NKHANI YOPHUNZIRA 16
“Mlongo Wako Adzauka”
“Yesu anamuuza [Marita] kuti: ‘Mlongo wako adzauka.’”—YOH. 11:23.
NYIMBO NA. 151 Iye Adzaitana
ZIMENE TIPHUNZIRE a
1. Kodi mnyamata wina anasonyeza bwanji kuti amakhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka?
MNYAMATA wina dzina lake Matthew ali ndi matenda aakulu ndipo wakhala akuchitidwa ma opaleshoni ambiri. Ali ndi zaka 7, tsiku lina iye ndi makolo ake ankaonera pulogalamu ya JW Broadcasting®. Chakumapeto kwa pulogalamuyo iwo anaonera vidiyo ya nyimbo yosonyeza anthu akulandira okondedwa awo omwe aukitsidwa. b Pulogalamuyo itatha, Matthew anapita pamene panali makolo ake n’kuwagwira manja, n’kunena kuti: “Mayi ndi bambo, mwaona, ngakhale nditamwalira ndidzaukitsidwa. Mukhoza kundidikira, zonse zidzakhala bwino.” Tangoganizani mmene makolowo anasangalalira kuona kuti mwana wawoyo amakhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka.
2-3. N’chifukwa chiyani n’zofunika kuti tiziganizira lonjezo lakuti akufa adzauka?
2 Tingachite bwino kuti nthawi ndi nthawi tiziganizira lonjezo la m’Baibulo lakuti akufa adzauka. (Yoh. 5:28, 29) Chifukwa chiyani? Chifukwa sitingadziwiretu nthawi imene tingadwale matenda aakulu kapena mwadzidzidzi munthu amene timamukonda angamwalire. (Mlal. 9:11; Yak. 4:13, 14) Kukhulupirira kuti akufa adzauka kungatithandize kuti tipirire mavuto ngati amenewa. (1 Ates. 4:13) Malemba amatitsimikizira kuti Atate wathu wakumwamba amatidziwa bwino ndipo amatikonda kwambiri. (Luka 12:7) Tangoganizani mmene Yehova Mulungu amatidziwira bwino kuti adzathe kutiukitsa ndi makhalidwe omwe tinali nawo komanso tikutha kukumbukira chilichonse. Ndipotu Yehova anasonyeza kuti amatikonda kwambiri potipatsa mwayi woti tidzakhale ndi moyo wosatha ngakhalenso kutiukitsa ngati titamwalira.
3 Munkhaniyi, choyamba tikambirana chifukwa chake tiyenera kukhulupirira lonjezo lakuti akufa adzauka. Kenako tikambirana nkhani ya m’Baibulo yolimbitsa chikhulupiriro yomwe ili ndi mawu a mulemba lomwe likutsogolera nkhaniyi, akuti: “Mlongo wako adzauka.” (Yoh. 11:23). Pomaliza tiphunzira zimene tingachite kuti tizikhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka.
CHIFUKWA CHAKE TIYENERA KUKHULUPIRIRA LONJEZO LAKUTI AKUFA ADZAUKA
4. Kuti tikhulupirire lonjezo, kodi timafunika kukhala otsimikiza za chiyani? Perekani chitsanzo.
4 Kuti tikhulupirire lonjezo linalake, tiyenera kukhala otsimikizira kuti amene akulonjezayo ndi wofunitsitsa komanso ali ndi mphamvu zochitira zimene akulonjezazo. Tiyerekeze kuti nyumba yanu yawonongeka kwambiri ndi mphepo ya mkuntho. Ndiyeno mnzanu wabwera ndipo akukulonjezani kuti, ‘Ndikuthandizani kumanganso nyumba yanuyi.’ Iye akunena zimenezi motsimikiza ndipo inuyo mwakhutira kuti akufuna kukuthandizani. Ngati ali ndi luso lomanga komanso ali ndi zida zonse zofunikira, mumadziwa kuti akhoza kukuthandizani. Choncho mukukhulupirira lonjezo lake. Ndiye kuli bwanji lonjezo la Mulungu lakuti adzaukitsa akufa? Kodi iye ndi wofunitsitsadi komanso ali ndi mphamvu zokwaniritsira lonjezo limenelo?
5-6. N’chifukwa chiyani sitingakayikire kuti Yehova amafunitsitsa kudzaukitsa akufa?
5 Kodi Yehova amafunitsitsa kudzaukitsa akufa? N’zosachita kufunsa. Iye anauzira anthu angapo kuti alembe m’Baibulo lonjezo lake lakuti adzaukitsa akufa. (Yes. 26:19; Hos. 13:14; Chiv. 20:11-13) Yehova akalonjeza, nthawi zonse amakwaniritsa zomwe walonjezazo. (Yos. 23:14) Ndipotu iye ndi wofunitsitsa kudzaukitsa anthu amene anamwalira. N’chifukwa chiyani tikutero?
6 Taganizirani zomwe Yobu analankhula. Iye sankakayikira kuti ngakhale atamwalira, Yehova adzalakalaka kumuonanso ali ndi moyo. (Yobu 14:14, 15) Yehova amafunitsitsanso kudzaukitsa atumiki ake onse amene anamwalira, kuti akhale athanzi komanso osangalala. Nanga bwanji za anthu mabiliyoni omwe anamwalira asanapeze mwayi wophunzira za Yehova? Mulungu wathu wachikondi amafunanso kudzawaukitsa. (Mac. 24:15) Iye amafuna kuti iwo akhale ndi mwayi wokhala anzake komanso kuti adzakhale ndi mwayi wokhala padzikoli mpaka kalekale. (Yoh. 3:16) Apatu n’zoonekeratu kuti Yehova amafunitsitsa kudzaukitsa akufa.
7-8. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova ali ndi mphamvu zoukitsa akufa?
7 Kodi Yehova alinso ndi mphamvu zotha kuukitsa akufa? Inde. Iye ndi “Wamphamvuyonse.” (Chiv. 1:8) Choncho ali ndi mphamvu zotha kugonjetsa mdani aliyense ngakhalenso imfa. (1 Akor. 15:26) Timalimbikitsidwa komanso kutonthozedwa chifukwa chodziwa zimenezi. Taganizirani zimene zinachitikira Mlongo Emma Arnold. Iye ndi banja lake anakumana ndi mayesero aakulu omwe anayesa chikhulupiriro chawo pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Pofuna kulimbikitsa mwana wake wamkazi chifukwa cha kuphedwa kwa okondedwa awo m’ndende zozunzirako anthu za Nazi, Emma anati: “Ngati anthu sadzaukitsidwa mpaka kalekale ndiye kuti imfa ingakhale yamphamvu kuposa Mulungu, si choncho?” Kunena zoona, palibe chinthu champhamvu kwambiri kuposa Yehova. Mulungu wamphamvuyonse yemwe analenga moyo angathenso kubwezeretsa moyo kwa amene anamwalira.
8 Chifukwa china chomwe chingatichititse kukhulupirira kuti Mulungu angathe kuukitsa anthu omwe anamwalira n’chakuti amakumbukira zinthu kuposa wina aliyense. Iye amatchula dzina la nyenyezi iliyonse. (Yes. 40:26) Amakumbukiranso anthu amene anamwalira. (Yobu 14:13; Luka 20:37, 38) Iye amakumbukiranso tinthu ting’onoting’ono tokhudza anthu omwe adzawaukitse kuphatikizapo makhalidwe ndi maonekedwe awo, zimene zinawachitikira pa moyo komanso zimene ankadziwa.
9. N’chifukwa chiyani mumakhulupirira lonjezo lakuti Yehova adzaukitsa akufa?
9 Ndi zomveka kukhulupirira lonjezo la Yehova lakuti adzaukitsa akufa chifukwa tikudziwa kuti amafunitsitsa komanso ali ndi mphamvu zokwaniritsira lonjezoli. Taganizirani chifukwa china chotichititsa kukhulupirira lonjezoli. Yehova anachitapo kale zimenezi. Kale, iye anapatsa amuna angapo okhulupirika kuphatikizapo Yesu, mphamvu zoukitsa akufa. Tsopano tiyeni tikambirane nkhani yokhudza mmodzi wa anthu omwe Yesu anawaukitsa yopezeka mu Yohane chaputala 11.
MNZAKE WA YESU ANAMWALIRA
10. Kodi n’chiyani chinachitika tsiku lina Yesu akulalikira kutsidya lina la Yorodano, nanga iye anachita chiyani? (Yohane 11:1-3)
10 Werengani Yohane 11:1-3. Yerekezerani kuti mukuona zimene zinachitika ku Betaniya chakumapeto kwa chaka cha 32 C.E. Yesu ali ndi anzake apamtima m’mudzi umenewu, omwe ndi Lazaro ndi azichemwali ake awiri Mariya ndi Marita. (Luka 10:38-42) Koma Lazaro akuyamba kudwala ndipo azichemwali akewo ali ndi nkhawa. Iwo akutumiza uthenga kwa Yesu yemwe ali kutsidya lina la mtsinje wa Yorodano, mtunda woyenda pafupifupi masiku awiri kuchokera ku Betaniya. (Yoh. 10:40) N’zomvetsa chisoni kuti Lazaro akumwalira uthenga utangofika kumene kwa Yesu. Ngakhale kuti Yesu wadziwa kuti mnzake wamwalira, iye akukhalabe komwe aliko kwa masiku ena awiri ndipo kenako akupita ku Betaniya. Choncho pamene akufika m’mudzimo, papita masiku 4 kuchokera pamene Lazaro wamwalira. Yesu akufuna kuchita chinthu chomwe chithandize anzakewo komanso kulemekeza Mulungu.—Yoh. 11:4, 6, 11, 17.
11. Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani pa mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi anzathu?
11 Nkhaniyi ikutiphunzitsa mmene tiyenera kumachitira zinthu ndi anzathu. Taganizirani izi: Pamene Mariya ndi Marita ankatumiza uthenga kwa Yesu sikuti ankamupempha kuti abwere ku Betaniya. Iwo anangomuuza kuti mnzake wapamtima akudwala. (Yoh. 11:3) Lazaro atamwalira, Yesu akanatha kumuukitsa ali kutali. Komabe anasankha kuti apite ku Betaniya kuti akakhale ndi anzake, Mariya ndi Marita. Kodi muli ndi mnzanu yemwe amakuthandizani popanda kumupempha? Ndiye kuti mumadziwa kuti mukhoza kumudalira kuti akuthandizani “pakagwa mavuto.” (Miy. 17:17) Mofanana ndi Yesu tiyeni tizikhala odalirika kwa anzathu. Tsopano tiyeni tipitirize nkhaniyi kuti tione zimene zikuchitika.
12. Kodi Yesu analonjeza chiyani Marita, nanga n’chifukwa chiyani iye ankayenera kukhulupirira lonjezolo? (Yohane 11:23-26)
12 Werengani Yohane 11:23-26. Marita wadziwa kuti Yesu akuyandikira ku Betaniya. Mwamsanga akupita kukakumana naye ndipo akunena kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.” (Yoh. 11:21) Zimenezi ndi zoona chifukwa Yesu akanatha kumuchiritsa Lazaro. Koma iye akuganiza zochita chinthu china chapadera kwambiri. Akumulonjeza kuti: “Mlongo wako adzauka.” Iye akuuzanso Marita chifukwa china chomuchititsa kukhulupirira lonjezoli kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo.” Zimenezi ndi zoona chifukwa Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zoukitsa akufa. M’mbuyomu iye anaukitsapo kamtsikana katangomwalira kumene komanso anaukitsapo mnyamata ndipo zikuonekanso kuti linali tsiku lomwe anamwaliralo. (Luka 7:11-15; 8:49-55) Koma kodi angaukitse munthu yemwe papita masiku 4 kuchokera pamene anamwalira ndipo thupi lake layamba kuwonongeka?
“LAZARO, TULUKA!”
13. Mogwirizana ndi Yohane 11:32-35, kodi Yesu anatani ataona Mariya ndi anthu ena akulira? (Onaninso chithunzi.)
13 Werengani Yohane 11:32-35. Taganizirani zimene zikuchitika pambuyo pake. Mariya yemwe ndi mchemwali wina wa Lazaro, akupita kukakumana ndi Yesu. Iye akubwerezanso zimene mchemwali wake ananena kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.” Iye ndi anthu omwe ali nawo ali ndi chisoni chachikulu. Poona komanso kumva anthuwo akulira, Yesu zikumukhudza kwambiri. Chifukwa chokonda kwambiri anzakewo, iye akugwetsa misozi. Amadziwa mmene zimapwetekera munthu yemwe umamukonda akamwalira. N’zoonekeratu kuti iye akufunitsitsa kuchotsa chomwe chawachititsa kuti akhale ndi chisoni.
14. Kodi tikuphunzira chiyani zokhudza Yehova pa zimene Yesu anachita ataona Mariya akulira?
14 Zimene Yesu anachita ataona Mariya akulira zikutiphunzitsa kuti Yehova ndi Mulungu wachifundo chachikulu. N’chifukwa chiyani tikutero? Monga momwe tinaonera munkhani yapita ija, Yesu amasonyeza ndendende mmene Atate ake amaganizira komanso mmene amamvera. (Yoh. 12:45) Choncho tikamawerenga kuti Yesu anamva chisoni kwambiri ataona anzake akulira ndipo nayenso analira tinganene kuti Yehova amakhudzikanso akationa tikulira chifukwa cha chisoni. (Sal. 56:8) Kodi zimenezi sizikukuchititsani kufuna kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu wathu wachifundoyu?
15. Mogwirizana ndi Yohane 11:41-44, kodi n’chiyani chinachitika kumanda a Lazaro? (Onaninso chithunzi.)
15 Werengani Yohane 11:41-44. Yesu akufika pamanda a Lazaro ndipo akuuza anthu kuti achotse mwala womwe atsekera pamandapo. Koma Marita akutsutsa zimenezi ponena kuti thupilo liyenera kuti layamba kununkha. Yesu akuyankha kuti: “Kodi sindinakuuze kuti ngati ukhulupirira udzaona ulemerero wa Mulungu?” (Yoh. 11:39, 40) Kenako Yesu akuyang’ana kumwamba n’kupemphera anthu onse akuona. Iye akufuna kupereka ulemerero wonse kwa Yehova pa zonse zomwe zichitike. Kenako Yesu akufuula kuti: “Lazaro, tuluka!” Ndipo Lazaro akutuluka m’mandamo. Apatu Yesu wachita zinthu zimene anthu ena amaona ngati n’zosatheka.—Onani nkhani yakuti, “N’chifukwa chiyani Yesu anatenga masiku anayi asanafike ku manda a Lazaro?” mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2008.
16. Kodi nkhani ya mu Yohane chaputala 11, imatithandiza bwanji kuti tizikhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka?
16 Nkhani ya mu Yohane chaputala 11, imatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka. N’chifukwa chiyani tikutero? Kumbukirani zimene Yesu anauza Marita kuti: “Mlongo wako adzauka.” (Yoh. 11:23) Mofanana ndi Atate wake, Yesu amafunitsitsa kuukitsa akufa ndipo ali ndi mphamvu zokwaniritsira lonjezo limeneli. Zimene anachita pogwetsa misozi zimasonyeza kuti iye amafunitsitsa kudzathetsa imfa komanso chisoni chimene imfa imabweretsa. Lazaro atatuluka m’mandamo, Yesu anasonyezanso kuti ali ndi mphamvu zotha kuukitsa akufa. Takumbukiraninso zimene Yesu anakumbutsa Marita kuti: “Kodi sindinakuuze kuti ngati ukhulupirira udzaona ulemerero wa Mulungu?” (Yoh. 11:40) Tili ndi zifukwa zomveka zokhulupirira kuti lonjezo la Mulungu lakuti akufa adzauka lidzakwaniritsidwa. Koma kodi tingatani kuti tizikhulupirira kwambiri lonjezo limeneli?
KODI TINGATANI KUTI TIZIKHULUPIRIRA KWAMBIRI KUTI AKUFA ADZAUKA?
17. Kodi tizikumbukira chiyani tikamawerenga nkhani za m’Baibulo za anthu omwe anaukitsidwa?
17 Muziwerenga komanso kuganizira nkhani za anthu omwe anaukitsidwa m’mbuyomu. Baibulo limatchula nkhani za anthu 8 omwe anaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo padzikoli. c Bwanji osaphunzira mosamala nkhani zimenezi? Mukamawerenga, muzikumbukira kuti nkhanizi ndi zokhudza anthu enieni omwe ndi amuna, akazi komanso ana. Muziona zimene mukuphunzirapo. Muziganizira mmene nkhani iliyonse ikusonyezera kuti Mulungu ndi wofunitsitsa komanso ali ndi mphamvu zoukitsa anthu. Koposa zonse muziganizira za kuukitsidwa kwa Yesu komwe ndi kofunika kwambiri. Kumbukirani kuti anthu ambiri anaona ndi maso Yesu ataukitsidwa ndipo zimenezi zimalimbitsa chikhulupiriro chathu.—1 Akor. 15:3-6, 20-22.
18. Kodi mungatani kuti muzipindula ndi nyimbo zokhudza chiyembekezo chakuti akufa adzauka? (Onaninso mawu a m’munsi.)
18 Muzimvetsera, kuimba komanso kuganizira “nyimbo zauzimu” zomwe zimanena za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa. d (Aef. 5:19) Nyimbo zimenezi zimatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri chiyembekezo chakuti akufa adzauka. Muzizimvetsera, kuziyeserera kuimba komanso kukambirana mawu ake pa kulambira kwanu kwa pabanja. Muziloweza mawu ake. Ndiye mukakumana ndi mayesero aakulu kapena munthu amene mumamukonda akamwalira, mzimu wa Yehova udzakuthandizani kukumbukira nyimbozi komanso kukutonthozani ndi kukupatsani mphamvu.
19. Kodi tingaganizire zinthu ziti zomwe zingadzachitike anthu akamadzaukitsidwa? (Onani bokosi lakuti “ Kodi Mudzawafunsa Chiyani?”)
19 Muziona zinthu m’maganizo mwanu. Yehova anatipatsa luso loti tizitha kudziona tili m’dziko latsopano. Mlongo wina anafotokoza kuti: “Kwa nthawi yayitali ndakhala ndikuyerekezera ndili m’dziko latsopano moti zimangokhala ngati ndikumva kununkhira kwa maluwa a m’Paradaiso.” Taganizirani mukukumana ndi amuna ndi akazi okhulupirika otchulidwa m’Baibulo. Kodi inuyo mukufuna kudzakumana ndi ndani? Mudzamufunsa mafunso otani? Yerekezeraninso kuti mukukumana ndi okondedwa anu omwe anamwalira ndipo mukuona zomwe zikuchitika pomwe mukukumanapo, monga mawu oyamba omwe mukulankhulana, mukukumbatirana komanso mukutulutsa misozi yachisangalalo.
20. Kodi tiyenera kutsimikiza kuchita chiyani?
20 Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha lonjezo lake lakuti akufa adzaukitsidwa. Sitingakayikire kuti lonjezoli lidzakwaniritsidwa chifukwa Yehova ndi wofunitsitsa ndiponso ali ndi mphamvu zochitira zimenezi. Tiyeni tikhale otsimikiza kuti tipitiriza kukhulupirira kwambiri chiyembekezo chamtengo wapatalichi. Tikamachita zimenezi tidzakhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu yemwe tingati akulonjeza wina aliyense wa ife kuti: ‘Okondedwa anu adzauka.’
NYIMBO NA. 147 Mulungu Watilonjeza Moyo Wosatha
a Ngati munthu yemwe mumamukonda anamwalira, mosakayikira mumalimbikitsidwa kwambiri ndi lonjezo lakuti akufa adzauka. Koma kodi mungafotokozere bwanji ena chifukwa chake mumakhulupirira lonjezo limeneli? Nanga mungatani kuti muzilikhulupirira kwambiri? Cholinga cha nkhaniyi ndi kuthandiza tonsefe kuti tizikhulupirira kwambiri lonjezoli.
b Vidiyo ya nyimboyi mutu wake ndi wakuti Dziko Latsopano Lili Pafupi ndipo inaonetsedwa mu pulogalamu ya JW Broadcasting ya November 2016.
c Onani bokosi lakuti, “Anthu 8 Otchulidwa M’Baibulo Amene Anaukitsidwa” mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2015, tsamba 4.
d Onani nyimbo zotsatirazi m’buku la nyimbo lakuti “Imbirani Yehova Mosangalala”: “Yerekezani Kuti Muli M’dziko Latsopano” (Nyimbo 139), “Yang’ananibe Pamphoto” (Nyimbo 144) komanso “Iye Adzaitana” (Nyimbo 151). Mungaonenso nyimbo za broadcasting izi pa jw.org, “Dziko Latsopano Lili Pafupi,” “The New World to Come,” ndi yakuti “Muone.”