Nkhani ya Davide ndi Goliyati—Kodi Inachitikadi?
Anthu ena amaganiza kuti nkhani ya Davide ndi Goliyati ndi nthano chabe. N’kutheka kuti inunso mukukayikira ngati nkhaniyi inachitikadi. Ngati zili choncho, mungachite bwino kuganizira mafunso atatu otsatirawa.
1 | Kodi n’zothekadi munthu kukhala wamtali mamita pafupifupi atatu?
Baibulo limanena kuti Goliyati anali “wamtali mikono 6 ndi chikhatho chimodzi.” (1 Samueli 17:4) Mkono umodzi unali masentimita 44.5, ndipo chikhatho chimodzi chinali masentimita 22.2. Choncho tinganene kuti Goliyati anali wamtali mamita 2.9. Anthu ena amatsutsa zoti Goliyati analidi wamtali chonchi. Komatu masiku ano palinso anthu ena aatali kwambiri. Mwachitsanzo, munthu wina anali wamtali mamita oposa 2.7. Ndiye kodi n’zosatheka kuti Goliyati anali wamtali kuposa munthuyu ndi masentimita pafupifupi 20 okha? Goliyati anali wochokera mu mtundu wa Arefai ndipo anthu ake ankakhala aatali kwambiri. Zolemba zina za ku Iguputo zomwe zinalembedwa m’zaka za m’ma 1200 B.C.E. zimanena kuti ku Kanani kunali asilikali ena oopsa omwe anali aatali mamita oposa 2.4. Choncho n’zotheka kuti Goliyati analidi wamtali pafupifupi mamita atatu.
2 | Kodi Davide analidi munthu weniweni?
M’mbuyomu akatswiri ena ankaona kuti nkhani ya Mfumu Davide ndi nthano chabe. Koma akatswiri ofukula zinthu zakale anapeza zolemba zakale zimene zimatchula za “nyumba ya Davide.” Komanso zimene Yesu Khristu ananena zimasonyeza kuti Davide anali munthu weniweni. (Mateyu 12:3; 22:43-45) M’Baibulo muli mndandanda wa makolo a Yesu womwe umapereka umboni woti Yesu analidi Mesiya ndipo mndandandawu umasonyeza kuti anali mdzukulu wa Mfumu Davide. (Mateyu 1:6-16; Luka 3:23-31) Izitu zikusonyeza kuti Davide anali munthu weniweni.
3 | Kodi malo otchulidwa m’nkhani ya Davide ndi Goliyati ndi enieni?
Baibulo limanena kuti nkhondo ya Afilisiti ndi Aisiraeli inachitikira m’chigwa cha Ela. Limafotokozanso kuti Afilisiti anasonkhana m’mbali mwa phiri pakati pa tauni ya Soko ndi ya Azeka. Limanenanso kuti Aisiraeli anaima m’mbali mwa phiri, kutsidya lina la chigwa. Kodi malo amenewa ndi enieni?
Munthu wina yemwe anapita posachedwapa kukaona malowa ananena kuti: “Munthu amene ankatitsogolera, yemwe sanali wachipembedzo, anapita nafe kuchigwa cha Ela. Tinadutsa m’kanjira kenakake mpaka kukafika pamwamba pa phiri linalake. Tili paphiripo, anatiuza kuti tiwerenge lemba la 1 Samueli 17:1-3. Titawerenga anatilozera kutsidya lina la chigwacho n’kunena kuti: ‘Mbali ya kumanzereko n’komwe kuli bwinja la tauni ya Soko.’ Kenako anatembenuka n’kutilozera kumanja n’kunena kuti: ‘Kumanjako n’kumene kuli bwinja la tauni ya Azeka. Afilisiti anasonkhana m’mapiri ali kutsogolo kwanuwo, pakati pa matauni awiriwa. Choncho zikuoneka kuti pamene taima pano m’pomwe Aisiraeli anasonkhana.’ Ndinachita chidwi kudziwa kuti mwina Sauli ndi Davide anaima pamalo amene ndinaimawo. Kenako tinatsika paphiripo n’kuwoloka kamtsinje kamuchigwacho komwe kanali ndi madzi ochepa ndipo munali miyala yambiri. Ndinkangokhala ngati ndikuona Davide akuwerama kuti atole miyala 5 yosalala ndipo umodzi wa miyalayo ndi umene anaphera Goliyati.” Mofanana ndi anthu ambiri, munthu wokaona maloyu anachita chidwi kwambiri ndi mmene Baibulo limafotokozera zinthu molondola.
Choncho palibe chifukwa choti tizikayikira zimene Baibulo limanena pa nkhani ya Davide ndi Goliyati. Tikutero chifukwa anthu ndiponso malo otchulidwa m’nkhaniyi ndi enieni. Ndipo chifukwa chachikulu chokhulupirira nkhaniyi n’chakuti imapezeka m’Mawu a Mulungu, yemwe “sanganame.”—Tito 1:2; 2 Timoteyo 3:16.