Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani Yesu atatsala pang’ono kufa analankhula mawu a Davide a pa Salimo 22:1?

Ena mwa mawu omaliza amene Yesu analankhula atatsala pang’ono kufa ndi amene amapezeka pa Mateyu 27:46 akuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?” Ponena zimenezi Yesu anakwaniritsa mawu a wamasalimo Davide omwe ali pa Salimo 22:1. (Maliko 15:34) Kungakhale kulakwa kuganiza kuti Yesu analankhula mawuwa chifukwa chokhumudwa kapena kuti anasowa chikhulupiriro kwa kanthawi kochepa. Tikutero popeza Yesu ankadziwa bwino chifukwa chake anayenera kufa ndipo anali wofunitsitsa kuchita zimenezo. (Mat. 16:21; 20:28) Iye ankadziwanso kuti pa nthawi ya imfa yake Yehova sadzamuteteza kapena ‘kumutchinga’ mwa njira inayake. (Yobu 1:10) Choncho Yehova analola kuti Yesu asonyeze kuti akhalabe wokhulupirika ngakhale imfa yake itakhala yowawa chotani.​—Maliko 14:35, 36.

Ndiye n’chifukwa chiyani Yesu ananena mawu a pa Salimo limeneli? Ngakhale kuti sitinganene motsimikiza chifukwa chake, tiyeni tikambirane zifukwa zimene mwina ndi zomwe zinamuchititsa kulankhula mawuwa. *

Polankhula mawu amenewa, mwina Yesu ankafuna kutsimikizira kuti Yehova salowererapo pa imfa yake. Yesu ankafunika kupereka dipo popanda kuthandizidwa ndi Yehova. Pa nthawiyi iye anali munthu ndipo ankafunika kufa kuti “alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.”​—Aheb. 2:9.

Potchula mawu ochepa opezeka mu Salimoli, n’kutheka kuti Yesu ankafuna anthu aganizire zimene zili mu Salimo lonselo. Pa nthawi imeneyo Ayuda ankakonda kuloweza Masalimo ambiri pamtima. Choncho akamva vesi la mu Salimo linalake, zinali zosavuta kuti akumbukire mavesi a mu Salimo lonselo. Ngati zimenezi ndi zomwe Yesu ankafuna ndiye kuti anathandiza Ayuda omwe ankamutsatira kukumbukira maulosi ambiri opezeka mu Salimoli onena za imfa yake. (Sal. 22:7, 8, 15, 16, 18, 24) Komanso mavesi omalizira a mu Salimoli amasonyeza kuti Yehova ndi woyenera kutamandidwa ndiponso kuti iye ndi wolamulira wa dziko lonse lapansi.​—Sal. 22:27-31.

Polankhula mawu a Davidewa, Yesu ayenera kuti ankafuna kusonyeza kuti iye ndi wosalakwa. Yesu asanafe anaimbidwa mlandu wabodza woti ankanyoza Mulungu ndipo anafunika kupirira zimenezi. (Mat. 26:65, 66) Oweruza a khoti lalikulu la Ayuda anamuzenga mlanduwu usiku ndipo zonse zimene ankachita zinali zosagwirizana ndi malamulo. (Mat. 26:59; Maliko 14:56-59) Pofunsa funso limene lili pa Salimoli, Yesu ayenera kuti ankafuna anthu adziwe kuti iye sanachite chilichonse chimene chikanachititsa kuti alandire chilango chimenechi.

N’kutheka kuti Yesu ankafuna kukumbutsa anthu ena kuti ngakhale kuti Davide yemwe analemba Salimoli anakumana ndi mavuto, sizinkatanthauza kuti Yehova sankasangalala naye. Funso limene Davide anafunsa silinkasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro chochepa. Tikutero chifukwa atafunsa funsoli, Davide anapitiriza kufotokoza mfundo zosonyeza kuti ankakhulupirira kuti Yehova ali ndi mphamvu zotha kupulumutsa anthu ake ndipo anapitiriza kumudalitsa. (Sal. 22:23, 24, 27) Mofananamo, ngakhale kuti Yesu yemwe anali “Mwana wa Davide,” anavutika pamtengo wozunzikirapo, sizinkatanthauza kuti Yehova wasiya kusangalala naye.​—Mat. 21:9.

Mwina pamenepa Yesu ankamva chisoni kwambiri chifukwa chakuti Yehova ankafunika kusiya kumuteteza, n’cholinga choti asonyeze mokwanira kuti anali wokhulupirika. Si kuti chinali cholinga cha Yehova kuti Mwana wake adzavutike n’kufa. Koma zimenezi zinakhala zofunika pambuyo pa kuchimwa kwa Adamu ndi Hava. Yesu sanalakwe chilichonse koma ankafunika kuvutika komanso kufa kuti ayankhe nkhani imene Satana anayambitsa n’kupereka dipo lowombolera zimene Adamu anataya. (Maliko 8:31; 1 Pet. 2:21-24) Izi zikanatheka pokhapokha ngati Yehova akanasiya kuteteza Yesu kwa kanthawi ndipo kameneka kanali koyamba kuti zimenezi zichitike pa moyo wa Yesu.

Yesu ayenera kuti amafuna kuthandiza otsatira ake kuti aziganizira chifukwa chake Yehova analola kuti iye afe mwa njira imeneyi. * Yesu ankadziwa kuti ambiri akhumudwa iye akaphedwa ngati wachifwamba n’kupachikidwa pamtengo wozunzikirapo. (1 Akor. 1:23) Ngati otsatira ake akanamaganizira chifukwa chenicheni chimene iye anafera, akanamvetsa kufunika kwa imfa yakeyi. (Agal. 3:13, 14) Choncho iwo akanamamuona ngati Mpulumutsi wawo osati wachifwamba.

Kaya pali zifukwa zotani zimene zinachititsa Yesu kulankhula mawu amenewa, iye ankadziwa kuti zimene zinamuchitikirazi zinakwaniritsa chifuniro cha Mulungu. Atangonena mawu a mu Salimoli Yesu ananena kuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!” (Yoh. 19:30; Luka 22:37) Chifukwa choti Yehova anasiya kuteteza Yesu kwa kanthawi, zinathandiza kuti Yesuyo akwanitse kuchita zonse zimene Atate wake anamutuma kudzachita padzikoli. Zinamuthandizanso kuti akwaniritse zinthu zonse zokhudza iyeyo zomwe zinalembedwa “m’chilamulo cha Mose, m’Zolemba za aneneri ndi m’Masalimo.”​—Luka 24:44

^ ndime 2 Onaninso ndime 9 ndi 10 munkhani yakuti “Zimene Tingaphunzire pa Mawu Omaliza a Yesu,” yomwe ili m’magaziniyi.

^ ndime 4 Pa nthawi ya utumiki wake, si nthawi zonse pamene Yesu ankalankhula kapena kupereka funso pofuna kusonyeza mmene ankamvera. Nthawi zambiri ankachita zimenezi pofuna kuthandiza ophunzira ake kuti afotokoze maganizo awo.​—Maliko 7:24-27; Yoh. 6:1-5; onani Nsanja ya Olonda, ya October 15, 2010, tsamba 4-5.