Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 19

Kodi Tingatani Kuti Tizikhulupirira Kwambiri Lonjezo la Yehova la Dziko Latsopano?

Kodi Tingatani Kuti Tizikhulupirira Kwambiri Lonjezo la Yehova la Dziko Latsopano?

“Kodi [Yehova] ananenapo kanthu koma osachita?”—NUM. 23:19.

NYIMBO NA. 142 Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1-2. Kodi tiyenera kumachita chiyani poyembekezera dziko latsopano?

 TIMAYAMIKIRA kwambiri Yehova chifukwa cha lonjezo lake lakuti adzachotsa dziko loipali n’kubweretsa dziko latsopano. (2 Pet. 3:13) Ngakhale kuti sitikudziwa tsiku lenileni lomwe dziko latsopano libwere, umboni ukusonyeza kuti sipatenga nthawi yaitali lisanafike.​—Mat. 24:32-34, 36; Mac. 1:7.

2 Kaya takhala m’choonadi kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe tiyenera kumakhulupirira kwambiri lonjezo limeneli. Chifukwa chiyani? Chifukwa ngakhale chikhulupiriro cholimba chikhoza kufooka. Ndipotu mtumwi Paulo ananena kuti kusowa chikhulupiriro “ndi tchimo limene limatikola mosavuta.” (Aheb. 12:1) Kuti chikhulupiriro chathu chisafooke, nthawi zonse tiyenera kumaganizira kwambiri umboni wosonyeza kuti dziko latsopano libwera posachedwapa.​—Aheb. 11:1.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Munkhaniyi tikambirana njira zitatu zimene zingatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri lonjezo la Yehova lokhudza dziko latsopano, zomwe ndi: (1) kuganizira mozama zokhudza dipo, (2) kuganizira mphamvu za Yehova, komanso (3) kuchita zinthu zokhudza kulambira. Kenako tikambirana mmene uthenga wa Yehova wopita kwa Habakuku ungatithandizire kulimbitsa chikhulupiriro chathu masiku ano. Choyamba, tiyeni tione zina mwa zinthu zomwe zingachitike pa moyo wathu masiku ano, zimene zingafune kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba pa lonjezo la dziko latsopano.

ZINTHU ZOMWE ZIMAFUNA KUTI TIKHALE NDI CHIKHULUPIRIRO CHOLIMBA

4. Kodi ndi zosankha ziti zomwe zimafuna chikhulupiriro cholimba?

4 Tsiku lililonse timafunika chikhulupiriro cholimba kuti tisankhe zochita pa nkhani zosiyanasiyana monga maphunziro, zosangalatsa, anthu ocheza nawo, banja, ana komanso ntchito. Tingachite bwino kumadzifunsa kuti: ‘Kodi zimene ndimasankha zimasonyeza kuti sindikayikira kuti dziko loipali ndi losakhalitsa ndipo posachedwapa lilowedwa m’malo ndi dziko latsopano la Mulungu? Kapena kodi ndimasankha zinthu mofanana ndi anthu omwe amaona kuti imfa ndi mapeto a zonse?’ (Mat. 6:19, 20; Luka 12:16-21) Tingamasankhe zochita mwanzeru ngati timakhulupirira kuti dziko latsopano lili pafupi kwambiri.

5-6. N’chifukwa chiyani timafunika chikhulupiriro cholimba tikamakumana ndi mavuto? Perekani chitsanzo.

5 Timafunikanso kukhala ndi chikhulupiriro cholimba tikamakumana ndi mayesero. Tikhoza kuzunzidwa, kudwala matenda aakulu kapenanso kukumana ndi zinthu zina zofooketsa. Mwina poyamba tingamaone kuti titha kupirira mavuto athuwo. Koma nthawi zambiri mayesero ngati amenewo amatenga nthawi yaitali. Choncho tingafunike chikhulupiriro cholimba kuti tiwapirire komanso tipitirize kutumikira Yehova mosangalala.​—Aroma 12:12; 1 Pet. 1:6, 7.

6 Tikamakumana ndi mayeserowo, mwina tingayambe kuona kuti dziko latsopano la Yehova silidzabwera. Koma kodi zimenezi zingatanthauze kuti chikhulupiriro chathu chafooka? Osati kwenikweni. Taganizirani chitsanzo ichi: Ngati tili m’nyengo yozizira kwambiri, mwina tingamaone ngati nyengo yotentha siibwera. Koma kenako nyengo yotenthayo imabwera. Mofanana ndi zimenezi, ngati tafooka kwambiri mwina tingamaone kuti dziko latsopano silidzabwera. Koma ngati chikhulupiriro chathu ndi cholimba timadziwa kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa. (Sal. 94:3, 14, 15; Aheb. 6:17-19) Chikhulupirirocho chingatithandize kuti tizipitiriza kuika kulambira Yehova pamalo oyamba pa moyo wathu.

7. Kodi tiyenera kusamala ndi maganizo ati?

7 Timafunikanso chikhulupiriro cholimba kuti tizigwira ntchito yathu yolalikira. Anthu ambiri omwe timawalalikira amaona kuti “uthenga wabwino” wokhudza dziko latsopano la Mulungu, umanena za zinthu zomwe ndi zosatheka. (Mat. 24:14; Ezek. 33:32) Sitiyenera kutengera maganizo awo okayikirawa. Choncho tiyenera kupitiriza kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Tiyeni tione njira zitatu zomwe tingachitire zimenezi.

TIZIGANIZIRA MOZAMA ZOKHUDZA DIPO

8-9. Kodi kuganizira mozama za dipo kungalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu?

8 Njira imodzi yomwe tingalimbitsire chikhulupiriro chathu ndi kuganizira mozama zokhudza dipo. Dipo ndi lomwe limatitsimikizira kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa. Tikamaganizira mosamala chifukwa chake dipo linaperekedwa komanso zimene zinalowetsedwapo, timayamba kukhulupirira kwambiri kuti lonjezo la Mulungu loti tidzakhala ndi moyo wosatha m’dziko labwino lidzakwaniritsidwa. N’chifukwa chiyani tikutero?

9 Kodi panafunika chiyani kuti dipo liperekedwe? Yehova anatumiza Mwana wake wokondedwa woyamba kubadwa komanso mnzake wapamtima, kuti adzabadwe monga munthu wangwiro padzikoli. Ali padzikoli, Yesu anapirira mavuto osiyanasiyana. Kenako anazunzidwa komanso kufa imfa yowawa. Apatu Yehova analipira mtengo wokwera kwambiri. Mulungu wathu wachikondi sakanalola kuti Mwana wake avutike n’kufa pongofuna kuti tidzakhale ndi moyo wabwino koma waufupi. (Yoh. 3:16; 1 Pet. 1:18, 19) Chifukwa choti anapereka mtengo wokwera chonchi, Yehova adzaonetsetsa kuti tidzakhale ndi moyo wosatha m’dziko latsopano.

MUZIGANIZIRA MPHAMVU ZA YEHOVA

10. Mogwirizana ndi Aefeso 3:20, kodi Yehova angathe kuchita chiyani?

10 Njira yachiwiri yomwe tingalimbitsire chikhulupiriro chathu ndi kuganizira mphamvu za Yehova. Iye ali ndi mphamvu zokwaniritsira chilichonse chomwe walonjeza. N’zoona kuti kwa anthu, lonjezo la moyo wosatha m’dziko latsopano lingaoneke losatheka. Koma nthawi zambiri Yehova amalonjeza zinthu zomwe anthu sangathe kuchita. Iyetu ndi Mulungu Wamphamvuyonse. (Yobu 42:2; Maliko 10:27) Ndiye kodi sitingayembekezere kuti angamalonjeze zinthu zodabwitsa?​—Werengani Aefeso 3:20.

11. Perekani chitsanzo chimodzi cha malonjezo odabwitsa a Mulungu. (Onani bokosi lakuti “ Ena mwa Malonjezo Odabwitsa Omwe Anakwaniritsidwa.”)

11 Taganizirani zina mwa zinthu zooneka ngati zosatheka zomwe Yehova analonjeza anthu ake m’mbuyomu. Iye anatsimikizira Abulahamu ndi Sara kuti adzakhala ndi mwana ngakhale kuti anali atakalamba. (Gen. 17:15-17) Anauzanso Abulahamu kuti ana ake adzapatsidwa dziko la Kanani. M’zaka zambiri zimene ana a Abulahamu, Aisiraeli, anali akapolo ku Iguputo, ziyenera kuti zinkaoneka ngati lonjezoli silidzakwaniritsidwa. Koma linakwaniritsidwa. Patapita zaka zambiri, Yehova analengeza kuti Elizabeti yemwe anali wokalamba adzakhala ndi mwana. Iye anauzanso Mariya yemwe anali namwali kuti adzabereka Mwana wake wamwamuna. Yehova anali atalonjeza za kubwera kwa Mwanayu zaka masauzande m’mbuyomo m’munda wa Edeni ndipo anakwaniritsa lonjezoli.​—Gen. 3:15.

12. Kodi Yoswa 23:14 ndi Yesaya 55:10, 11, amatitsimikizira zotani zokhudza mphamvu za Yehova?

12 Tikamaganizira zimene Yehova anachitapo m’mbuyomu polonjeza komanso kukwaniritsa malonjezowo, timakhulupirira kwambiri kuti ali ndi mphamvu zobweretsa dziko latsopano. (Werengani Yoswa 23:14; Yesaya 55:10, 11.) Zimenezi zimatithandiza kukhala okonzeka kuthandiza ena kuti adziwe kuti lonjezo la dziko latsopano si maloto chabe. Ponena za kumwamba kwatsopano ndi dziko latsopano, Yehova mwiniyo ananena kuti: “Mawu awa ndi odalirika ndi oona.”​—Chiv. 21:1, 5.

MUZITANGANIDWA NDI ZINTHU ZOKHUDZA KULAMBIRA

MISONKHANO YA MPINGO

Kodi chilichonse mwa zinthu zokhudza kulambirazi chingalimbitse bwanji chikhulupiriro chanu? (Onani ndime 13)

13. Kodi misonkhano ya mpingo ingalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu? Fotokozani.

13 Chinthu chachitatu chomwe chingatithandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu ndi kuchita zinthu zokhudza kulambira. Mwachitsanzo, taganizirani mmene misonkhano ya mpingo imatithandizira. Anna, yemwe wakhala akuchita utumiki wa nthawi zonse m’njira zosiyanasiyana, ananena kuti: “Misonkhano imandithandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Ngakhale zitakhala kuti wokamba nkhani alibe luso lophunzitsa kapena sanafotokoze mfundo iliyonse yatsopano, nthawi zambiri ndimamva kanthu kenakake komwe kamandithandiza kumvetsa mfundo inayake ya choonadi ndipo izi zimalimbitsa chikhulupiriro changa.” b N’zosakayikitsa kuti timayamikiranso ndemanga zolimbitsa chikhulupiriro za abale ndi alongo.​—Aroma 1:11, 12; 10:17.

NTCHITO YOLALIKIRA

Kodi chilichonse mwa zinthu zokhudza kulambirazi chingalimbitse bwanji chikhulupiriro chanu? (Onani ndime 14)

14. Kodi kugwira nawo ntchito yolalikira kumalimbitsa bwanji chikhulupiriro chathu?

14 Timalimbitsanso chikhulupiriro chathu tikamagwira nawo ntchito yolalikira. (Aheb. 10:23) Barbara, yemwe wakhala akutumikira Yehova kwa zaka zoposa 70, ananena kuti: “Nthawi zonse ndimaona kuti ntchito yolalikira imandithandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Ndikamauza kwambiri ena zokhudza malonjezo osangalatsa a Yehova, m’pamenenso chikhulupiriro changa chimalimba kwambiri.”

KUPHUNZIRA PATOKHA

Kodi chilichonse mwa zinthu zokhudza kulambirazi chingalimbitse bwanji chikhulupiriro chanu? (Onani ndime 15)

15. Kodi kuphunzira patokha kumalimbitsa bwanji chikhulupiriro chathu? (Onaninso zithunzi.)

15 Palinso chinthu china chokhudza kulambira chimene chimalimbitsa chikhulupiriro chathu, chomwe ndi kuphunzira patokha. Susan amaona kuti kukhala ndi ndandanda yophunzirira kumamuthandiza kwambiri. Iye anati: “Lamlungu ndimakonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu wotsatira. Lolemba ndi Lachiwiri ndimakonzekera misonkhano yamkati mwa mlungu. Pa masiku otsalawo ndimakhala ndikufufuza nkhani inayake yomwe ndasankha.” Popeza kuti nthawi zonse amatsatira ndandanda yake yophunzirira, Susan akupitiriza kulimbitsa chikhulupiriro chake. Irene, yemwe wakhala akutumikira kulikulu lathu la padziko lonse kwa zaka zambiri, amaona kuti kuphunzira maulosi a m’Baibulo kumalimbitsa chikhulupiriro chake. Iye anati: “Zimandichititsa chidwi kuona kuti ngakhale mbali zing’onozing’ono zokhudza maulosi a Yehova, zimakwaniritsidwa.” c

“ADZAKWANIRITSIDWA NDITHU”

16. Kodi zimene Yehova anauza Habakuku zimatilimbikitsa bwanji masiku ano? (Aheberi 10:36, 37)

16 Atumiki ena a Yehova akhala akuyembekezera mapeto a dzikoli kwa nthawi yaitali. Kwa anthu, lonjezo la Mulunguli lingaoneke ngati likuchedwa kukwaniritsidwa. Yehova amadziwa mmene atumiki ake amamvera. Ndipotu anatsimikizira Habakuku kuti: “Uchite zimenezi pakuti masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu ndipo akuthamangira kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengereza, uziwayembekezerabe chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu. Iwo sadzachedwa.” (Hab. 2:3) Kodi Mulungu ananena mawuwa pongofuna kulimbikitsa Habakuku yekha? Kapena kodi angatilimbikitsenso ifeyo masiku ano? Mouziridwa, mtumwi Paulo anafotokoza mawu omwewa kwa Akhristu omwe akuyembekezera dziko latsopano. (Werengani Aheberi 10:36, 37.) Choncho ngakhale kuti lonjezo la Mulungu loti adzatipulumutsa lingaoneke ngati likuchedwa, sitingakayikire kuti ‘lidzakwaniritsidwa ndithu, silidzachedwa.’

17. Kodi mlongo wina amagwiritsa ntchito bwanji malangizo omwe Yehova anapatsa Habakuku?

17 Kwa zaka, atumiki ambiri a Yehova akhala akutsatira malangizo ake akuti “uziwayembekezerabe.” Mwachitsanzo, Mlongo Louise anayamba kutumikira Yehova mu 1939. Iye anati: “Pa nthawiyo ndinkaganiza kuti Aramagedo ifika ndisanamalize sukulu. Koma zimenezi sizinachitike. Pa zaka zonsezi, ndaona kuti chimene chimandithandiza ndi kuwerenga nkhani zomwe ndimangozitchula kuti ‘anthu omwe anadikira,’ monga nkhani ya Nowa, Abulahamu, Yosefe ndi enanso ambiri omwe anafunika kudikira kwa nthawi yaitali asanalandire zomwe Yehova anawalonjeza. Kupitiriza kuyembekezera kwathandiza ineyo komanso ena kuti tisamakayikire ngakhale pang’ono kuti dziko latsopano lili pafupi.” Anthu ambiri omwe atumikira Yehova kwa nthawi yaitali angavomereze zimenezi.

18. Kodi kuchita chidwi ndi zachilengedwe kungatithandize bwanji kuti tizikhulupirira kwambiri za dziko latsopano lomwe likubwera?

18 N’zoona kuti dziko latsopano silinafike. Komabe taganizirani zinthu zomwe mumaziona monga nyenyezi, mitengo, nyama komanso anthu anzanu. Palibe angakayikire kuti zinthuzi ndi zenizeni ngakhale kuti pa nthawi ina kunalibe. Zinthuzi zilipo chifukwa choti Yehova anazilenga. (Gen. 1:1, 26, 27) Mulungu wathu akufunanso kubweretsa dziko latsopano. Iye adzakwaniritsa cholinga chakechi. M’dziko latsopano anthu adzasangalala ndi moyo wosatha ali ndi thanzi labwino. Pa nthawi yake, Mulungu adzatipatsa dziko latsopano, ndipo mofanana ndi chilengedwe timaonachi, dzikolo lidzakhala lenileni.​—Yes. 65:17; Chiv. 21:3, 4.

19. Kodi mungalimbitse bwanji chikhulupiriro chanu?

19 Panopa muzichita chilichonse chomwe mungathe kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu. Muziyamikira kwambiri dipo. Muziganizira mphamvu za Yehova. Muzitanganidwa ndi zinthu zokhudza kulambira. Mukamachita zimenezo, mungakhale m’gulu la anthu amene “mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza monga cholowa chawo.”​—Aheb. 6:11, 12; Aroma 5:5.

NYIMBO NA. 139 Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano

a Anthu ambiri masiku ano sakhulupirira lonjezo la m’Baibulo lokhudza dziko latsopano. Iwo amaona kuti zimenezi ndi maloto chabe, kapena kuti zinthu zomwe sizingachitike. Komabe ifeyo sitikayikira kuti malonjezo onse a Yehova adzakwaniritsidwa. Ngakhale zili choncho, tiyenera kupitiriza kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Motani? Nkhaniyi ifotokoza mmene tingachitire zimenezi.

b Mayina ena asinthidwa.

c Nkhani zambiri zokhudza maulosi a m’Baibulo mungazipeze pa mutu wakuti “Prophecy” mu Watch Tower Publications Index. Mwachitsanzo onani nkhani yakuti, “Zimene Yehova Amalosera Zimakwaniritsidwa” mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2008.