Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungaphunzirenso Izi

Mungaphunzirenso Izi

Kodi mumapindula ndi malifalensi ofotokoza mavesi a m’Baibulo, opezeka mu Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani?

Malifalensi ofotokozera malembawa angakuthandizeni kuti muzifufuza mozama Mawu a Mulungu. Malifalensiwa angakhale ofotokoza mmene zinthu zinalili pamene zinthu zomwe zalembedwa pa vesi linalake zinkachitika, chifukwa chake vesilo linalembedwa, amene ankakhudzidwa ndi zinthu zofotokozedwa palembalo kapenanso tanthauzo lenileni la mawu ena ake.

Pa LAIBULALE YA PA INTANETI komanso pa JW Library, mungathe kupeza malifalensi a m’Buku Lofufuzira Nkhani mwachindunji pa mavesi a m’Baibulo. Mungapeze malifalensiwa m’Mabaibulo amene muli nawo pachipangizo chanu.

Mukamagwiritsa ntchito malifalensiwa muziyang’anitsitsa madeti ake. Nkhani zatsopano zimakhala pamwamba. Mukamatsika m’munsi mungapeze nkhani zakale zomwe mwina panopa mfundo zake zinasintha kamvedwe.

  • Pa LAIBULALE YA PA INTANETI malifalensiwa amapezeka mukangodina vesilo.

  • Kuti mupeze malifalensi a mavesi a m’Baibulo pa JW Library, muyenera kupanga dawunilodi Buku Lofufuzira Nkhani ndipo muzilipanganso dawunilodi mukaikidwa zinthu zatsopano. Mungachite zimenezi podina pamene alemba kuti “Download” pakagawo kophunzirira mukangotsegula chaputala cha Baibulo.