Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mungathandizire Amene Akudwala Matenda Amaganizo

Mmene Mungathandizire Amene Akudwala Matenda Amaganizo

BAIBULO LIMATI: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—MIYAMBO 17:17.

Tanthauzo Lake

Tikhoza kusowa chochita ngati mnzathu akuvutika ndi matenda amaganizo. Komabe, tingasonyeze kuti timamukonda poyesetsa kumuthandiza kuti apirire vuto lakelo.

Mmene Mungachitire Zimenezi

‘Muzikhala wofulumira kumva.’—YAKOBO 1:19.

Njira yoyamba yofunika kwambiri pomuthandiza mnzanuyo ndi kumumvetsera akamalankhula. Musamayembekezere kuti mukufunika kuyankha chilichonse chimene angalankhule. Muzisonyeza kuti mukumumvetsera komanso kuti mumamuganizira. Muzilankhula naye momasuka komanso musamamuweruze. Muzikumbukira kuti nthawi zina angalankhule zinthu zimene sangakhale kuti akutanthauza zimenezo kwenikweni ndipo pambuyo pake angayambe kumadziimba mlandu.​—Yobu 6:2, 3.

‘Muzilankhula molimbikitsa.’—1 ATESALONIKA 5:14.

Mnzanuyo akhoza kukhala ndi nkhawa kapena angamalimbane ndi vuto lodziona kuti ndi wachabechabe. Mungamulimbikitse kwambiri komanso kumutonthoza, mukamamutsimikizira kuti mumamukonda ngakhale musakudziwa zoti munene.

“Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse.”​—MIYAMBO 17:17.

Muzichita zinazake pomuthandiza. M’malo moganiza kuti mukudziwa kale zoyenera kuchita kuti mumuthandize, muzimupempha kuti akuuzeni zomwe akufuna kuti mumuchitire. Ngati mnzanuyo akulephera kukufotokozerani zimene akufunikira, muziyesa kukambirana naye zinthu zimene mungachitire limodzi monga kukayendera limodzi kumalo enaake. Mwinanso mungamupemphe kuti mukamugulire zinthu kumsika, kumuthandiza ntchito zapakhomo kapenanso zinthu zina.​—Agalatiya 6:2.

‘Muzikhala oleza mtima.’—1 ATESALONIKA 5:14.

Si nthawi zonse pamene mnzanuyo angakhale womasuka kufotokoza maganizo ake. Muzimutsimikizira kuti ndinu wokonzeka kumumvetsera pa nthawi ina iliyonse yomwe angafune kukufotokozerani maganizo ake. Chifukwa cha matenda amene akudwalawo, iye akhoza kuchita kapena kulankhula zinthu zina zimene zingakukhumudwitseni. Ndipo nthawi zina, akhoza kusintha zinthu zimene munapangana kuti muchitire limodzi kapenanso akhoza kukwiya zosadziwika bwino. Choncho, muzichita naye zinthu moleza mtima komanso kumumvetsa pa nthawi imene mukumuthandizayo.​—Miyambo 18:24.

Zimene Mungachite Zingathandize Mnzanuyo

“Ndimayesetsa kuchita zinthu zosonyeza kuti ndine mnzake amene angamudalire. Ngakhale kuti nthawi zina sindingathe kumuthandiza kuthana ndi mavuto ake, komabe ndimamumvetsera mwachidwi akamandifotokozera nkhawa zake. Nthawi zina, iye amangofuna kuti munthu amumvetsere basi ndipo amamva bwino.”​—Farrah, a yemwe mnzake amadwala matenda a nkhawa, ovutika kudya komanso matenda aakulu amaganizo (clinical depression).

“Ndili ndi mnzanga wina yemwe amandichitira zinthu mokoma mtima komanso amandilimbikitsa. Tsiku lina anandiitanira kunyumba kwake kuti tikadyere limodzi chakudya. Zinali zosavuta kumufotokozera nkhawa zanga chifukwa cha chikondi chachikulu chimene anandisonyeza. Zimenezi zinandilimbikitsa kwambiri.”​—Ha-eun, yemwe amadwala matenda aakulu amaganizo (clinical depression).

“Kuleza mtima ndi kofunika kwambiri. Mkazi wanga akachita zinazake zondikhumudwitsa, ndimadzikumbutsa kuti vuto si iyeyo koma ndi matenda akewo. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizipewa kupsa mtima komanso ndizichita zinthu momuganizira.”​—Jacob, yemwe mkazi wake amadwala matenda aakulu amaganizo (clinical depression).

“Mkazi wanga wakhala akundithandiza komanso kunditonthoza kwambiri. Ndikapanikizika kwambiri ndi nkhawa, iye samandikakamiza kuti ndichite zinthu zimene sindikufuna. Nthawi zina, iye amalolela kusachita zinthu zimene akanasangalala kuzichita. Iye ndi wapadera kwambiri kwa ine chifukwa ndi wodzimana komanso ndi wodzichepetsa.”​—Enrico, yemwe amadwala matenda a nkhawa (anxiety disorder).

a Mayina ena asinthidwa.