Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 41

NYIMBO NA. 13 Titsanzire Yesu

Zimene Tikuphunzira kwa Yesu pa Masiku Ake 40 Omaliza

Zimene Tikuphunzira kwa Yesu pa Masiku Ake 40 Omaliza

“Iwo anamuona masiku onse 40 ndipo ankawauza za Ufumu wa Mulungu.”—MAC. 1:3.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tikambirana zimene tikuphunzira pa zimene Yesu anachita m’masiku 40 omaliza a moyo wake padzikoli.

1-2. Kodi n’chiyani chomwe chinachitika ophunzira a Yesu akuyenda pamsewu wopita ku Emau?

 PA NISANI 16 mu 33 C.E., ophunzira a Yesu anali ndi chisoni komanso mantha. Ophunzira awiri anachoka ku Yerusalemu kupita ku Emau, mudzi womwe unali pa mtunda wa makilomita 11. Amunawo anali okhumudwa kwambiri chifukwa Yesu yemwe ankamutsatira anali atangophedwa kumene. Zinkangooneka ngati zimene ankayembekezera zoti Mesiya angachite zalephereka. Koma kenako panachitika zinthu zina zodabwitsa.

2 Munthu wina anayamba kuyenda nawo limodzi mumsewu. Iwo anamufotokozera zinthu zokhumudwitsa zimene zinachitikira Yesu. Munthuyo anayamba kukambirana nawo zinthu zimene sakanadzaiwala. Iye anawafotokozera chifukwa chake Yesu ankayenera kuvutika komanso kufa pogwiritsa ntchito “zolemba za Mose komanso zonse zimene aneneri analemba.” Atafika ku Emau, munthuyo anadziulula kuti anali Yesu ndipo anali ataukitsidwa. N’zoonekeratu kuti ophunzira anasangalala kwambiri kudziwa kuti Mesiya ali moyo.—Luka 24:​13-35.

3-4. Kodi n’chiyani chomwe chinachitikira ophunzira a Yesu, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi? (Machitidwe 1:3)

3 Pa masiku 40 omaliza a moyo wake padzikoli, Yesu anaonekera maulendo angapo kwa ophunzira ake. (Werengani Machitidwe 1:3.) Pa nthawiyi, ophunzira a Yesu omwe anali achisoni komanso amantha, anasintha n’kuyamba kusangalala komanso kukhala olimba mtima ndipo ankalalikira komanso kuphunzitsa anthu zokhudza Ufumu wa Mulungu. a

4 Kuphunzira zimene Yesu anachita pa masiku 40 amenewa kungatithandize kwambiri. Munkhaniyi tiona mmene Yesu anagwiritsira ntchito nthawi imeneyi (1) polimbikitsa ophunzira ake, (2) powathandiza kumvetsa Malemba komanso (3) powakonzekeretsa kudzakhala ndi maudindo akuluakulu. Tionanso mmene tingatsanzirire Yesu pa mbali zitatuzi.

MUZILIMBIKITSA ENA

5. N’chifukwa chiyani ophunzira a Yesu ankafunika kulimbikitsidwa?

5 N’chifukwa chiyani ophunzira a Yesu ankafunika kulimbikitsidwa? Ena anasiya nyumba, mabanja komanso mabizinezi awo n’cholinga choti azitsatira Yesu. (Mat. 19:27) Pomwe enanso ankazunzidwa chifukwa chokhala ophunzira ake. (Yoh. 9:22) Iwo analolera kusintha moyo wawo komanso kuvutika chifukwa ankakhulupirira kuti Yesu ndi Mesiya wolonjezedwa. (Mat. 16:16) Koma Yesu ataphedwa, iwo anakhumudwa chifukwa choona kuti zimene ankayembekezera zalephereka.

6. Kodi Yesu anachita chiyani ataukitsidwa?

6 Yesu ankaona kuti zinali zomveka kuti ophunzira ake akhale ndi chisoni ndipo sunali umboni wakuti anali ofooka mwauzimu. Choncho tsiku limene anaukitsidwa anayamba kulimbikitsa anzakewo. Mwachitsanzo, iye anaonekera kwa Mariya wa ku Magadala pomwe ankalira pamanda ake. (Yoh. 20:​11, 16) Anaonekeranso kwa ophunzira awiri omwe tawatchula kumayambiriro aja. Komanso anaonekera kwa mtumwi Petulo. (Luka 24:34) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu anachita? Tiyeni tione zimene zinachitika ataonekera kwa Mariya wa ku Magadala.

7. Mogwirizana ndi Yohane 20:​11-16, kodi Yesu anaona Mariya akuchita chiyani m’mawa wa pa Nisani 16, nanga izi zinamulimbikitsa kuchita chiyani? (Onaninso chithunzi.)

7 Werengani Yohane 20:​11-16. M’mawa pa Nisani 16, amayi ena okhulupirika anapita kumanda a Yesu. (Luka 24:​1, 10) Tiyeni tione zimene zinachitikira mmodzi wa amayiwa dzina lake Mariya wa ku Magadala. Mariya atafika anapeza kuti m’mandamo munalibe kanthu. Iye anathamanga kukauza Petulo ndi Yohane ndipo anawalondola pomwe iwo ankapita kumandako. Petulo ndi Yohane atatsimikizira kuti m’mandamo mulibe kanthu anabwerera kunyumba, koma Mariya anatsala komweko n’kumalira. Iye sankadziwa kuti Yesu akumuona. Yesu anakhudzidwa kwambiri ataona mayi wokhulupirikayo akulira. Choncho anaonekera kwa Mariya ndipo anachita chinthu china chomwe chinamulimbikitsa kwambiri. Yesu analankhula naye ndipo anamutuma kuti akauze abale ake kuti iye waukitsidwa.—Yoh. 20:​17, 18.

Muzitsanzira Yesu pochita chidwi ndi ena komanso kulimbikitsa amene akhumudwa (Onani ndime 7)


8. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu?

8 Kodi ifeyo tingatsanzire bwanji Yesu? Mofanana ndi Yesu, tikaona abale ndi alongo athu ali ndi nkhawa tizilankhula nawo mokoma mtima. Zimenezi zingawathandize kuti apitirize kutumikira Yehova. Chitsanzo ndi zimene zinachitikira Mlongo Jocelyn yemwe mchemwali wake anafa pa ngozi. Iye anati: “Ndinali ndi chisoni kwa miyezi yambiri.” Koma m’bale wina ndi mkazi wake anamuitanira kunyumba kwawo. Anamumvetsera mwachifundo komanso kumutsimikizira kuti Mulungu amamuona kuti ndi wamtengo wapatali. Jocelyn ananenanso kuti: “Ndinkangomva ngati Yehova wawagwiritsa ntchito kuti andivuule m’nyanja yowinduka n’kundipititsa m’boti. Iwo anandithandiza kuti ndiyambirenso kutumikira Yehova mosangalala.” Ifenso tingalimbikitse ena powamvetsera mwachifundo akamafotokoza nkhawa zawo komanso kuwalankhula mokoma mtima. Tikatero tidzawathandiza kuti apitirize kutumikira Mulungu.—Aroma 12:15

MUZITHANDIZA ENA KUMVETSA MALEMBA

9. Kodi ophunzira a Yesu anali ndi vuto liti, nanga iye anawathandiza bwanji?

9 Ophunzira a Yesu ankadziwa Mawu a Mulungu ndipo ankawatsatira pa moyo wawo. (Yoh. 17:6) Komabe iwo anasokonezeka pomwe iye anaphedwa ngati chigawenga pamtengo wozunzikirapo. Yesu anazindikira kuti iwo ankakayikira chifukwa chakuti sankamvetsa zinthu, osati chifukwa chakuti anali ndi mtima woipa. (Luka 9:​44, 45; Yoh. 20:9) Choncho iye anawathandiza kumvetsa Malemba. Tiyeni tikambirane mmene anachitira zimenezi kwa ophunzira awiri omwe ankapita ku Emau.

10. Kodi Yesu anawathandiza bwanji ophunzira ake kutsimikizira kuti iye analidi Mesiya? (Luka 24:​18-27)

10 Werengani Luka 24:​18-27. Onani kuti pocheza nawo sanangofikira kuwauza kuti iye waukitsidwa. M’malomwake, anayamba ndi kuwafunsa mafunso. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? N’kutheka kuti iye ankafuna kuti afotokoze zimene zinali m’maganizo ndi mumtima mwawo, ndipo iwo anafotokozadi. Iwo anamufotokozera kuti ankayembekezera kuti Yesu apulumutsa Aisiraeli ku ulamuliro wopondereza wa Aroma. Atafotokoza momveka bwino zimene zinkawadetsa nkhawa, Yesu anagwiritsa ntchito Malemba powathandiza kumvetsa zimene zinachitika. b Madzulo a tsiku limenelo, Yesu anathandizanso ophunzira ena kumvetsa mfundo zimenezi. (Luka 24:​33-48) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi?

11-12. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa njira imene Yesu anagwiritsa ntchito? (Onaninso zithunzi.) (b) Kodi m’bale amene ankaphunzitsa Nortey Baibulo anamuthandiza bwanji?

11 Kodi tingatsanzire bwanji Yesu? Choyamba, mukamaphunzira Baibulo ndi munthu muzigwiritsa ntchito mafunso pomuthandiza kufotokoza zimene zili mumtima mwake ndi m’maganizo ake. (Miy. 20:5) Mukamvetsa zimene zili mumtima mwake, muzimusonyeza mmene angapezere malemba omwe angamuthandize. Muzipewa kumuuza zochita. M’malomwake, muzimuthandiza kumvetsa Malemba komanso kumuthandiza kuganizira mmene mfundo za m’Baibulo zingamuthandizire pa moyo wake. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina wa ku Ghana dzina lake Nortey.

12 Nortey anayamba kuphunzira Baibulo ali ndi zaka 16. Pasanapite nthawi yaitali anthu a m’banja lake anayamba kumutsutsa. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti asafooke? Mphunzitsi wake anagwiritsa ntchito lemba la Mateyu chaputala 10 pomufotokozera kuti Akhristu oona adzazunzidwa. Nortey anati: “Choncho anthu atayamba kundizunza ndinazindikira kuti ndapeza choonadi.” Mphunzitsi wake anakambirana naye lemba la Mateyu 10:16 pomuthandiza kuti azikhala wosamala komanso waulemu akamakambirana nkhani za chipembedzo ndi anthu a m’banja lake. Nortey atabatizidwa ankafuna kuyamba upainiya koma bambo ake ankafuna kuti iye apite kuyunivesite. M’malo momuuza zochita, mphunzitsi wake anagwiritsa ntchito mafunso pomuthandiza kuti azigwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba. Zotsatira zake n’zakuti Nortey anayamba utumiki wa nthawi zonse. Zitatero bambo ake anamuthamangitsa pakhomo. Kodi Nortey amamva bwanji akaganizira zimene zinachitikazi? Iye anati: “Sindimakayikira kuti ndinasankha bwino.” Ifenso tikamathandiza ena kuti aziganizira mfundo za m’Malemba tingawathandize kuti apitirize kutumikira Yehova.—Aef. 3:​16-19.

Muzitsanzira Yesu pothandiza ena kumvetsa Malemba (Onani ndime 11) e


MUZITHANDIZA AMUNA KUTI AKHALE “MPHATSO”

13. Kodi Yesu anatani kuti ntchito yolalikira ipitirizebe iye akabwerera kumwamba? (Aefeso 4:8)

13 Ali padzikoli Yesu anagwira bwino ntchito imene Atate wake anamupatsa. (Yoh. 17:4) Koma Yesu analibe maganizo akuti, ‘Zinthu zingayende bwino ngati nditamachita ndekha.’ Pa utumiki wake womwe anauchita zaka zitatu ndi hafu, anaphunzitsa ena kuti azigwira bwino ntchitoyi. Asanapite kumwamba Yesu anapatsa ophunzira ake ntchito yosamalira nkhosa za Mulungu komanso kutsogolera pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. N’kutheka kuti ena mwa ophunzirawa anali ndi zaka za m’ma 20. (Werengani Aefeso 4:8.) Ophunzira a Yesu anali odzipereka, okhulupirika komanso akhama. Ndiye kodi Yesu anagwiritsa ntchito bwanji masiku 40 omaliza a moyo wake powathandiza kuti akhale “mphatso?”

14. Pa masiku 40 omaliza a moyo wake, kodi Yesu anathandiza bwanji ophunzira ake kuti akule mwauzimu? (Onaninso chithunzi.)

14 Yesu anapereka malangizo kwa ophunzira ake mosapita m’mbali koma mokoma mtima. Mwachitsanzo, iye anazindikira kuti ena ankakayikira zinthu zina ndipo anawadzudzula. (Luka 24:​25-27; Yoh. 20:27) Iye anawathandizanso kuti aziona ntchito yolalikira kukhala yofunika kwambiri kuposa ntchito zina. (Yoh. 21:15) Anawathandizanso kuti asamaganizire kwambiri mwayi wa utumiki umene ena apatsidwa m’gulu la Yehova. (Yoh. 21:​20-22) Anawathandizanso kukonza maganizo olakwika omwe anali nawo okhudza Ufumu ndipo anawalimbikitsa kuti aziganizira kwambiri zolalikira uthenga wa Ufumu. (Mac. 1:​6-8) Kodi akulu angaphunzire chiyani kwa Yesu?

Muzitsanzira Yesu pothandiza amuna kuti adzakhale ndi maudindo (Onani ndime 14)


15-16. (a) Kodi akulu angatsanzire Yesu m’njira ziti? Fotokozani (b) Kodi Patrick anapindula bwanji chifukwa chotsatira malangizo?

15 Kodi akulu angatsanzire bwanji Yesu? Iwo ayenera kuphunzitsa amuna kuphatikizapo achinyamata kuti adzakhale ndi maudindo aakulu. c Akulu samayembekezera kuti amene akuwaphunzitsawo sazilakwitsa kalikonse. Iwo ayenera kupereka malangizo kwa achinyamata kuti adziwe zambiri, akhale odzichepetsa, okhulupirika komanso ofunitsitsa kutumikira ena.—1 Tim. 3:1; 2 Tim. 2:2; 1 Pet. 5:5.

16 M’bale wina dzina lake Patrick anapindula kwambiri chifukwa chotsatira malangizo. Ali wachinyamata iye sankalankhula bwino kapena kuchita zinthu mokoma mtima pochita zinthu ndi anthu ena ngakhalenso alongo. Mkulu wina anazindikira vuto la Patrick ndipo anamupatsa malangizo mosapita m’mbali koma mokoma mtima. Patrick anati: “Ndikuyamikira kuti anandipatsa malangizo. Ndinkakhumudwa ndikaona abale ena akupatsidwa utumiki umene ine ndinkaufuna. Koma malangizo amene mkuluyo anandipatsa anandithandiza kuti ndiziganizira kwambiri zotumikira abale ndi alongo anga, osati zolandira udindo wina wake mumpingo.” Zotsatira zake n’zakuti Patrick anaikidwa kukhala mkulu ali ndi zaka za m’ma 20.—Miy. 27:9.

17. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira ophunzira ake?

17 Yesu anapatsa ophunzira ake ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. Ophunzirawo ayenera kuti ankaona kuti sangakwanitse kugwira ntchitoyo. Koma Yesu sankakayikira kuti iwo akwanitsa ndipo anawauza zimenezo. Yesu anasonyeza kuti amawakhulupirira kwambiri powauza kuti: “Mofanana ndi mmene Atate ananditumira, inenso ndikukutumani.”—Yoh. 20:21.

18. Kodi akulu angatsanzire bwanji Yesu?

18 Kodi akulu angatsanzire bwanji Yesu? Akulu amene amadziwa zambiri amapatsa ena zochita. (Afil. 2:​19-22) Mwachitsanzo, akulu angapemphe achinyamata kuti athandize pa ntchito yokonza ndi kusamalira Nyumba ya Ufumu. Akamapatsa ena zochita amasonyeza kuti amawadalira powaphunzitsa n’kumakhulupirira kuti agwira bwinobwino ntchitoyo. Mathew, yemwe wangokhala kumene mkulu, ananena kuti amayamikira ngati akulu ena amuphunzitsa ntchito n’kumakhulupirira kuti aigwira bwinobwino. Iye anati: “Ndikalakwitsa zinthu ndimayamikira ngati iwo amaona zimenezo ngati mbali ya kuphunzira n’kundithandiza kuti ndizichita bwino.” d

19. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?

19 Yesu anagwiritsa ntchito masiku 40 omaliza a moyo wake padzikoli kuti alimbikitse komanso kuphunzitsa ena. Ifenso tiyenera kutsatira chitsanzo chake mosamala. (1 Pet. 2:21) Iye adzatithandiza kuchita zimenezi. Paja analonjeza kuti: “Ine ndili limodzi ndi inu masiku onse mpaka mʼnyengo ya mapeto a nthawi ino.”—Mat. 28:20.

NYIMBO NA. 15 Tamandani Mwana Woyamba Kubadwa wa Yehova

a Mabuku a Uthenga Wabwino komanso mabuku ena a m’Baibulo amafotokoza nthawi zingapo pomwe Yesu yemwe anali ataukitsidwa anaonekera kwa anthu monga Mariya wa ku Magadala (Yoh. 20:​11-18); amayi ena (Mat. 28:​8-10; Luka 24:​8-11); ophunzira awiri (Luka 24:​13-15); kwa Petulo (Luka 24:34); ophunzira onse kupatulapo Tomasi (Yoh. 20:​19-24); ophunzira onse kuphatikizapo Tomasi (Yoh. 20:26); ophunzira 7 (Yoh. 21:​1, 2); ophunzira oposa 500 (Mat. 28:16; 1 Akor. 15:6); m’bale wake Yakobo (1 Akor. 15:7); atumwi onse (Mac. 1:4); komanso kwa atumwi pafupi ndi ku Betaniya. (Luka 24:​50-52) N’kuthekanso kuti pali maulendo ena omwe anaonekera koma sanalembedwe.—Yoh. 21:25.

b Kuti muone maulosi okhudza Mesiya, onani pa jw.org nkhani yakuti, “Kodi Maulosi Onena za Mesiya Amatsimikizira Kuti Yesu Analidi Mesiya?

c Nthawi zina amuna a zaka za pakati pa 25 ndi 30 amaikidwa kukhala oyang’anira dera. Koma amayenera kukhala oti akudziwa zambiri ndipo atumikirapo ngati akulu.

d Kuti mupeze njira zina zothandizira achinyamata kuti adzakhale ndi maudindo, onani Nsanja ya Olonda ya August 2018 tsamba 11-12, ndime 15-17, komanso ya April 15, 2015, tsamba 3-13.

e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pambuyo pothandizidwa kumvetsa bwino Malemba, wophunzira Baibulo akutaya maluwa okhudzana ndi khirisimasi.