Zomwe Yesu Ananena Zokhudza Kachilembo Kachiheberi Zimalimbitsa Chikhulupiriro Chathu
Kodi tingatsimikize bwanji kuti zinthu zonse zimene Mulungu analonjeza zidzachitikadi? Yesu sankakayikira kuti Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake onse. Pamene iye ankaphunzitsa anthu anawathandiza kuti nawonso akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Mwachitsanzo, taganizirani zimene ananena pa ulaliki wake wa paphiri, zomwe zimapezeka pa Mateyu 5:18. Iye anati: “Ndithu ndikukuuzani kuti kumwamba ndi dziko lapansi zingachoke mosavuta, kusiyana n’kuti kalemba kochepetsetsa kapena kachigawo kamodzi ka lemba kachoke m’Chilamulo zinthu zonse zisanachitike.”
Kachilembo kakang’ono pa afabeti yachiheberi ndi aka י (yod), ndipo ndi kachilembo koyamba pa zilembo zoimira dzina la Mulungu lakuti Yehova. * Ansembe ndi Afarisi ankaona kuti mawu komanso zilembo za m’Chilamulo cha Mulungu ndi zofunika kwambiri. Koma kuwonjezera pamenepo iwo ankaona kuti “kachigawo kamodzi ka lemba” n’kofunikanso kwambiri.
Yesu ananena kuti zingakhale zosavuta kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke kusiyana ndi kuti mawu a m’Chilamulo, ngakhale aang’ono kwambiri, asakwaniritsidwe. Koma Malemba amatitsimikizira kuti kumwamba kwenikweniku komanso dziko lapansili, zidzakhalapo mpaka kalekale. (Salimo 78:69) Choncho mawu a Yesuwa ndi amphamvu kwambiri ndipo ankatanthauza kuti chilichonse chimene chili m’Chilamulo, chidzakwaniritsidwa.
Kodi Yehova amaonetsetsa kuti zonse zomwe zili m’Mawu ake zakwaniritsidwa, ngakhale zinthu zing’onozing’ono? Inde. Taganizirani chitsanzo ichi: Aisiraeli akale anauzidwa kuti akamadya nyama ya mwana wa nkhosa pa Pasika, asamaphwanye mafupa. (Ekisodo 12:46) Tingati mfundo imeneyi inali ngati yaing’ono. Mwinanso Aisiraeli sankadziwa n’komwe chifukwa chimene Mulungu anawauzira kuti asamaphwanye fupa. Komatu Yehova ankadziwa kuti zimenezi zinali ulosi ndipo zinkaimira mfundo yoti palibe fupa la Mesiya, ngakhale limodzi, limene lidzathyoledwe Mesiyayo akadzapachikidwa.—Salimo 34:20; Yohane 19:31-33, 36.
Ndiye kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Yesu a pa Mateyu 5:18? Phunziro ndi lakuti ifenso tisamakayikire kuti zonse zimene Yehova walonjeza, ngakhale zinthu zing’onozing’ono, zidzakwaniritsidwa. Apatu taona kuti zimene Yesu ananena zokhudza kachilembo kakang’ono kachiheberi zimalimbitsa chikhulupiriro chathu.
^ ndime 3 Kachilembo kakang’ono ka afabeti yachigiriki ndi iota ndipo kayenera kuti kuchepa kwake n’kofanana ndi kachiheberi kaja י (yod). Popeza poyamba Chilamulo cha Mose chinalembedwa m’Chiheberi ndipo anthu ankachiwerenganso m’Chiheberi, apa Yesu ayenera kuti ankanena za kachilembo kachiheberi.