Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 18

‘Tizithamanga Panjirayo Mpaka pa Mapeto’

‘Tizithamanga Panjirayo Mpaka pa Mapeto’

“Ndathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake.”​—2 TIM. 4:7.

NYIMBO NA. 129 Tipitirizabe Kupirira

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi tonsefe tiyenera kuchita chiyani?

NGATI mukudwala kapena mwatopa, kodi mungafune kuthamanga pa mpikisano umene mukudziwa kuti ndi wovuta? N’zosakayikitsa kuti simungafune. Koma mtumwi Paulo ananena kuti Akhristu oona onse ali pa mpikisano. (Aheb. 12:1) Ndipo tonsefe, kaya ndife achinyamata kapena achikulire, amphamvu kapena ofooka, tiyenera kuthamanga mopirira mpaka pa mapeto ngati tikufuna kudzapeza mphoto imene Yehova adzatipatse.​—Mat. 24:13.

2. Malinga ndi 2 Timoteyo 4:7, 8, n’chifukwa chiyani tinganene kuti Paulo anali ndi ufulu wolankhula?

2 Paulo anali ndi ufulu wolankhula pa nkhaniyi chifukwa anali ‘atathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake.’ (Werengani 2 Timoteyo 4:7, 8.) Koma kodi mpikisano umene Paulo anatchulawo ndi wotani?

KODI MPIKISANO WAKE NDI WOTANI?

3. Kodi mpikisano umene Paulo ananena ndi wotani?

3 Nthawi zina, Paulo ankagwiritsa ntchito zinthu zimene zinkachitika pa masewera a ku Girisi pofuna kuphunzitsa mfundo zina zofunika. (1 Akor. 9:25-27; 2 Tim. 2:5) Maulendo angapo, iye anayerekezera moyo wa Mkhristu ndi mpikisano wothamanga. (1 Akor. 9:24; Agal. 2:2; Afil. 2:16) Munthu amayamba nawo ‘mpikisanowu’ akadzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa. (1 Pet. 3:21) Ndipo amamaliza mpikisanowu Yehova akamupatsa mphoto ya moyo wosatha.​—Mat. 25:31-34, 46; 2 Tim. 4:8.

4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Kodi moyo wa Mkhristu umafanana bwanji ndi mpikisano wothamanga? Pali zinthu zingapo, koma munkhaniyi tikambirana zinthu zitatu. Choyamba, tiyenera kuthamanga panjira yoyenera. Chachiwiri, tiyenera kuganizira kwambiri zomaliza nawo mpikisanowu. Ndipo chachitatu, tiyenera kuthamangabe ngakhale kuti tingakumane ndi mavuto.

TIZITHAMANGA PANJIRA YOYENERA

Tonsefe tiyenera kutsatira njira ya moyo wa Chikhristu (Onani ndime 5-7) *

5. Kodi tiyenera kutsatira njira iti? Perekani chifukwa.

5 Kuti munthu alandire mphoto pa mpikisano weniweni, ayenera kuthamanga panjira imene anthu okonza mpikisanowo asankha. Kuti ifenso tikalandire mphoto ya moyo wosatha, tiyenera kutsatira njira ya moyo wa Chikhristu. (Mac. 20:24; 1 Pet. 2:21) Koma Satana ndi anthu amene amamutsatira amafuna kuti tisiye njirayi n’kuyamba ‘kumathamanga nawo limodzi.’ (1 Pet. 4:4) Iwo amanyoza njira imene timatsatira ndipo amanena kuti njira yawo ndi yabwino komanso yopereka ufulu. Koma zimenezi ndi zabodza.​—2 Pet. 2:19.

6. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Brian?

6 Anthu onse amene amatsatira njira imene dziko la Satana limalimbikitsa amazindikira kuti njirayi sipereka ufulu koma imawachititsa kukhala akapolo. (Aroma 6:16) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Brian. Makolo ake ankamulimbikitsa kuti azitsatira njira ya moyo wa Chikhristu. Koma ali mnyamata, anayamba kukayikira ngati njirayi ingamuthandize kukhala wosangalala. Choncho anayamba kutsatira anthu amene amayendera mfundo za Satana. Iye ananena kuti: “Sindinadziwe kuti zimene ndinkachita pofuna kupeza ufulu zingachititse kuti ndikhale kapolo wa zinthu zoipa. Patapita nthawi, ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kumwa mowa kwambiri komanso kuchita chiwerewere. Pa zaka zotsatira, ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo amphamvu kwambiri ndipo ndinakhala kapolo wa mankhwalawo. . . . Ndinayambanso kugulitsa mankhwalawa n’cholinga choti ndizipeza ndalama zondithandiza kuchitabe zinthuzi.” Koma patapita nthawi, Brian anasankha kutsatira mfundo za Yehova. Iye anasintha ndipo anabatizidwa mu 2001. Panopa akusangalala kwambiri kuti akutsatira njira ya moyo wa Chikhristu. *

7. Mogwirizana ndi Mateyu 7:13, 14, kodi tiyenera kusankha pakati pa misewu iwiri iti?

7 Kusankha njira yolondola n’kofunika kwambiri. Satana amafuna kuti tisiye kuthamanga panjira yopanikiza ‘yolowera ku moyo’ n’kuyamba kuyenda pamsewu waukulu umene anthu ambiri m’dzikoli akuyendamo. Anthu ambiri amakonda msewu umenewu ndipo ndi wosavuta kuyendamo koma “ukupita kuchiwonongeko.” (Werengani Mateyu 7:13, 14.) Choncho kuti tikhalebe panjira yolondola popanda kusokonezeka, tiyenera kudalira Yehova ndiponso kumumvera.

TIZIPEWA ZOSOKONEZA KOMANSO ZOPUNTHWITSA

Tizipewa zosokoneza komanso kupunthwitsa anthu ena (Onani ndime 8-12) *

8. Kodi munthu wothamanga akapunthwa amatani?

8 Anthu othamanga pa mpikisano amayang’ana kwambiri msewu n’cholinga choti asapunthwe. Komabe akhoza kuponda pakadzenje kapena munthu wina akhoza kuwapunthwitsa mwangozi. Ndiye ngati agwa, amadzuka n’kupitiriza kuthamanga. Iwo amaganizira kwambiri zomaliza mpikisanowo n’kukalandira mphoto, osati zimene zawapunthwitsa.

9. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikapunthwa?

9 Pa mpikisano wathu, timapunthwa nthawi zambiri, kaya polankhula kapena kuchita zinthu zolakwika. Nthawi zina, anzathu amene akuthamanga nafe pampikisanowu ndi amene angatikhumudwitse. Koma zimenezi si zodabwitsa chifukwa tonsefe si angwiro ndipo tikuthamanga limodzi pamsewu wopanikiza wopita ku moyo wosatha. Choncho nthawi zina tikhoza kusokonezana. Paulo anasonyeza kuti nthawi zina tonsefe tikhoza kuchititsa anzathu kukhala ndi “chifukwa chodandaulira.” (Akol. 3:13) Koma m’malo moganizira zimene zatipunthwitsa, tiziganizira kwambiri za mphoto imene tidzalandire. Ndiye tikagwa, tiziyesetsa kudzuka n’kupitiriza kuthamanga. Tikakwiya n’kumakana kudzuka, sitingamalize nawo mpikisanowu ndipo sitingalandire mphoto. Komanso ngati tikukana kudzuka tikhoza kupunthwitsa anthu ena omwe akuyesetsa kuthamanga pamsewu wopanikiza wopita ku moyowu.

10. Kodi tingapewe bwanji ‘kupunthwitsa’ anthu ena?

10 Njira ina imene tingapewere ‘kupunthwitsa’ anthu pa mpikisanowu ndi kulolera zimene ena akufuna m’malo moumirira maganizo athu. (Aroma 14:13, 19-21; 1 Akor. 8:9, 13) Pamenepa tingati tikusiyana ndi othamanga pa mpikisano weniweni. Iwo amakhala akupikisana ndi othamanga ena, ndipo aliyense amafuna kuti mphotoyo ikhale yake basi. Othamanga amenewa amangoganizira zofuna zawo zokha. Choncho angakankhe anthu ena n’cholinga choti iwowo akhale patsogolo. Koma ifeyo sitilimbana pa mpikisanowu. (Agal. 5:26; 6:4) Cholinga chathu n’kuthandiza anthu ambiri kuti akamalize nafe mpikisanowu n’kulandira mphoto ya moyo. Choncho tiziyesetsa kutsatira malangizo a Paulo akuti: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”​—Afil. 2:4.

11. Kodi munthu wothamanga pa mpikisano amaganizira kwambiri za chiyani? Perekani chifukwa.

11 Kuwonjezera pa kuyang’ana msewu, othamanga pa mpikisano amaganizira kwambiri zomaliza mpikisanowo. Ngakhale kuti sangaone pamene akamalizire, amayerekezera atamaliza mpikisanowo n’kulandira mphoto. Kuganizira kwambiri za mphotoyo kumawathandiza kuti apitirizebe kuthamanga mwamphamvu.

12. Kodi Yehova watilonjeza chiyani?

12 Yehova walonjeza kuti adzapereka mphoto kwa aliyense amene adzamalize mpikisanowu, kaya ndi moyo wosatha kumwamba kapena padzikoli. Baibulo limafotokoza madalitso amene tidzalandire, ndipo zimenezi zimatithandiza kuganizira mmene moyo udzakhalire m’tsogolo. Tikamaganizira kwambiri madalitso amene tikuyembekezerawa, sitidzalola kuti chilichonse chitilepheretse kumaliza mpikisanowu.

TIZITHAMANGABE NGAKHALE KUTI PALI MAVUTO

Tizithamangabe pa mpikisano wokalandira moyo ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto (Onani ndime 13-20) *

13. Kodi tikhoza kudalira mphamvu iti yomwe othamanga ena sakhala nayo?

13 Anthu othamanga pa mpikisano ku Girisi ankatopa komanso kumva kupweteka. Zimene ankadalira kuti apirire mavutowo zinali mphamvu zawo komanso zimene anaphunzira pokonzekera mpikisano basi. Nafenso timaphunzira mmene tingathamangire pa mpikisano wokalandira moyo. Koma tili ndi zinthu zinanso zimene zimatithandiza. Timadalira Yehova yemwe ali ndi mphamvu zopanda malire. Komanso iye analonjeza kuti azitiphunzitsa komanso kutilimbitsa.​—1 Pet. 5:10.

14. Kodi lemba la 2 Akorinto 12:9, 10 lingatithandize bwanji kuti tipirire mavuto athu?

14 Paulo anakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, ankanyozedwa, kuzunzidwa, kutopa komanso kupirira vuto lina limene analitchula kuti “munga m’thupi.” (2 Akor. 12:7) Iye sankaona kuti zimenezi ndi zifukwa zomuchititsa kusiya kutumikira Yehova koma ankaona kuti ndi mwayi woti azimudalira. (Werengani 2 Akorinto 12:9, 10.) Popeza Paulo anali ndi maganizo amenewa, Yehova anamuthandiza pa mavuto ake onse.

15. Kodi chingachitike n’chiyani tikamatsanzira Paulo?

15 Ifenso tikhoza kunyozedwa kapena kuzunzidwa chifukwa cha zimene timakhulupirira. Tingavutikenso chifukwa cha matenda kapena kutopa. Koma tikamatsanzira Paulo, vuto lililonse lingatipatse mwayi woona Yehova akutithandiza mwachikondi.

16. Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachite ngakhale kuti ndinu achikulire kapena mukudwala?

16 Kodi panopa muli chigonere chifukwa cha matenda? Kapena kodi mumayenda pa njinga ya olumala? Kodi mawondo anu amangokhala njenjenje kapena mumavutika kuona bwinobwino? Ngati ndi choncho, kodi zingatheke kuthamanga limodzi ndi achinyamata amphamvu? Inde. Anthu ambiri achikulire komanso odwala akuthamanga panjira ya ku moyo. Iwo sadalira mphamvu zawo pochita zimenezi. M’malomwake, amadalira mphamvu za Yehova zomwe amazipeza akamamvetsera kapena kuonera misonkhano yochita kujambulidwa. Iwo amayesetsanso kulalikira kwa madokotala, manesi ndi achibale.

17. Kodi Yehova amamva bwanji akaona anthu achikulire kapena odwala?

17 Kaya mukukumana ndi vuto lotani, simuyenera kukhumudwa n’kumaganiza kuti simungathe kuthamanga panjira yopita ku moyo. Yehova amakukondani kwambiri chifukwa cha chikhulupiriro chanu komanso kupirira kumene mwasonyeza kwa zaka zambiri. Panopa m’pamene mukufunika kuthandizidwa kwambiri ndi Yehova ndipo iye sadzakusiyani. (Sal. 9:10) M’malomwake, adzakuyandikirani kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina amene akudwala. Iye anati: “Matenda akakula ndimaona kuti mipata yolalikira imachepa. Koma ndimadziwa kuti Yehova amasangalala ngakhale nditangolalikira pang’ono ndipo zimenezi zimandisangalatsa.” Mukakhumudwa muzikumbukira kuti simuli nokha chifukwa Yehova ali nanu. Kumbukirani chitsanzo cha Paulo komanso mawu olimbikitsa amene ananena akuti: “Ndimasangalala ndi kufooka . . . Pakuti pamene ndili wofooka, m’pamene ndimakhala wamphamvu.”​—2 Akor. 12:10.

18. Kodi anthu ena amakumana ndi vuto liti?

18 Anthu ena amene akuthamanga pa mpikisano wokalandira moyowu amakumananso ndi vuto lina. Iwo amakhala ndi mavuto amene anthu ena sangawaone kapena kuwamvetsa. Mwachitsanzo, ena amadwala matenda a maganizo kapena kuda nkhawa kwambiri. N’chifukwa chiyani tinganene kuti vuto limeneli ndi losowetsa mtendere? Munthu akathyoka mkono kapena akamayenda pa njinga ya olumala, aliyense amatha kuona vuto lake ndipo amafuna kumuthandiza. Koma amene ali ndi vuto la maganizo kapena nkhawa sangakhale ndi zizindikiro zoonekera. Vuto lawolo limakhala lopweteka ngati mmene zimakhalira ndi munthu amene wathyoka mkono koma mwina anthu sangawachitire chifundo ngati mmene angachitire ndi winayo.

19. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Mefiboseti?

19 Ngati muli ndi vuto limene mukuona kuti anthu ena salimvetsa, mukhoza kulimbikitsidwa ndi chitsanzo cha Mefiboseti. (2 Sam. 4:4) Iye anali wolumala ndipo Mfumu Davide anamuganizira zolakwika. Palibe chilichonse chimene Mefiboseti analakwitsa kuti akumane ndi mavutowa. Koma m’malo mongokhalira kukhumudwa, iye ankayamikira zinthu zabwino zimene zinkachitika pa moyo wake. Mwachitsanzo, ankayamikira kukoma mtima kumene Davide anali atamusonyeza. (2 Sam. 9:6-10) Choncho pamene Davide anamuganizira zolakwika, maganizo ake sanali pa nkhani yokhayo. Iye sanalole kuti akhumudwe kwambiri ndi zimene Davide analakwitsazi. Komanso sanaimbe mlandu Yehova chifukwa cha zimene Davide anachita. Koma Mefiboseti ankaganizira kwambiri zimene akanatha kuchita pothandiza mfumu yosankhidwa ndi Yehova. (2 Sam. 16:1-4; 19:24-30) Ndipo Yehova anachititsa kuti chitsanzo chabwino cha Mefiboseti chilembedwe m’Mawu ake kuti chizitithandiza.​—Aroma 15:4.

20. Kodi anthu ena angavutike bwanji chifukwa cha nkhawa, nanga sayenera kukayikira za chiyani?

20 Chifukwa cha matenda a nkhawa, abale ndi alongo ena amavutika kwambiri kuchita zinthu ndi anthu ena. Ngakhale kuti zimawavuta kukhala pa gulu, amapezekabe pamisonkhano ya mpingo komanso ikuluikulu. Mwina amavutikanso kulankhula ndi anthu osawadziwa, koma amalalikirabe. Ngati ndi mmene zilili ndi inuyo, dziwani kuti si inu nokha. Anthu ambiri amavutika ndi zimenezi. Musaiwale kuti Yehova amasangalala mukamachita zonse zimene mungakwanitse. Popeza mukupitiriza kuchita zimene mungathe, ndiye kuti Yehova akukupatsani mphamvu imene mukufunikira. * (Afil. 4:6, 7; 1 Pet. 5:7) Ngati mukutumikira Yehova ngakhale kuti mukulimbana ndi mavuto enaake, musamakayikire kuti iye akusangalala nanu.

21. Kodi Yehova angatithandize tonsefe kuchita chiyani?

21 N’zosangalatsa kuti mpikisano umene Paulo anatchula sufanana ndendende ndi mpikisano weniweni. Pa mpikisano wothamanga weniweni munthu mmodzi ndi amene amalandira mphoto. Koma aliyense amene angakhalebe wokhulupirika n’kumaliza mpikisano wa Chikhristu adzalandira mphoto ya moyo wosatha. (Yoh. 3:16) Pa mpikisano weniweni, othamanga onse amafunika kukhala athanzi, kupanda kutero sangapambane. Pomwe pa mpikisano wathuwu, ambirife sitikupeza bwino koma tikuthamangabe. (2 Akor. 4:16) Ndipo Yehova akhoza kutithandiza tonsefe kuti tithamange mpaka pa mapeto pa mpikisanowu.

NYIMBO NA. 144 Yang’ananibe Pamphoto

^ ndime 5 Atumiki a Yehova ambiri masiku ano akuvutika ndi ukalamba kapena matenda aakulu. Ndipo tonsefe timatopa nthawi zina. Choncho tikhoza kuona kuti sitingakwanitse kuthamanga pa mpikisano. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti tithamange mopirira mpikisano umene mtumwi Paulo anatchula, n’cholinga choti tidzapeze mphoto ya moyo wosatha.

^ ndime 6 Onani nkhani yakuti “Baibulo Limasintha Anthu” mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2013.

^ ndime 20 Kuti mudziwe zinthu zimene zingathandize anthu amene amavutika ndi nkhawa komanso nkhani za anthu amene anakumana ndi vutoli, onerani pulogalamu ya JW Broadcasting® ya May 2019. Pitani pa jw.org®. Pitani pamene alemba kuti LAIBULALE > JW BROADCASTING®.

^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kulalikira mwakhama kumathandiza m’bale wachikulireyu kuti azithamanga panjira yoyenera.

^ ndime 65 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Tikhoza kupunthwitsa anthu ena ngati titawakakamiza kuti amwe mowa wambiri kapena ngati ifeyo sitidziletsa pa nkhaniyi.

^ ndime 67 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale amugoneka m’chipatala koma akuthamangabe pa mpikisanowu polalikira kwa anthu omusamalira.