Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumatsanzira Yehova pa Nkhani ya Chilungamo?

Kodi Mumatsanzira Yehova pa Nkhani ya Chilungamo?

Ndidzalengeza dzina la Yehova. . . . Mulungu wokhulupirika, amene sachita chosalungama.”​DEUT. 32:3, 4.

NYIMBO: 110, 2

1, 2. (a) Fotokozani zinthu zopanda chilungamo zimene zinachitikira Naboti ndi ana ake. (b) Kodi tikambirana makhalidwe awiri ati m’nkhaniyi?

BAMBO wina ananamiziridwa kuti wapalamula mlandu waukulu. Achibale ake komanso anzake anadabwa kuona kuti bamboyo waweruzidwa kuti aphedwe ngakhale kuti anthu amene anapereka umboni anali osadalirika. Anthu okonda chilungamo zinawapweteka kwambiri kuona bambo wosalakwayo limodzi ndi ana ake aamuna akuphedwa. Zimene tafotokozazi zinachitikira mtumiki wa Yehova wokhulupirika dzina lake Naboti. Iye anaphedwa limodzi ndi ana ake mu ulamuliro wa Mfumu Ahabu ya Isiraeli.​—1 Maf. 21:11-13; 2 Maf. 9:26.

2 M’nkhaniyi tikambirana za Naboti komanso za mtumwi wina amene anali mkulu wokhulupirika mumpingo. Nkhani za anthu awiriwa zikusonyeza kuti kudzichepetsa n’kofunika kwambiri ngati tikufuna kutsanzira Mulungu pa nkhani ya chilungamo. Zikusonyezanso kuti tingatsanzire Yehova pa nkhaniyi ngati timakhululukira anthu amene tikuganiza kuti sanachite chilungamo.

ANACHITIRIDWA ZINTHU ZOPANDA CHILUNGAMO

3, 4. Kodi Naboti anali munthu wotani, nanga n’chifukwa chiyani anakana kugulitsa munda wake kwa Mfumu Ahabu?

3 Naboti anali wokhulupirika kwa Yehova pa nthawi imene Aisiraeli ambiri ankatsatira chitsanzo choipa cha Mfumu Ahabu ndi mkazi wake Yezebeli. Ahabu ndi mkazi wake ankalambira Baala ndipo sankatsatira mfundo za Yehova. Koma Naboti ankaona kuti ubwenzi wake ndi Yehova ndi wofunika kwambiri kuposa chilichonse, ngakhale moyo wake.

4 Werengani 1 Mafumu 21:1-3. Pa nthawi ina Ahabu anauza Naboti kuti amugulitse munda wake wa mpesa kapena asinthane ndi wina. Koma Naboti anakana. Kodi n’chifukwa chiyani anakana? Naboti anayankha mwaulemu kuti: “Sindingachite zimenezo pamaso pa Yehova, kupereka cholowa cha makolo anga kwa inuyo.” Naboti anakana zimene Ahabu ankafunazo chifukwa choti ankatsatira lamulo limene Mulungu anapatsa Aisiraeli. Lamulo lake linali lakuti munthu asamagulitse mpaka kalekale cholowa cha fuko lawo. (Lev. 25:23; Num. 36:7) Izi zikusonyeza kuti Naboti anali ndi maganizo a Yehova pa nkhaniyi.

5. Kodi Yezebeli anachita chiyani kuti mwamuna wake atenge munda wa Naboti?

5 Naboti atakana kugulitsa munda wake, Mfumu Ahabu ndi mkazi wake anachita zinthu zoipa kwambiri. Yezebeli ankafunitsitsa kuti mwamuna wake atenge mundawo, choncho anakonza chiwembu choti Naboti anamiziridwe mlandu waukulu, moti iye limodzi ndi ana ake anaphedwa. Koma kodi Yehova anatani ndi zinthu zopanda chilungamo zimene zinachitikazi?

MULUNGU ANAWERUZA AHABU MWACHILUNGAMO

6, 7. (a) Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti amakonda chilungamo? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene Yehova anachita zinali zolimbikitsa kwa achibale ndi anzake a Naboti?

6 Nthawi yomweyo Yehova anatumiza Eliya kwa Ahabu. Eliya anauza Ahabu kuti anali ndi mlandu wakupha komanso wakuba. Ndiye kodi Yehova anapereka chiweruzo chotani? Anati Ahabu, mkazi wake komanso ana ake nawonso adzaphedwa.​—1 Maf. 21:17-25.

7 Achibale ndi anzake a Naboti anamva chisoni kwambiri chifukwa cha zimene Ahabu anachita. Komabe ayenera kuti analimbikitsidwa atadziwa kuti Yehova anaona zonsezo ndipo anaweruza mwachilungamo. Koma kenako panachitika zinthu zina zimene zikanawalepheretsa kukhalabe odzichepetsa komanso okhulupirika kwa Yehova.

8. Kodi Ahabu anatani atamva za chiweruzo cha Yehova, nanga zotsatira zake zinali zotani?

8 Ahabu atamva za chiweruzo cha Yehova, “anang’amba zovala zake n’kuvala chiguduli. Iye anayamba kusala kudya, kugona pachiguduli ndipo anali kuyenda mwachisoni.” Apatu Ahabu anadzichepetsa kwambiri. Ndiye kodi Yehova anatani? Anauza Eliya kuti: ‘Popeza Ahabu wadzichepetsa chifukwa cha ine, sindidzabweretsa tsokali m’masiku ake. M’malomwake, ndidzalibweretsa panyumba yake m’masiku a mwana wake.’ (1 Maf. 21:27-29; 2 Maf. 10:10, 11, 17) Paja Yehova “amayesa mitima” ndipo apa anasonyeza chifundo kwa Ahabu.​—Miy. 17:3.

KODI KUDZICHEPETSA KUNGATITHANDIZE BWANJI?

9. Kodi kudzichepetsa kukanathandiza bwanji achibale komanso anzake a Naboti?

9 Achibale komanso anzake a Naboti atamva kuti Mulungu sapereka chilango ku banja la Ahabu mpaka Ahabuyo adzamwalire, ziyenera kuti zinawavuta kumvetsa. Koma kudzichepetsa ndi komwe kukanawathandiza kuti akhalebe okhulupirika kwa Yehova podziwa kuti iye sangachite zinthu zopanda chilungamo. (Werengani Deuteronomo 32:3, 4.) Yehova adzaukitsa Naboti ndi ana ake ndipo iwo ndi achibale awo adzasangalala kuona kuti Yehova ndi wachilungamo. (Yobu 14:14, 15; Yoh. 5:28, 29) Komanso munthu wodzichepetsa amakumbukira kuti “Mulungu woona adzaweruza ntchito iliyonse ndiponso chinthu chilichonse chobisika, kuti aone ngati zili zabwino kapena zoipa.” (Mlal. 12:14) Izi zikusonyeza kuti Yehova akamapereka chiweruzo amaganizira mfundo zonse ndipo zina zimakhala zoti ifeyo sitikuzidziwa. Choncho kudzichepetsa kungatithandize kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova.

10, 11. (a) Tchulani zinthu zina zimene zingachititse kuti tiziona ngati sipanachitike chilungamo. (b) Kodi kudzichepetsa kungatithandize bwanji?

10 Ndiye kodi inuyo mumatani ngati simukumvetsa kapena simukugwirizana ndi zimene akulu asankha? Mwachitsanzo, mumatani ngati mukuona kuti akulu sanachite bwino posonyeza chifundo kwa munthu amene anachita tchimo? Kodi mungatani ngati inuyo kapena mnzanu wachotsedwa pa udindo? Nanga mungatani ngati mkazi kapena mwamuna wanu, mnzanu kapenanso mwana wanu wachotsedwa mumpingo koma simukugwirizana nazo? Kupanda kusamala zinthu ngati zimenezi zingalepheretse munthu kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake. Ndiye kodi kudzichepetsa kungatithandize bwanji? Taganizirani njira ziwiri zotsatirazi.

Kodi mungatani akulu akalengeza zinthu zimene simukugwirizana nazo? (Onani ndime 10 ndi 11)

11 Choyamba, kudzichepetsa kungatithandize kuvomereza kuti pakachitika nkhani sitingadziwe zonse. Kaya pangakhale zina zimene tikudziwa, koma tisaiwale kuti Yehova yekha ndi amene amaona mmene mtima ulili. (1 Sam. 16:7) Kudziwa mfundo imeneyi kungachititse kuti tiziona zinthu moyenera. Chachiwiri, kudzichepetsa kungatithandizenso kuti tizikhala ogonjera komanso oleza mtima n’kumadikira kuti Yehova akonze zinthu. Baibulo limati: “Anthu amene amaopa Mulungu woona zidzawayendera bwino . . .  Koma woipayo sizidzamuyendera bwino n’komwe, ndiponso sadzachulukitsa masiku ake.” (Mlal. 8:12, 13) Tikakhala odzichepetsa zimatithandiza ifeyo komanso aliyense amene akukhudzidwa ndi nkhaniyo.​—Werengani 1 Petulo 5:5.

ANACHITA ZINTHU MWACHINYENGO

12. Kodi tikambirana nkhani iti ndipo itithandiza bwanji?

12 Ku Antiokeya wa ku Siriya kunachitikanso nkhani ina yovuta. Kuwonjezera pa kudzichepetsa, Akhristu a kumeneko anafunika kusonyezanso mtima wokhululuka. Tiyeni tikambirane nkhani imene inachitikayo n’kuona mmene ingatithandizire kukhala okhululuka. Nkhaniyi ikusonyezanso kuti Yehova akhoza kugwiritsa ntchito anthu omwe si angwiro popanda kuphwanya mfundo zake.

13, 14. Kodi Petulo anali ndi mwayi wochita zinthu ziti, ndipo anasonyeza bwanji kulimba mtima?

13 Mtumwi Petulo anali mkulu wodziwika bwino mumpingo. Iye anali mnzake wa Yesu ndipo anapatsidwa maudindo apadera. (Mat. 16:19) Mwachitsanzo, mu 36 C.E. iye analalikira uthenga wabwino kwa Koneliyo ndi banja lake. Koneliyo sanali Myuda komanso anali wosadulidwa, choncho zimene zinachitika pa tsikuli zinali zochititsa chidwi. Ndiyeno Koneliyo ndi banja lake atalandira mzimu woyera, Petulo anati: “Anthu awa alandira mzimu woyera monga mmenenso ife tinalandirira. Ndani amene angaletse kuti asabatizidwe ndi madzi?”​—Mac. 10:47.

14 Kenako mu 49 C.E., atumwi ndi akulu anakumana ku Yerusalemu kuti akambirane ngati zinali zoyenera kuti anthu a mitundu ina amene anakhala Akhristu azidulidwa. Pa msonkhanowu, Petulo analankhula molimba mtima n’kukumbutsa abalewo kuti iye anaona anthu a mitundu ina osadulidwa akulandira mzimu woyera. Zimene Petulo ananenazi zinathandiza kuti bungwe lolamuliralo lisankhe zochita mwanzeru. (Mac. 15:6-11, 13, 14, 28, 29) Akhristu achiyuda komanso a mitundu ina ayenera kuti anasangalala ndi zimene Petulo anachita. Zinali zosavuta kuti Akhristu onsewa aziona kuti Petulo ndi wodalirika chifukwa anali wokhulupirika komanso womvetsa zinthu.​—Aheb. 13:7.

15. Fotokozani zinthu zolakwika zimene Petulo anachita ku Antiokeya wa ku Siriya. (Onani chithunzi choyambirira.)

15 Msonkhano wa ku Yerusalemu utatha, Petulo anapita ku Antiokeya wa ku Siriya. Ali kumeneko, ankachita zonse bwinobwino ndi abale a mitundu ina. N’zosachita kufunsa kuti abalewo anaphunzira zambiri kwa Petulo. Koma kenako Petulo anangosintha mwadzidzidzi n’kusiya kudyera nawo limodzi. Izi ziyenera kuti zinawapweteka kwambiri abalewo ndipo zinawadabwitsa. Akhristu ena achiyuda monga Baranaba anayambanso kutsanzira Petulo n’kumasala abale awowo. Kodi n’chifukwa chiyani mkulu wodalirikayu anachita zinthu zimene zikanagawanitsa mpingo? Koma funso lofunika kwambiri ndi lakuti, kodi nkhani ya Petuloyi ingatithandize bwanji ngati mkulu walankhula kapena kuchita zinthu zotikhumudwitsa?

16. Kodi Petulo anathandizidwa bwanji pa zimene analakwitsa, nanga tingafunse mafunso ati?

16 Werengani Agalatiya 2:11-14. Petulo anakodwa mumsampha wa kuopa anthu. (Miy. 29:25) Ngakhale kuti iye ankadziwa kuti Yehova alibe tsankho, anachita zolakwika chifukwa choopa Akhristu achiyuda a mumpingo wa ku Yerusalemu. Koma mtumwi Paulo, yemwe analiponso pamsonkhano womwe unachitika mu 49 C.E. uja, anadzudzula Petulo chifukwa chochita zinthu mwachinyengo. (Mac. 15:12; Agal. 2:13) Kodi Akhristu a mitundu inawo anatani ataona zinthu zopanda chilungamo zimene Petulo anachitazi? Kodi anakhumudwa nazo kwambiri? Nanga kodi Petuloyo anasiyitsidwa maudindo ake chifukwa cha zimene analakwitsazi?

TIZIKHULULUKA

17. Kodi Yehova atakhululukira Petulo, zotsatira zake zinali zotani?

17 Baibulo silinena kuti Petulo anasiyitsidwa udindo wake. Iye anadzichepetsa ndipo analandira malangizo amene Paulo anam’patsa. Ndipo kenako Mulungu anamugwiritsa ntchito kulemba makalata awiri omwe anakhala mbali ya Baibulo. N’zochititsanso chidwi kuti m’kalata yake yachiwiri anatchula Paulo kuti “m’bale wathu wokondedwa.” (2 Pet. 3:15) Ngakhale kuti zimene Petulo anachita zija zinakhumudwitsa Akhristu a mitundu ina, Yesu yemwe ndi mutu wa mpingo, anapitirizabe kumugwiritsa ntchito. (Aef. 1:22) Choncho nawonso abale ndi alongo mumpingo anayenera kutsanzira Yehova ndi Yesu n’kumukhululukira Petulo. Iwo sankafunika kulola kuti zochita za Petulo ziwafooketse.

18. Kodi tingatsanzire chilungamo cha Yehova pa nkhani ngati ziti?

18 Masiku anonso, akulu amene akutsogolera mipingo si angwiro. Paja tonsefe timalakwitsa zinthu zina. (Yak. 3:2) Koma kodi timatani m’bale wina akatilakwira? Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati mkulu walankhula mawu osonyeza tsankho? Nanga mungatani ngati mkulu walankhula mawu amene akukhumudwitsani kapena kukupwetekani kwambiri? Kodi mungathamangire kuganiza kuti sakuyeneranso kukhala mkulu? Kapena kodi mungasiye nkhaniyo m’manja mwa Yesu yemwe ndi mutu wa mpingo? M’malo moganizira kwambiri zinthu zimene m’baleyo walakwitsa, ndi bwino kuganizira zaka zambirimbiri zimene watumikira mokhulupirika. Ngati m’bale amene wakulakwiraniyo akutumikirabe monga mkulu kapena wapatsidwa udindo wina, kodi mungasangalale naye limodzi? Mukakhululuka mumasonyeza kuti mukutsanzira Yehova pa nkhani ya chilungamo.​—Werengani Mateyu 6:14, 15.

19. Kodi tiyenera kuchita chiyani?

19 Popeza timakonda chilungamo, timafunitsitsa kuti nthawi imene Yehova adzathetse zinthu zonse zopanda chilungamo m’dziko la Satanali ifike. (Yes. 65:17) Koma panopa tiyeni tipitirize kutsanzira Yehova pa nkhani ya chilungamo. Tizikhala odzichepetsa n’kumavomereza kuti sitidziwa zonse ndiponso tizikhululuka ndi mtima wonse.