Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Kodi Baibulo lingakuthandizeni mukakhala ndi nkhawa?
Kodi mungayankhe bwanji?
Inde
Ayi
Mwina
Zimene Baibulo limanena
‘Muzimutulira [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’ (1 Petulo 5:7) Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu angatithandize tikakhala ndi nkhawa.
Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo
Mukapemphera, mungapeze “mtendere wa Mulungu” womwe ungakuthandizeni kuchepetsa nkhawa.—Afilipi 4:6, 7.
Kuwerenga Mawu a Mulungu kungakuthandizeni kuti mudziwe zoyenera kuchita mukakhala ndi nkhawa.—Mateyu 11:28-30.
Kodi zidzatheka anthufe kukhala opanda nkhawa?
Anthu ena amakhulupirira kuti . . . nkhawa ndi mbali imodzi ya moyo wa munthu, pomwe ena amakhulupirira kuti nkhawa zidzatha akadzamwalira n’kupita kumwamba. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?
Zimene Baibulo limanena
Mulungu analonjeza kuti adzachotsa zinthu zonse zomwe zimayambitsa nkhawa.—Chivumbulutso 21:4.
Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo
Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira padzikoli, anthu azidzakhala mwamtendere komanso mosangalala.—Yesaya 32:18.
Nkhawa zidzakhala mbiri yakale.—Yesaya 65:17.