Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 18

Tingatani Kuti Tizikhala ndi Zolinga Zauzimu N’kumazikwaniritsa?

Tingatani Kuti Tizikhala ndi Zolinga Zauzimu N’kumazikwaniritsa?

“Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Dzipereke pa zinthu zimenezi kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.”—1 TIM. 4:15.

NYIMBO NA. 84 Timadzipereka

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi ndi zolinga zauzimu ziti zomwe tingadziikire?

 MONGA Akhristu oona, timakonda kwambiri Yehova. Timafunitsitsa kuti tizichita zonse zomwe tingathe pomutumikira. Kuti zimenezi zitheke timafunika kudziikira zolinga zauzimu monga kukhala ndi makhalidwe abwino, kuphunzira maluso othandiza komanso kupeza njira zimene tingathandizire ena. *

2. N’chifukwa chiyani tiyenera kudziikira zolinga zauzimu n’kumayesetsa kuzikwaniritsa?

2 N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kupita patsogolo mwauzimu? Chifukwa chachikulu n’chakuti timafuna kusangalatsa Atate wathu wakumwamba. Yehova amasangalala akationa tikugwiritsa ntchito luso lathu mmene tingathere pomutumikira. Kuwonjezera pamenepo timafuna kupita patsogolo mwauzimu kuti tizithandiza kwambiri abale ndi alongo athu. (1 Ates. 4:9, 10) Kaya takhala m’choonadi kwa nthawi yayitali bwanji, tonsefe tingathe kupita patsogolo mwauzimu. Tiyeni tione mmene tingachitire zimenezi.

3. Mogwirizana ndi 1 Timoteyo 4:12-16, kodi mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteyo kuchita chiyani?

3 Pamene mtumwi Paulo ankalembera Timoteyo kalata yake yoyamba, n’kuti wachinyamata wachitsanzo chabwinoyo ali kale mkulu waluso. Komabe Paulo anamulimbikitsa kuti apitirizebe kupita patsogolo mwauzimu. (Werengani 1 Timoteyo 4:12-16.) Mukamaganizira mawu a Paulowa muona kuti iye ankafuna kuti Timoteyo apite patsogolo m’njira ziwiri izi: Kukhala ndi makhalidwe abwino monga chikondi, chikhulupiriro komanso khalidwe loyera ndiponso kuwonjezera luso lake pakuwerenga pamaso pa anthu, kulimbikitsa ndi kuphunzitsa. Poona chitsanzo cha Timoteyo, tiyeni tikambirane mmene kukhala ndi zolinga zomwe tingazikwaniritse kungatithandizire kupita patsogolo mwauzimu. Tikambirananso njira zina zimene zingatithandize kuti tizichita zambiri pa utumiki wathu.

KUKHALA NDI MAKHALIDWE ABWINO

4. Mogwirizana ndi Afilipi 2:19-22, n’chiyani chinathandiza Timoteyo kuti akhale mtumiki wabwino wa Yehova?

4 Kodi n’chiyani chinathandiza Timoteyo kukhala mtumiki wabwino wa Yehova? Ndi makhalidwe abwino amene anali nawo. (Werengani Afilipi 2:19-22.) Tikaona mmene Paulo anafotokozera zokhudza Timoteyo, tinganene kuti iye anali wodzichepetsa, wokhulupirika, wakhama komanso wodalirika. Iye anali wachikondi ndipo ankadera nkhawa kwambiri abale. Zimenezi zinachititsa kuti Paulo azimukonda ndipo sankakayikira kuti akwanitsa mautumiki ovuta omwe anam’patsa. (1 Akor. 4:17) Mofanana ndi zimenezi, ifenso Yehova angamatikonde ndipo tingakhale othandiza kwambiri mumpingo tikakhala ndi makhalidwe omwe amamusangalatsa.​—Sal. 25:9; 138:6.

Sankhani khalidwe labwino lomwe mukufuna kuti muzilisonyeza kwambiri (Onani ndime 5-6)

5. (a) Kodi mungatani kuti mukhale ndi cholinga chofuna kukulitsa khalidwe linalake? (b) Kodi mlongo wachitsikana pachithunzichi, akuchita zotani kuti akwaniritse cholinga chake choti azisonyeza kwambiri ena chifundo?

5 Muzisankha cholinga chimene mukufuna kukwaniritsa. Muzipemphera n’kuganizira mbali ya umunthu wanu imene muyenera kusintha. Muzisankha khalidwe linalake limene mukufuna kukulitsa. Mwachitsanzo, kodi mukufunitsitsa kuti muzisonyeza kwambiri ena chifundo kapena kuthandiza Akhristu anzanu? Kodi mukufunitsitsa kuti muzikhala mwamtendere ndi ena komanso muzikhululuka? Mungachite bwino kufunsa mnzanu wodalirika kuti akuthandizeni kudziwa zimene mungachite kuti mupite patsogolo.​—Miy. 27:6.

6. Kodi mungatani kuti mukwaniritse cholinga chanu chofuna kukulitsa khalidwe linalake?

6 Muzichita khama kuti mukwaniritse cholinga chanu. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Njira imodzi ndi kuphunzira mosamala khalidwe linalake limene mukufuna kukulitsa. Tiyerekeze kuti mukufuna kuyesetsa kuti muzikhululukira ena. Mungayambe ndi kuwerenga komanso kuganizira mozama nkhani za anthu otchulidwa m’Baibulo omwe ankakhululuka ndi mtima wonse komanso amene sankakhululuka. Taganizirani chitsanzo cha Yesu. Iye ankakhululukira ena ndi mtima wonse. (Luka 7:47, 48) Sankaganizira kwambiri zolakwa zawo ndipo ankawaona kuti angathe kusintha. Koma Afarisi a munthawi yake ankaona “ena onse ngati opanda pake.” (Luka 18:9) Pambuyo poganizira zitsanzo zimenezi dzifunseni kuti: ‘Kodi ineyo ndimaona zotani mwa ena? Kodi ndimasankha kuganizira makhalidwe ati omwe ali nawo?’ Ngati zikukuvutani kukhululukira winawake, muziyesa kulemba penapake makhalidwe ambiri abwino a munthuyo. Kenako muzidzifunsa kuti: ‘Kodi Yesu amamuona bwanji munthuyu? Kodi akanasankha kumukhululukira?’ Kuphunzira mwa njira imeneyi kungatithandize kuti tisinthe mmene timaganizira. Poyamba tingamafunike kuyesetsa kuti tikhululukire munthu amene watilakwira. Koma tikapitiriza kuchita khama, m’kupita kwa nthawi zidzakhala zosavuta kuti tizikhululuka.

KUPHUNZIRA MALUSO OTHANDIZA

Muzidzipereka kuphunzira mmene mungakonzere zinthu pa Nyumba ya Ufumu (Onani ndime 7) *

7. Mogwirizana ndi Miyambo 22:29, kodi Yehova akugwiritsa ntchito bwanji anthu aluso masiku ano?

7 Cholinga china chimene mungadziikire ndi kuphunzira luso linalake lothandiza. Ganizirani za kuchuluka kwa anthu amene amafunika pomanga maofesi a nthambi, Malo a Msonkhano komanso Nyumba za Ufumu. Ambiri mwa iwo anapeza luso pogwira ntchito limodzi ndi abale ndi alongo omwe amadziwa bwino ntchitoyo. Monga mmene tikuonera pachithunzipa, abale ndi alongo akuphunzira luso lomwe lingawathandize pa ntchito yokonza Malo a Msonkhano ndi Nyumba za Ufumu. M’njira zimenezi komanso zina, Yehova Mulungu yemwe ndi “Mfumu yamuyaya,” ndi Yesu Khristu yemwe ndi “Mfumu ya . . . mafumu,” akukwanitsa zinthu zazikulu pogwiritsa ntchito anthu aluso. (1 Tim. 1:17; 6:15; werengani Miyambo 22:29.) Timafuna kuti tizichita khama komanso kugwiritsa ntchito luso lathu polemekeza Yehova osati kudzilemekeza tokha.​—Yoh. 8:54.

8. Kodi mungatani kuti mudziikire cholinga chofuna kuphunzira luso linalake?

8 Muzisankha cholinga chimene mukufuna kukwaniritsa. Kodi ndi luso liti limene mukufuna kuphunzira? Mungafunse akulu a mumpingo wanu kapena woyang’anira dera wanu kuti akuthandizeni kudziwa luso limene akuona kuti mungachite bwino kukhala nalo. Mwachitsanzo, ngati atakuuzani kuti muyenera kukulitsa luso lanu la kulankhula ndi kuphunzitsa, mungawafunse kuti akutchulireni luso la kulankhula limene muyenera kugwirirapo ntchito. Kenako muzichita khama kuti mukulitse lusolo. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

9. Kodi mungatani kuti mukwanitse cholinga chanu chofuna kuphunzira luso linalake?

9 Muzichita khama kuti mukwaniritse cholinga chanu. Tiyerekeze kuti mukufuna kukulitsa luso lanu lophunzitsa. Mukhoza kuphunzira mosamala kabuku ka Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso. Mukapatsidwa nkhani pa misonkhano ya mkati mwa mlungu, mungapemphe m’bale waluso kuti aimvetsere pasadakhale komanso kukufotokozerani momwe mungafunike kukonza. Kuwonjezera pa kukhala waluso, muzikonzekera m’njira yoti anthu aone kuti ndinu wakhama komanso wodalirika.​—Miy. 21:5; 2 Akor. 8:22.

10. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene tingakulitsire luso linalake?

10 Bwanji ngati mukufuna kukulitsa luso linalake limene mwachibadwa ndi lovuta kwa inu? Musamataye mtima. M’bale wina dzina lake Garry, zinkamuvuta kuwerenga. Iye amakumbukira mmene ankachitira manyazi akamawerenga pamisonkhano yampingo. Koma anayesetsa kuchita khama. Iye amanena kuti chifukwa cha zimene anaphunzitsidwa, panopa amakwanitsa kukamba nkhani m’Nyumba ya Ufumu, pamisonkhano yadera komanso yachigawo.

11. Mofanana ndi Timoteyo, kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizichita zambiri potumikira Yehova?

11 Kodi Timoteyo anafika pokhala mphunzitsi wabwino kwambiri? Baibulo silinena. Koma n’zosakayikitsa kuti chifukwa chotsatira malangizo a Paulo, iye anapitiriza kuchita bwino kwambiri pa utumiki wake. (2 Tim. 3:10) Mofanana ndi zimenezi, ifenso tikamakulitsa luso lathu, tingamachite zambiri potumikira Yehova.

MUZIFUFUZA NJIRA ZOTHANDIZIRA ENA

12. Kodi ena amakuthandizani bwanji?

12 Tonsefe timapindula ndi zimene ena amachita potithandiza. Tikagonekedwa m’chipatala, timayamikira abale a m’Makomiti Olankhulana ndi Achipatala kapena a m’Magulu Oyendera Odwala akabwera kudzationa. Tikakumana ndi mavuto enaake timayamikira mkulu wachikondi akapatula nthawi yake kuti atimvetsere komanso kutilimbikitsa. Tikafuna thandizo pa nkhani ya mmene timachititsira phunziro la Baibulo, timasangalala mpainiya waluso akavomera kukhala nawo paphunzirolo komanso kutipatsa malangizo. Abale ndi alongo onsewo amasangalala kutithandiza. Ifenso tingamasangalale ngati titamadzipereka kuti tithandize abale athu. Yesu anati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Ndiye ngati mukufuna kuchita zambiri pambali zimenezi komanso m’njira zina, n’chiyani chingakuthandizeni kukwaniritsa zolinga zanuzo?

13. Mukamadziikira cholinga, kodi muyenera kukumbukira chiyani?

13 Muzidziikira cholinga chenicheni chimene mukufuna kuti muchikwaniritse. Mwachitsanzo, mwina mungaganize kuti, ‘Ndikufuna ndizichita zambiri mumpingo.’ Komatu zingakhale zovuta kudziwa mmene mungakwaniritsire cholinga ngati chimenecho ndipo mwina simungadziwe ngati mwachikwaniritsa. Choncho muzidziwa zenizeni zimene mukufuna kuchita. Mungathe kulemba penapake cholingacho komanso zimene mukufuna kuchita kuti muchikwaniritse.

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala okonzeka kusintha pa nkhani ya zolinga zimene timadziikira?

14 Tiyeneranso kukhala okonzeka kusintha pa nkhani ya zolinga zimene timadziikira. Chifukwa chiyani? Chifukwa sitingathe kulamulira zinthu zonse zimene zimachitika pa moyo wathu. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anathandiza kukhazikitsa mpingo watsopano mumzinda wa Tesalonika. Ndipo n’zosakayikitsa kuti anali ndi cholinga choti akhalebe kumeneko kuti azithandiza Akhristu atsopanowo. Koma otsutsa anamukakamiza kuti achoke mumzindawo. (Mac. 17:1-5, 10) Paulo akanakhalabe komweko, akanaika abale akewo pangozi. Komabe iye sanasiye kuwathandiza. M’malomwake anavomereza kusinthaku. Pambuyo pake anatumiza Timoteyo kuti akathandize Akhristu atsopanowo kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. (1 Ates. 3:1-3) Akhristu a ku Tesalonika anasangalala kwambiri kuti Timoteyo anadzipereka kukatumikira kumeneko.

15. Kodi zimene zimachitika pa moyo wathu zingakhudze bwanji zolinga zathu? Perekani chitsanzo.

15 Tingaphunzire zambiri pa zimene zinachitikira Paulo ku Tesalonika. Tingamafune titachita utumiki winawake koma zinthu zina pa moyo wathu zingatilepheretse kukwaniritsa cholinga chathucho. (Mlal. 9:11) Ngati umu ndi mmene zilili ndi inu, muzikhala okonzeka kusankha cholinga china chimene mungachikwaniritse. Izi ndi zimene banja la Ted ndi Hiedi linachita. Chifukwa cha matenda, iwo ankafunika kusiya utumiki wa pa Beteli. Koma kukonda Yehova kunawachititsa kufunafuna njira zina zowonjezerera utumiki wawo. Iwo anayamba ndi kuchita upainiya wokhazikika. M’kupita kwa nthawi anaikidwa kukhala apainiya apadera ndipo Ted anaphunzitsidwa kuti akhale woyang’anira dera wogwirizira. Kenako panakhala kusintha pa nkhani ya msinkhu umene munthu angatumikire monga woyang’anira dera. Zitatero Ted ndi Hiedi anadziwiratu kuti sakuyenereranso utumiki umenewu. Ngakhale kuti anakhumudwa, iwo anazindikira kuti angatumikire Yehova m’njira zinanso. Ted ananena kuti, “Taphunzira kuti tisamangoganizira zochita mtundu umodzi wokha wa utumiki.”

16. Kodi tikuphunzira chiyani pa Agalatiya 6:4?

16 Sitingathe kulamulira chilichonse chimene chimachitika pa moyo wathu. Choncho tisamaone kuti ndife ofunika kwa Yehova chifukwa cha utumiki umene tikuchita kapenanso kumayerekezera utumiki wathu ndi wa ena. Hiedi anafotokoza kuti, “Sukhala ndi mtendere ukamayerekezera zimene zikuchitika pa moyo wako ndi wa anthu ena.” (Werengani Agalatiya 6:4.) Choncho n’zofunika kuti tizifufuza njira zimene tingathandizire ena komanso kutumikira Yehova. *

17. Kodi mungatani kuti muyenerere kupatsidwa utumiki winawake?

17 Mungathe kuchita zambiri potumikira Yehova ngati mumakhala moyo wosalira zambiri komanso ngati mumapewa ngongole. Mungadziikire zolinga zing’onozing’ono zomwe zingakuthandizeni kudzakwaniritsa zolinga zikuluzikulu m’tsogolo. Mwachitsanzo, ngati cholinga chanu chachikulu ndi kudzachita upainiya wokhazikika, bwanji osayamba panopa kuchita upainiya wothandiza mwezi uliwonse? Ngati cholinga chanu ndi kukhala mtumiki wothandiza, kodi mukhoza kuwonjezera nthawi imene mumalalikira komanso kuyendera odwala ndi achikulire mumpingo wanu? Zimene mungaphuzire panopa zingathandize kuti mudzachite mautumiki osiyanasiyana m’tsogolo. Muziyesetsa kuchita zonse zomwe mungathe pa utumiki uliwonse womwe mwapatsidwa.​—Aroma 12:11.

Muzisankha cholinga chenicheni chomwe mungathe kuchikwaniritsa (Onani ndime 18) *

18. Monga mmene tikuonera pa chithunzipa, kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Beverley?

18 Uchikulire sungalepheretse munthu kudziikira zolinga zauzimu n’kuzikwaniritsa. Taganizirani chitsanzo cha mlongo wina wa zaka 75 dzina lake Beverley. Iye anali ndi matenda ena ake aakulu omwe ankachititsa kuti azivutika kuyenda. Koma ankafuna atagwira nawo mokwanira ntchito yoitanira anthu ku Chikumbutso. Choncho anadziikira zolinga zimene ankafuna kuzikwaniritsa. Mlongoyo atakwaniritsa zolinga zakezo anasangalala kwambiri. Khama lake linalimbikitsa ena kuti adzipereke pa ntchito yolalikira. Yehova amayamikira ntchito imene abale ndi alongo athu achikulire amagwira, ngakhale kuti sangathe kuchita zambiri malinga ndi mmene zinthu zilili pa moyo wawo.​—Sal. 71:17, 18.

19. Kodi ndi zolinga zauzimu ziti zomwe tingadziikire?

19 Muzidziikira zolinga zimene mungazikwaniritse. Muziyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene angachititse kuti Yehova azikukondani. Muziphunzira maluso amene angachititse kuti Mulungu ndi gulu lake azikugwiritsani ntchito kwambiri. Muzifunafuna njira zimene mungathandizire abale ndi alongo anu mokwanira. * Mofanana ndi Timoteyo, Yehova adzakudalitsani ndipo ‘anthu onse adzaona kuti mukupita patsogolo.’​—1 Tim. 4:15.

NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa

^ Timoteyo anali mlaliki waluso wa uthenga wabwino. Komabe Paulo anamulimbikitsa kuti apitirizebe kupita patsogolo mwauzimu. Kumvera malangizowa, kukanachititsa kuti Yehova azimugwiritsa ntchito ndiponso azithandiza kwambiri abale ndi alongo ake. Kodi inunso mofanana ndi Timoteyo mukufunitsitsa kuti muzichita zambiri potumikira Yehova komanso Akhristu anzanu? Mosakayikira. Ndiye kodi ndi zolinga ziti zimene zingakuthandizeni? Nanga mungatani kuti mukhale nazo n’kumazikwaniritsa?

^ TANTHAUZO LA MAWU ENA: Zolinga zauzimu zikuphatikizapo zonse zomwe timayesetsa kuchita kuti tizitumikira Yehova mokwanira komanso kumusangalatsa.

^ Onani pamutu wakuti “Kutumikira Kumene Kukufunikira Ofalitsa Ambiri,” m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, mutu 10 ndime 6-9.

^ Onani phunziro 60 lakuti, “Pitirizani Kulimbitsa Ubwenzi Wanu ndi Yehova,” m’buku la Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale.

^ MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akuphunzitsa alongo awiri mmene angakonzere zinthu m’Nyumba ya Ufumu ndipo iwo akugwiritsa ntchito luso limene aphunziralo

^ MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo yemwe sangathe kuchoka panyumba akulalikira patelefoni ndipo akuitanira anthu ku Chikumbutso