Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 15

Kodi Tingaphunzire Chiyani pa Zozizwitsa za Yesu?

Kodi Tingaphunzire Chiyani pa Zozizwitsa za Yesu?

“Anayendayenda m’dziko, n’kumachita zabwino ndi kuchiritsa.”​—MAC. 10:38.

NYIMBO NA. 13 Khristu Ndi Chitsanzo Chathu

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Fotokozani mmene zinthu zinaliri pamene Yesu ankachita chozizwitsa chake choyamba.

 TAYEREKEZERANI kuti mukuona zimene zinachitika kumapeto kwa chaka cha 29 C.E., chakumayambiriro kwa utumiki wa Yesu. Yesu ndi mayi ake Mariya komanso ena mwa ophunzira ake, aitanidwa ku ukwati ku Kana, mudzi womwe unali kumpoto kwa Nazareti komwe ndi kwawo kwa Yesu. Mariya ndi mnzawo wa eni ukwatiwo ndipo akuthandizira kulandira alendo. Koma phwandolo lili mkati, pachitika vuto lina lomwe likhoza kuchititsa manyazi eni ukwatiwo komanso banja latsopanolo. Vinyo waathera. b N’kutheka kuti ku ukwatiwo kwabwera anthu ambiri kuposa omwe amayembekezeredwa. Mwamsanga, Mariya akuuza mwana wake kuti: “Vinyo waathera.” (Yoh. 2:1-3) Ndiye kodi Yesu akuchita chiyani? Iye akuchita chozizwitsa posandutsa madzi kukhala “vinyo wabwino.”​—Yoh. 2:9, 10.

2-3. (a) Kodi Yesu ankagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zake zochitira zozizwitsa? (b) Kodi tingapindule bwanji chifukwa choganizira zozizwitsa za Yesu?

2 Yesu anachitanso zozizwitsa zina zambiri pa utumiki wake. c Iye anagwiritsa ntchito mphamvu zomwe anali nazo zochitira zozizwitsa pothandiza anthu masauzande ambiri. Mwachitsanzo, taganizirani kuchuluka kwa anthu omwe anawathandiza pa zozizwitsa ziwiri zokha. Pamene anadyetsa amuna 5,000 komanso pa nthawi ina amuna 4,000, ngati titaphatikizapo akazi ndi ana omwe analiponso pa nthawiyi, n’kutheka kuti anadyetsa anthu 27,000. (Mat. 14:15-21; 15:32-38) Pa zochitika ziwiri zonsezi, Yesu anachiritsanso anthu ambiri odwala. (Mat. 14:14; 15:30, 31) Tangoganizani mmene anthu analili odabwa kuona Yesu akuwachiritsa mozizwitsa komanso kuwadyetsa.

3 Masiku ano tingaphunzire zambiri pa zozizwitsa zimene Yesu anachita. Munkhaniyi, tikambirana mfundo zingapo zolimbitsa chikhulupiriro zomwe tingaphunzirepo. Kenako tikambirana mmene tingatsanzirire kudzichepetsa komanso chifundo cha Yesu, makhalidwe omwe ankasonyeza akamachita zozizwitsazi.

ZIMENE TIMAPHUNZIRA ZOKHUDZA YEHOVA NDI YESU

4. Kodi zozizwitsa za Yesu zimatiphunzitsa mfundo zolimbitsa chikhulupiriro zokhudza ndani?

4 Zozizwitsa za Yesu zimatiphunzitsa mfundo zolimbitsa chikhulupiriro zokhudza iye komanso Atate wake. Ndipotu mphamvu zochitira zozizwitsazi, iye anazitenga kwa Yehova. Lemba la Machitidwe 10:38 limatiuza kuti: “Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera ndi mphamvu. Ndiponso kuti popeza Mulungu anali naye, anayendayenda m’dziko, n’kumachita zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Mdyerekezi.” Kumbukiraninso kuti zonse zimene Yesu ananena, kuchita komanso zozizwitsa zake, zinasonyeza bwino mmene Atate wake amaganizira komanso mmene amamvera. (Yoh. 14:9) Tiyeni tione mfundo zitatu zomwe tikuphunzira pa zozizwitsa za Yesu.

5. N’chiyani chinkachititsa kuti Yesu azichita zozizwitsa? (Mateyu 20:30-34)

5 Choyamba, Yesu ndi Atate wake amatikonda kwambiri. Ali padzikoli, Yesu anasonyeza kuti amakonda kwambiri anthu pogwiritsa ntchito mphamvu zake zodabwitsa pothandiza omwe ankavutika. Pa nthawi ina anthu awiri osaona anamufuulira kuti awathandize. (Werengani Mateyu 20:30-34.) Onani kuti Yesu “atagwidwa ndi chifundo,” anawachiritsa. Monga mmene agwiritsidwira ntchito palembali, mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “atagwidwa ndi chifundo,” amanena za chifundo chachikulu chomwe munthu amamva kuchokera pansi pa mtima. Chifundo chimenechi, chomwe chimasonyeza chikondi, ndi chimene chinachititsa Yesu kuti adyetse anjala komanso achiritse wakhate. (Mat. 15:32; Maliko 1:41) Sitikayikira kuti Yehova, yemwe ndi Mulungu “wachifundo chachikulu,” komanso Mwana wake amatikonda kwambiri ndipo amakhudzidwa tikamavutika. (Luka 1:78; 1 Pet. 5:7) Iwo ndi ofunitsitsa kudzachotsa mavuto onse omwe anthu amakumana nawo.

6. Kodi Mulungu wapereka mphamvu zotani kwa Yesu?

6 Chachiwiri, Mulungu wapatsa Yesu mphamvu zothetsa mavuto onse a anthu. Pochita zozizwitsa, Yesu anasonyeza kuti ali ndi mphamvu zothetsera mavuto omwe sitingathe kuwathetsa patokha. Mwachitsanzo, iye ali ndi mphamvu yotipulumutsa ku zimene zinayambitsa mavuto a anthu, zomwe ndi uchimo umene tinatengera komanso zotsatirapo zake monga matenda ndi imfa. (Mat. 9:1-6; Aroma 5:12, 18, 19) Zozizwitsa zomwe anachita, zimasonyeza kuti iye angathe kuchiritsa “matenda amtundu uliwonse” ngakhalenso kuukitsa akufa. (Mat. 4:23; Yoh. 11:43, 44) Alinso ndi mphamvu yotha kuletsa mphepo zamkuntho komanso kugonjetsa mizimu yoipa. (Maliko 4:37-39; Luka 8:2) N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova wapatsa Mwana wake mphamvu zochitira zimenezi.

7-8. (a) Kodi zozizwitsa za Yesu zimatitsimikizira za chiyani? (b) Kodi inuyo mumafunitsitsa kudzaona chozizwitsa chiti m’dziko latsopano?

7 Chachitatu, sitikayikira kuti malonjezo omwe tikuyembekezera mu Ufumu wa Mulungu adzakwaniritsidwa. Zozizwitsa zimene Yesu anachita ali munthu padzikoli, zimatiphunzitsa kuti monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzachita zambiri m’tsogolomu. Taganizirani zimene tikuyembekezera mu ulamuliro wa Khristu. Tidzakhala ndi thanzi labwino, chifukwa adzachotsa matenda alionse komanso kulumala kwa mtundu uliwonse. (Yes. 33:24; 35:5, 6; Chiv. 21:3, 4) Sitidzavutikanso ndi njala kapena zotsatirapo zoopsa za ngozi zam’chilengedwe. (Yes. 25:6; Maliko 4:41) Tidzasangalala kwambiri kulandira okondedwa athu akamadzaukitsidwa “m’manda achikumbutso.” (Yoh. 5:28, 29) Kodi inuyo mumafunitsitsa kudzaona chozizwitsa chiti m’dziko latsopano?

8 Akamachita zozizwitsa, Yesu ankadzichepetsa komanso ankasonyeza chifundo, makhalidwe omwe tiyenera kutsanzira. Tiyeni tione zitsanzo ziwiri ndipo tiyamba ndi kukambirana nkhani yokhudza mphwando la ukwati womwe unachitika ku Kana.

ZIMENE TIKUPHUNZIRA PA NKHANI YA KUDZICHEPETSA

9. Kodi Yesu anachita chiyani paphwando la ukwati? (Yohane 2:6-10)

9 Werengani Yohane 2:6-10. Vinyo atatha paphwando la ukwati, kodi unali udindo wa Yesu kuchitapo kanthu? Ayi. Palibe ulosi womwe unaneneratu kuti Mesiya adzapanga vinyo mozizwitsa. Koma tangoganizirani mmene mungamvere ngati zakumwa zitatha pa ukwati wanu. Yesu ayenera kuti anachitira chifundo banjali, makamaka mkwati ndi mkwatibwi ndipo sankafuna kuti iwo achite manyazi. Choncho monga tafotokozera kale, iye anachita chozizwitsa. Anasandutsa madzi okwana malita pafupifupi 390 kukhala vinyo wabwino kwambiri. N’kutheka kuti iye anasandutsa vinyo wochuluka chonchi kuti wina atsaleko kuti adzamugwiritse ntchito m’tsogolo kapena kuti banja latsopanolo ligulitse n’kupeza ndalama. Banjali liyenera kuti linayamikira kwambiri.

Muzitsanzira Yesu posadzitama pa zimene mwakwanitsa kuchita (Onani ndime 10-11) e

10. Kodi ndi mfundo zina zofunika ziti zopezeka munkhani ya pa Yohane chaputala 2? (Onaninso chithunzi.)

10 Taganizirani mfundo zina zofunika zopezeka munkhani ya pa Yohane chaputala 2. Kodi mwaona kuti si Yesu yemwe anadzaza madzi m’mitsuko ija? M’malo mochititsa kuti anthu aziganizira za iyeyo, iye anauza anthu omwe ankatumikira kuti adzaze madzi m’mitsukoyo. (Vesi 6 ndi 7) Ndipo atasandutsa madziwo kukhala vinyo, si iye amene anapititsa vinyo kwa woyang’anira phwando laukwati. M’malomwake anauza otumikirawo kuti achite zimenezo. (Vesi 8) Yesu sanatenge kapu ya vinyoyo n’kuonetsa alendo omwe anabwera pa ukwatiwo n’kumanena modzitama kuti, ‘Tangolawani vinyo yemwe ndapangayu!’

11. Kodi tikuphunzira chiyani pa chozizwitsa chimene Yesu anachita?

11 Kodi tikuphunzira chiyani pa chozizwitsa cha Yesu chosandutsa madzi kukhala vinyo? Tikuphunzirapo khalidwe la kudzichepetsa. Yesu sanadzitame chifukwa cha chozizwitsa chomwe anachita ndipotu sanadzitamepo pa zonse zomwe anachita. M’malomwake, modzichepetsa komanso mobwerezabwereza, ankapereka ulemerero wonse kwa Atate wake. (Yoh. 5:19, 30; 8:28) Tikamatsanzira Yesu pokhala odzichepetsa, sitingamadzitame chifukwa cha zimene takwanitsa kuchita. Choncho kaya tikuchita zotani potumikira Yehova, tisamadzitame chifukwa cha zimene tikuchitazo koma tizidzitama chifukwa choti tili ndi mwayi wotumikira Mulungu yemwe ndi wodabwitsa. (Yer. 9:23, 24) Tiyeni tizimupatsa ulemerero umene timayenera kumupatsa. Ndipotu palibe chabwino chilichonse chomwe tingachite popanda kuthandizidwa ndi Yehova.​—1 Akor. 1:26-31.

12. Kodi tingatsanzire kudzichepetsa kwa Yesu m’njira ina iti? Perekani chitsanzo.

12 Taganizirani njira ina yomwe tingasonyezere kuti ndife odzichepetsa ngati Yesu. Tiyerekeze kuti mkulu wathandiza mtumiki wothandiza wachinyamata kukonzekera nkhani yake ya onse yoyamba. Ndipo zotsatira zake n’zakuti m’bale wachinyamatayo wakamba nkhani yolimbikitsa yomwe yasangalatsa aliyense mumpingo. Pambuyo pa misonkhano munthu wina akuuza mkuluyo kuti: ‘M’bale wakutiwakuti wakamba nkhani yabwino kwambiri, si choncho?’ Kodi pamenepa mkuluyo ayenera kuyankha kuti: ‘Inde, ndinayesetsa kumuthandiza kwambiri’? Kapena kodi angayankhe modzichepetsa kuti: ‘Inde waikambadi bwino, inenso ndasangalala kwambiri’? Tikakhala odzichepetsa sitingafune kuti anthu azitilemekeza chifukwa cha zabwino zomwe tachitira ena. Timakhala okhutira chifukwa chodziwa kuti Yehova amaona komanso kuyamikira zimene timachita. (Yerekezerani ndi Mateyu 6:2-4; Aheb. 13:16) Ndipotu timasangalatsa Yehova tikamatsanzira Yesu pokhala odzichepetsa.​—1 Pet. 5:6.

ZIMENE TIKUPHUNZIRA PA NKHANI YOKHALA ACHIFUNDO

13. Kodi Yesu anaona chiyani pafupi ndi mzinda wa Naini, nanga kodi anachita chiyani? (Luka 7:11-15)

13 Werengani Luka 7:11-15. Yerekezerani kuti mukuona zomwe zatchulidwazi, zomwe zinachitika cham’katikati mwa utumiki wa Yesu. Iye wapita kumzinda wa Naini ku Galileya kufupi ndi ku Sunemu komwe mneneri Elisa anaukitsa mwana wa mayi wina zaka pafupifupi 900 m’mbuyomo. (2 Maf. 4:32-37) Pamene Yesu akufika pageti, akuona anthu atanyamula maliro akutuluka mumzindawo. N’zomvetsa chisoni kwambiri chifukwa mwana mmodzi yekhayo wa mayi ena amasiye wamwalira. Koma mayi oferedwawo sali okha. Anthu ambiri a mumzindawo ali nawo limodzi. Yesu akuimitsa anthuwo, ndipo akuwachitira mayiwo chinthu china chapadera powaukitsira mwana wawoyo. Ameneyu ndi munthu woyamba pa anthu atatu omwe mabuku a Uthenga Wabwino amafotokoza mwachindunji kuti Yesu anawaukitsa.

Muzitsanzira Yesu pochitira chifundo anthu omwe aferedwa (Onani ndime 14-16)

14. Kodi ndi mfundo zina zofunika ziti zomwe tikupeza munkhani ya pa Luka chaputala 7? (Onaninso chithunzi.)

14 Taganizirani mfundo zina zofunika zomwe zikupezeka munkhani ya pa Luka chaputala 7. Kodi mwaona kuti choyamba Yesu “anaona” mayi oferedwawo ndipo kenako “anawamvera chifundo”? (Vesi 13) Choncho ataona mayiwo akulira kwinaku akuyenda pafupi ndi thupi la mwana wawoyo, anawamvera chisoni kwambiri. Sikuti Yesu anangowamvera chisoni, koma anawasonyezanso chifundo. Iye analankhula ndi mayiwo, mosakayikira ndi mawu olimbikitsa, kuti: “Tontholani mayi.” Kenako anachitapo kanthu kuti awathandize. Anaukitsa mnyamatayo ndipo “anam’pereka kwa mayi ake.”​—Vesi 14, 15.

15. Kodi tingaphunzire chiyani pa chozizwitsa cha Yesu?

15 Kodi tingaphunzire chiyani pa chozizwitsa chomwe Yesu anachita poukitsa mwana wa mayi wamasiye? Tikuphunzirapo kuti tizichitira chifundo anthu omwe aferedwa. N’zoona kuti sitingaukitse anthu akufa ngati mmene Yesu anachitira. Koma mofanana ndi iye tikhoza kuchitira chifundo anthu omwe aferedwa ngati titamachita nawo chidwi. Tingawasonyeze chifundo polankhula komanso kuchita zomwe tingathe kuti tiwathandize ndiponso kuwatonthoza. d (Miy. 17:17; 2 Akor. 1:3, 4; 1 Pet. 3:8) Ngakhale mawu ochepa kapena zinthu zing’onozing’ono zosonyeza kukoma mtima zingawalimbikitse kwambiri.

16. Mogwirizana ndi chithunzichi, kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira mayi wina yemwe mwana wake anali atangomwalira kumene?

16 Taganizirani zimene zinachitikira mayi wina. Zaka zingapo zapitazo akuimba nyimbo pamisonkhano, mlongo anaona mayi wina akulira chapafupi. Nyimboyo inkatchula za kuukitsidwa kwa akufa ndipo mwana wamkazi wa mayiyo anali atangomwalira kumene. Atadziwa zimenezi, nthawi yomweyo mlongoyo anapita pamene panali mayiyo n’kumugwira m’khosi ndipo anaimbira limodzi nyimbo yonseyo. Patapita nthawi mayiyo ananena kuti: “Ndinaona kuti abale ndi alongo amandikonda kwambiri.” Iye anaona kuti anachita bwino kwambiri kupita kumisonkhano. Ndipo anati: “Ku Nyumba ya Ufumu n’kumene timalandira thandizo.” Tingakhale otsimikiza kuti Yehova amaona komanso amayamikira ngakhale zinthu zing’onozing’ono zomwe timachita posonyeza chifundo kwa amene aferedwa, omwe amakhala kuti ‘akudzimvera chisoni mumtima mwawo.’​—Sal. 34:18.

KUPHUNZIRA ZOZIZWITSA ZA YESU KUNGALIMBITSE CHIKHULUPIRIRO CHANU

17. Kodi taphunzira chiyani munkhaniyi?

17 Tingalimbikitsidwe kwambiri tikamaphunzira nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino zonena za zozizwitsa za Yesu. Nkhanizi zimatiphunzitsa kuti Yehova ndi Yesu amatikonda kwambiri. Zimatiphunzitsanso kuti Yesu ali ndi mphamvu yothetsa mavuto onse a anthu komanso kuti tingamakhulupirire kwambiri malonjezo a Ufumu omwe akwaniritsidwe posachedwapa. Tikamaphunzira nkhanizi, tingaganizire mmene tingatsanzirire makhalidwe a Yesu. Bwanji osakonza zoti muphunzire panokha kapena pa Kulambira kwa Pabanja zina mwa zozizwitsa zomwe Yesu anachita? Muziona zimene mukuphunzirapo komanso kuuza ena zimene mwaphunzirazo. Mukamachita zimenezi, mungakhale ndi nkhani zambiri zolimbikitsa zoti muzikambirana.​—Aroma 1:11, 12.

18. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

18 Chakumapeto kwa utumiki wake, Yesu anaukitsa munthu wachitatu pa anthu omwe Baibulo limafotokoza kuti iye anawaukitsa. Koma pa nthawiyi zinali zapadera chifukwa anaukitsa mnzake wapamtima komanso zinkaoneka ngati zosatheka kumuukitsa. Kodi tingaphunzire chiyani pa chozizwitsa chimenechi? Nanga tingatani kuti tizikhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso amenewa.

NYIMBO NA. 20 Munapereka Mwana Wanu Wobadwa Yekha

a Timasangalala kwambiri tikamawerenga za zozizwitsa zomwe Yesu anachita. Mwachitsanzo, iye analetsa mphepo yamkuntho panyanja, anachiritsa odwala komanso anaukitsa akufa. Nkhani zimenezi zinalembedwa m’Baibulo osati kuti zizingotisangalatsa koma zizitiphunzitsa. Tikamaziwerenga, timaphunziramo zinthu zimene zingachititse kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova ndi Yesu komanso kuona makhalidwe abwino amene tiyenera kukhala nawo.

b Katswiri wina wa Baibulo anafotokoza kuti: “Kumadera a kum’mawa kuchereza alendo kunali kofunika kwambiri ndipo wocherezayo ankafunika kuonetsetsa kuti alendowo apatsidwa zambiri kuposa zimene akufunikira. Ndipo makamaka paphwando laukwati, eni ukwatiwo ankafunika kupatsa alendo awo zakudya komanso zakumwa zambiri.”

c Mabuku a Uthenga Wabwino amafotokoza zozizwitsa zoposa 30 zimene Yesu anachita. Kuwonjezera pamenepo, iye anachitanso zozizwitsa zina zambiri zomwe Baibulo silinatchule chilichonse pachokhapachokha. Pa nthawi ina ‘anthu onse a mumzinda’ anabwera kwa iye ndipo “anachiritsa ambiri amene anali kudwala.”​—Maliko 1:32-34.

d Kuti mudziwe zina zimene munganene kapena kuchita kuti mutonthoze amene aferedwa, onani nkhani yakuti, “Muzitonthoza Anthu Amene Aferedwa, Ngati Mmene Yesu Anachitira” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2010.

e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yesu waimirira chakumbuyo pomwe banja latsopano ndi alendo awo akusangalala ndi vinyo wabwino.