NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUDZIWA ZAMBIRI ZOKHUDZA ANGELO?
Kodi Angelo Angakuthandizeni Bwanji?
Angelo okhulupirika amachita chidwi ndi anthu ndipo amachita zofuna za Yehova. Mwachitsanzo, Mulungu atalenga dziko lapansili, angelo ‘anafuula pamodzi mokondwera, ndipo ana onse a Mulungu anayamba kufuula ndi chisangalalo.’ (Yobu 38:4, 7) Kuyambira kale angelo akhala akufunitsitsa ‘kusuzumira’ kuti adziwe kukwaniritsidwa kwa maulosi okhudza zochitika za padzikoli.—1 Petulo 1:11, 12.
Baibulo limasonyeza kuti nthawi zina angelo amateteza anthu okhulupirika pofuna kukwaniritsa cholinga cha Mulungu. (Salimo 34:7) Mwachitsanzo:
-
Pamene Yehova ankawononga anthu oipa m’mizinda ya Sodomu ndi Gomora, angelo anathandiza Loti ndi banja lake kuti athawe.—Genesis 19:1, 15-26.
-
Anyamata atatu achiheberi ataponyedwa m’ng’anjo ya moto ku Babulo, Mulungu “anatumiza mngelo wake” kuti akawapulumutse.—Danieli 3:19-28.
-
Danieli, yemwe anali munthu wokhulupirika, atakhala m’dzenje la mikango usiku wonse, ananena kuti mikangoyo sinamudye chifukwa Mulungu anatumiza “mngelo wake kudzatseka pakamwa pa mikango.”—Danieli 6:16, 22.
ANGELO ANKATHANDIZA MPINGO WACHIKHRISTU M’NTHAWI YA ATUMWI
Nthawi zina angelo ankathandiza Akhristu oyambirira kuti akwaniritse cholinga cha Yehova. Mwachitsanzo:
-
Mngelo anatsegula zitseko za ndende ndipo anathandiza atumwi kuti atuluke m’ndendemo n’kukapitiriza kulalikira m’kachisi.—Machitidwe 5:17-21.
-
Mngelo anauza Filipo kuti adutse msewu wa m’chipululu womwe unkachokera ku Yerusalemu kupita ku Gaza. Anamuuza zimenezi n’cholinga choti akalalikire kwa munthu wina wa ku Itiyopiya yemwe ankachokera kolambira Mulungu ku Yerusalemu.—Machitidwe 8:26-33.
-
Nthawi ya Mulungu itakwana yoti anthu omwe sanali Ayuda akhale Akhristu, mngelo anaonekera kwa Koneliyo, yemwe anali mkulu wa gulu la asilikali achiroma. Anamuuza kuti atume anthu kuti akaitane mtumwi Petulo.—Machitidwe 10:3-5.
-
Mtumwi Petulo ali m’ndende, mngelo anapita kukamutulutsa.—Machitidwe 12:1-11.
KODI ANGELO ANGAKUTHANDIZENI BWANJI?
Palibe umboni wakuti masiku ano Mulungu akugwiritsa ntchito angelo kuthandiza anthu mozizwitsa ngati mmene ankachitira kale. Komabe ponena za nthawi yathu ino Yesu anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Kodi mukudziwa kuti otsatira a Khristu akugwira ntchito imeneyi mothandizidwa ndi angelo?
Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti angelo akuthandiza anthu padziko lonse kuphunzira za Yehova Mulungu komanso cholinga chake polenga anthu. Mtumwi Yohane anati: “Ndinaona mngelo winanso akuuluka chapafupi m’mlengalenga. Iye anali ndi uthenga wabwino wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa anthu okhala padziko lapansi, ndi kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse. Iye anali kunena mofuula kuti: ‘Opani Mulungu ndi kumupatsa ulemerero, chifukwa ola lakuti apereke chiweruzo lafika. Chotero lambirani Iye amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe amadzi.’” (Chivumbulutso 14:6, 7) Pali zitsanzo zambiri zosonyeza kuti angelo akuthandiza pa ntchito yolalikira za Ufumu yomwe ikuchitika padziko lonse. Ndiponso munthu mmodzi wochimwa akalapa n’kubwerera kwa Yehova, “kumakhala chisangalalo chochuluka kwa angelo a Mulungu.”—Luka 15:10.
Kodi chidzachitike n’chiyani ntchito yolalikira ikadzatha? Angelo, omwe ndi ‘magulu ankhondo akumwamba,’ adzathandiza Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu ya mafumu, kumenya nkhondo ya “tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” pa Aramagedo. (Chivumbulutso 16:14-16; 19:14-16) Angelo amphamvu adzagwira ntchito yopereka chiweruzo cha Mulungu pamene Ambuye Yesu “adzabwezera chilango kwa anthu . . . osamvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.”—2 Atesalonika 1:7, 8.
Musamakayikire kuti angelo amakufunirani zabwino. Amafunitsitsa kuthandiza anthu amene akufuna kutumikira Mulungu. Ndipotu Yehova wakhala akugwiritsa ntchito angelo kulimbikitsa komanso kuteteza atumiki ake okhulupirika padzikoli.—Aheberi 1:14.
Choncho aliyense ayenera kusankha kumvera uthenga wabwino umene ukulalikidwa padziko lonse kapena ayi. A Mboni za Yehova angakuthandizeni kuti inunso mupindule ndi ntchito imene angelo a Mulungu amphamvu akugwira.