Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala

Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala

INUNSO mungathe kudzakhala ndi moyo wopanda matenda, ukalamba komanso imfa. Koma panopa moyo ndi wa mavuto okhaokha. Ndiye kodi mungatani kuti muzikhala wosangalala? M’Baibulo muli malangizo amene angakuthandizeni. Tiyeni tione mmene Baibulo lingatithandizire kukhala osangalala.

KUKHALA WOKHUTIRA

Malangizo a m’Baibulo: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.”Aheberi 13:5.

Masiku ano pali zinthu zambiri zimene anthu a m’dzikoli amati tiyenera kukhala nazo. Koma Baibulo limanena kuti mungathe kumakhala “okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.” Ndiye kodi mungatani kuti muzikhala okhutira?

Muzipewa “kukonda ndalama.” Anthu ena amalolera kuwononga thanzi lawo, kusokoneza banja lawo, kudana ndi anzawo, kuchita makhalidwe oipa kapenanso kudzichotsera ulemu chifukwa ‘chokonda ndalama.’ (1 Timoteyo 6:10) Komatu kumeneku n’kupanda nzeru. Ndipo anthu oterewa pamapeto pake amakhalabe ‘osakhutira.’​—Mlaliki 5:10.

Muziona kuti anthu ndiye ofunika kwambiri. N’zoona kuti zinthu zina zomwe tili nazo ndi zothandiza. Koma zinthu zimenezi sizingatikonde kapena kutiyamikira. Anthu ndi amene angachite zimenezi. Kukhala ndi “bwenzi lenileni” kumatithandiza kuti tizikhala okhutira.​—Miyambo 17:17.

TIKHOZA KUMASANGALALA NGATI TIMATSATIRA MALANGIZO A M’BAIBULO

NGATI MUKUDWALA

Malangizo a m’Baibulo: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa.”​Miyambo 17:22.

Mofanana ndi “mankhwala ochiritsa,” kukhala osangalala kungatithandize kupirira matenda. Koma kodi munthu angakhale bwanji wosangalala ngati akudwala?

Muzikhala ndi mtima woyamikira. Tikamangoganizira za mavuto athu, “masiku onse” akhoza kumangokhala oipa. (Miyambo 15:15) Koma Baibulo limatiuza kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.” (Akolose 3:15) Phunzirani kumayamikira pa zinthu zabwino, ngakhale zitakhala zing’onozing’ono. Zinthu monga kuona mmene kumwamba kumakongolera dzuwa likamalowa, kamphepo kayeziyezi komanso munthu amene timam’konda akatimwetulira, zimatithandiza kukhala osangalala.

Muzithandiza ena. Ngakhale zitakhala kuti tikudwala tizikumbukira kuti “kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Anthu ena akatiyamikira pa zimene tawachitira, timasangalala kwambiri ndipo zimenezi zimachititsa kuti tiiwaleko mavuto athu. Tikamathandiza ena kuti azisangalala nafenso timasangalala.

KULIMBITSA BANJA

Malangizo a m’Baibulo: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”​Afilipi 1:10.

Anthu okwatirana amene sakhala ndi nthawi yambiri yochitira zinthu limodzi akhoza kusokoneza banja lawo. Choncho mwamuna ndi mkazi angachite bwino kumaona kuti banja lawo ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri.

Muzichita zinthu limodzi. M’malo momangochita panokha zinthu zimene zimakusangalatsani, mungachite bwino kukonza zoti muzichitira limodzi zinthu. Baibulo limati: “Awiri amaposa mmodzi.” (Mlaliki 4:9) Mukhoza kumachitira limodzi zinthu monga kuphika chakudya, kuchita masewera olimbitsa thupi, kumwa zakumwa zoziziritsa kukhosi kapenanso kuchitira limodzi zinthu zina zimene mumakonda.

Muzisonyezana chikondi. Baibulo limati anthu okwatirana ayenera kumakondana komanso kulemekezana. (Aefeso 5:28, 33) Zinthu monga kumwetulirana mwachikondi, kukumbatirana kapenanso kupatsana timphatso zimalimbitsa banja. Komanso anthu okwatirana sayenera kusonyeza anthu ena chikondi chimene amafunika kusonyeza mwamuna kapena mkazi wawo yekha.​—Aheberi 13:4.