NKHANI YA PACHIKUTO | KODI NDI NDANI ANGATITHANDIZE TIKAKHALA PA MAVUTO?
Kodi Mulungu Amatilimbikitsa Bwanji?
Mtumwi Paulo ananena kuti Yehova * ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Apa Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu akhoza kuthandiza munthu aliyense ndipo angamulimbikitse akakumana ndi vuto lina lililonse.
Komabe pali zimene tiyenera kuchita kuti Mulungu azitilimbikitsa. Kodi dokotala angatithandize bwanji ngati titapanda kukonza zoti tionane naye? Mneneri Amosi anafunsa kuti: “Kodi anthu awiri amayenda pamodzi asanapangane ndi kukumana mogwirizana ndi pangano lawolo?” (Amosi 3:3) N’chifukwa chake Malemba amanena kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.
Kodi tikudziwa bwanji kuti Mulungu adzatiyandikiradi? Choyamba, tikudziwa chifukwa chakuti iye amatiuza mobwerezabwereza kuti amafuna kutithandiza. (Onani bokosi limene lili m’nkhaniyi.) Chachiwiri, tili ndi umboni wosonyeza kuti Mulungu ankathandiza anthu akale komanso akuthandizabe anthu masiku ano.
Mofanana ndi anthu ambiri amasiku ano amene amafuna kuti Mulungu awathandize, Davide ankakumana ndi mavuto ambiri. Nthawi ina iye anapempha Yehova kuti: “Imvani mawu anga ochonderera pamene ndikufuulira inu kuti mundithandize.” Kodi Mulungu anayankha pempheroli? Inde. Tikutero chifukwa Davide ananenanso kuti: “Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukukondwera.”—Salimo 28:2, 7.
YESU ANAPATSIDWA UDINDO WOLIMBIKITSA ONSE OLIRA
Mulungu anapatsa Yesu udindo woti azilimbikitsa anthu. Anamupatsa ntchito yoti ‘amange zilonda za anthu osweka mtima komanso kuti atonthoze anthu onse olira.’ (Yesaya 61:1, 2) Mogwirizana ndi ulosiwu, Yesu ankalimbikitsa kwambiri anthu “ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa.”—Mateyu 11:28-30.
Iye ankalimbikitsa anthu powapatsa malangizo anzeru, kuwachitira zinthu mokoma mtima komanso nthawi zina kuwachiritsa. Tsiku lina munthu wina wakhate anapempha Yesu kuti: “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.” Yesu atagwidwa ndi chifundo, anayankha kuti: “Ndikufuna. Khala woyera.” (Maliko 1:40, 41) Nthawi yomweyo munthuyo anachiritsidwa.
Panopa Mwana wa Mulungu sangatilimbikitse ngati mmene ankachitiramu chifukwa sali padziko lapansi 2 Akorinto 1:3) Tiyeni tione njira 4 zikuluzikulu zimene Mulungu amagwiritsa ntchito polimbikitsa anthu.
pano. Koma Atate wake Yehova yemwe ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse,” akupitirizabe kuthandiza anthu omwe ali ndi mavuto. (-
Baibulo. “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize. Malembawa amatipatsa chiyembekezo chifukwa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.”—Aroma 15:4.
-
Mzimu Woyera wa Mulungu. Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Yesu anamwalira, mpingo wachikhristu unalowa m’nyengo yamtendere. Zimenezi zinatheka chifukwa choti “unali kuyenda moopa Yehova ndiponso kulimbikitsidwa ndi mzimu woyera.” (Machitidwe 9:31) Mzimu woyera, kapena kuti mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito, ndi wamphamvu kwambiri. Mulungu angaugwiritse ntchito kuti alimbikitse munthu pa vuto lina lililonse.
-
Pemphero. Baibulo limatiuza kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse.” Ndipo “zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”—Afilipi 4:6, 7.
-
Akhristu Anzathu akhoza kutilimbikitsa kwambiri monga anzathu apamtima. Mtumwi Paulo ananena kuti anzake ‘ankamuthandiza ndi kumulimbikitsa’ pa nthawi imene anali “m’masautso.”—Akolose 4:11; 1 Atesalonika 3:7.
Koma mwina mukudzifunsa kuti, Kodi zinthu zimenezi zimathandizadi? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tionenso bwinobwino zitsanzo za anthu omwe tawatchula m’nkhani yapitayi. Mofanana ndi anthuwa, inunso mukhoza kuona umboni wakuti Mulungu amachitadi zimene analonjeza kuti: “Mofanana ndi munthu amene mayi ake amamutonthoza, inenso ndidzakutonthozani anthu inu.”—Yesaya 66:13.
^ ndime 3 Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.