Choonadi Chonena za Ufumu wa Mulungu
Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani? Kodi Ufumuwu ukuchita chiyani panopa? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuupempherera kuti ubwere?
Yesu ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.
Luka 1:31-33: “Udzam’patse dzina lakuti Yesu. Ameneyu adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake. Iye adzalamulira monga mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya, moti ufumu wake sudzatha.”
Mfundo yaikulu ya zimene Yesu ankalalikira inali Ufumu wa Mulungu.
Mateyu 9:35: “Yesu anayamba ulendo woyendera mizinda ndi midzi yonse. Anali kuphunzitsa m’masunagoge awo, kulalikira uthenga wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda amtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse.”
Yesu anapatsa ophunzira ake chizindikiro chimene chingawathandize kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kubwera.
Mateyu 24:7: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana.”
Panopa otsatira a Yesu akulalikira za Ufumu padziko lonse.
Mateyu 24:14: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”