Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Imfa Idzagonjetsedwa Bwanji?

Kodi Imfa Idzagonjetsedwa Bwanji?

NGAKHALE kuti kusamvera kwa Adamu ndi Hava kunabweretsa uchimo ndi imfa kumtundu wonse wa anthu, cholinga cha Mulungu chokhudza anthu sichinasinthe. Kudzera m’Mawu ake Baibulo, Mulungu amatitsimikizira mobwerezabwereza kuti cholinga chake sichinasinthe.

  • “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”Salimo 37:29.

  • “Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.”​Yesaya 25:8.

  • “Imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.”​1 Akorinto 15:26.

  • “Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”​Chivumbulutso 21:4.

Kodi Mulungu “adzameza” bwanji imfa kapena kuti kuiwononga? Monga taonera kale, Baibulo limanena kuti ‘Olungama adzakhala kwamuyaya.’ Koma limanenanso kuti: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha.” (Mlaliki 7:20) Pogonjetsa imfa, kodi ndiye kuti Mulungu adzaphwanya mfundo zake? Ayi. Iye sangachite zimenezo m’pang’ono pomwe chifukwa ndi “Mulungu amene sanganame.” (Tito 1:2) Ndiye kodi Mulungu adzakwaniritsa bwanji cholinga chimene anali nacho pamene ankalenga anthu?

MULUNGU “ADZAMEZA IMFA KWAMUYAYA.”​—YESAYA 25:8

KUGONJETSA IMFA POPEREKA DIPO

Mwachikondi Mulungu anapereka dipo monga njira yowombolera anthu ku imfa. Dipo ndi malipiro amene amaperekedwa polipira zinthu zomwe zawonongedwa kapena pofuna kuti pakhale chilungamo. Malipirowo amafunika kukhala ofanana ndendende ndi zinthu zomwe zawonongedwazo. Popeza anthu onse ndi ochimwa ndipo ndi oyenera kufa, Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene angathe kuwombola m’bale wake, kapena kumuperekera dipo kwa Mulungu, (ndipo malipiro owombolera moyo wawo ndi amtengo wapatali, moti munthu sangathe kuwapereka mpaka kalekale).”​—Salimo 49:7, 8.

Munthu akamwalira, amakhala kuti wapereka malipiro a machimo ake okha. Munthu wopanda ungwiro sangathe kudziperekera dipo kapena kupereka dipo lowombola anthu ena. (Aroma 6:7) Pankafunika munthu wangwiro komanso wopanda uchimo kuti apereke moyo wake, osati chifukwa cha machimo ake, koma chifukwa cha machimo athu.​—Aheberi 10:1-4.

Zimenezi ndi zimene Mulungu anachita. Anatumiza Mwana wake, Yesu, kuchokera kumwamba kuti adzabadwe padzikoli monga munthu wangwiro komanso wopanda uchimo. (1 Petulo 2:22) Yesu ananena kuti anabwera “kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Maliko 10:45) Iye anafa chifukwa cha machimo athu komanso kuti atiwombole ku imfa n’cholinga choti tidzakhale ndi moyo wosatha.​—Yohane 3:16.

KODI IMFA IDZAGONJETSEDWA LITI?

Masiku ano, mogwirizana ndi zimene Baibulo linalosera, tikukhala mu “nthawi yapadera komanso yovuta” ndipo umenewu ndi umboni wakuti tili “m’masiku otsiriza” a dziko loipali. (2 Timoteyo 3:1) Masiku otsiriza adzafika kumapeto pa ‘tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.’ (2 Petulo 3:3, 7) Koma anthu amene amakonda Mulungu adzapulumuka ndipo adzakhala ndi “moyo wosatha.”​—Mateyu 25:46.

Yesu anabwera “kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.”​—Maliko 10:45

Anthu enanso ambirimbiri adzaukitsidwa n’kupeza mwayi wokhala ndi moyo wosatha. Yesu atapita mumzinda wa Naini anaukitsa mwana wa mayi wina wamasiye. Iye anachita zimenezi chifukwa choti anamuchitira “chifundo” mayiyo. (Luka 7:11-15) Nayenso mtumwi Paulo analemba kuti: “Ine ndili ndi chiyembekezo mwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” Chiyembekezo chimenechi ndi umboni wosatsutsika wakuti Mulungu amakonda anthu.​—Machitidwe 24:15.

Anthu mamiliyoni ambiri angakhale ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha. Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Pa nthawiyo adzasangalala kwambiri kuona kukwaniritsidwa kwa mawu amene mtumwi Paulo analemba zaka pafupifupi 2,000 zapitazo akuti, “Imfa iwe, kupambana kwako kuli kuti? Imfawe, mphamvu yako ili kuti?” (1 Akorinto 15:55) Pamenepatu imfa idzakhala itagonjetsedwa.