi, tikhoza kupeza zitsanzo zimene zingafanane ndi zimene zikutichitikira ifeyo.
Mmene Zimenezi Zingakuthandizireni
Tonsefe timafuna titadziwa ngati anthu ena amamvetsa mmene timamvera, makamaka ngati tikuvutika ndi matenda amaganizo. Tikamawerenga Baibulo, timaphunzira za anthu amene ankaganiza komanso kumva ngati mmene ifeyo timamvera. Zimenezi zimatithandiza kuzindikira kuti pali anthu enanso amene anakumanapo ndi mavuto a nkhawa komanso kuvutika maganizo ndipo timamva kuti sitili tokha.
M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene anadzimvapo kuti ndi osafunika ndipo alibe chiyembekezo chilichonse. Kodi munayamba mwavutikapo maganizo mpaka kufika ponena kuti, ‘Basi ine ndatopa nazo?’ Mose, Eliya komanso Davide anamvapo choncho.—Numeri 11:14; 1 Mafumu 19:4; Salimo 55:4.
Baibulo limatiuza za mzimayi wina dzina lake Hana amene ‘anakhumudwa kwambiri’ chifukwa choti anali wosabereka ndiponso mkazi mnzake ankamunyoza kwambiri.—1 Samueli 1:6, 10.
Baibulo limatiuzanso za munthu wina dzina lake Yobu yemwe chitsanzo chake chingatithandizenso. Ngakhale kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova, iye anavutikapo ndi nkhawa mpaka kufika ponena kuti: “Moyo ndaukana sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.”—Yobu 7:16.
Ifenso tikhoza kupeza mphamvu zimene zingatithandize kulimbana ndi nkhawa zosiyanasiyana, tikamaganizira zitsanzo za anthu ngati amenewa omwe anakwanitsa kulimbana ndi maganizo olakwika.