Kodi Mulungu Amamva Bwanji Akamakuonani Mukuvutika?
Anthu ena amaganiza kuti Mulungu sizimam’khudza akamaona anthu akuvutika ndipo ena amaganiza kuti saona n’komwe.
TAGANIZIRANI ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Mulungu amaona komanso amakhudzidwa tikamavutika
“Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kwachuluka padziko lapansi . . . ndipo zinam’pweteka kwambiri mumtima.”—Genesis 6:5, 6.
Mulungu adzathetsa mavuto onse
“Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:10, 11.
Mulungu amatifunira zabwino
“‘Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizira zokupatsani mtendere osati masoka, kuti mukhale ndi chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino,’ watero Yehova. ‘Mudzaitanira pa ine komanso mudzabwera ndi kupemphera kwa ine ndipo ine ndidzakumvetserani.’”—Yeremiya 29:11, 12.
“Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.