Zomwe Mungasankhe Zingakhudze Tsogolo Lanu
Zaka 3,500 zapitazo, Yehova Mulungu anauza atumiki ake zomwe angachite kuti akhale ndi tsogolo labwino. Iye anati: “Ndaika moyo ndi imfa, dalitso ndi temberero pamaso panu. Kumwamba ndi dziko lapansi ndi mboni pa zochita zanu. Choncho inuyo ndi mbadwa zanu musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.”—Deuteronomo 30:19.
Anthuwa ankafunika kusankha zinthu mwanzeru kuti akhale ndi tsogolo labwino. Ndi zimene nafenso tiyenera kuchita. Baibulo limafotokoza kuti zimenezi zingatheke “mwa kukonda Yehova Mulungu wanu [ndiponso] kumvera mawu ake.”—Deuteronomo 30:20.
KODI TINGAKONDE BWANJI YEHOVA NDIPONSO KUMVERA MAWU AKE?
MUZIPHUNZIRA BAIBULO: Kuti muzikonda Yehova, choyamba mukufunika kuphunzira za iye kuchokera m’Baibulo. Mukamatero mudzaona kuti Mulungu ndi wachikondi ndiponso kuti amakufunirani zabwino. Mulungu amafuna kuti muzipemphera kwa iye chifukwa “amakuderani nkhawa.” (1 Petulo 5:7) Baibulo limanena kuti mukamayesetsa kuyandikira Mulungu, “iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.
MUZICHITA ZIMENE MWAPHUNZIRA: Kumvera Mulungu kumatanthauza kutsatira malangizo ake anzeru omwe amapezeka m’Baibulo. Mukatero, ‘mudzakhala ndi moyo wopambana, ndipo mudzachita zinthu mwanzeru.’—Yoswa 1:8.
Mungachite bwino kwambiri kuyamba panopa kutsatira mfundo za m’Baibulo kuti mukhale ndi tsogolo labwino.