Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 18

Tizilimbikitsana Pamisonkhano ya Mpingo

Tizilimbikitsana Pamisonkhano ya Mpingo

“Tiyeni tiganizirane . . . , tilimbikitsane.”​—AHEB. 10:24, 25.

NYIMBO NA. 88 Ndidziwitseni Njira Zanu

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. N’chifukwa chiyani timayankha pamisonkhano?

 N’CHIFUKWA chiyani timapita kumisonkhano ya mpingo? Chifukwa chachikulu ndi kutamanda Yehova. (Sal. 26:12; 111:1) Timapitanso kumisonkhano n’cholinga choti tizilimbikitsana munthawi yovutayi. (1 Ates. 5:11) Tikakweza dzanja lathu n’kuyankha, timakwaniritsa zolinga ziwiri zimenezi.

2. Kodi ndi nthawi ziti pomwe timakhala ndi mwayi woyankha pamisonkhano yathu?

2 Mlungu uliwonse timakhala ndi mwayi woyankha pamisonkhano yathu. Mwachitsanzo, kumapeto kwa mlungu tikhoza kuyankha pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Pamisonkhano ya mkati mwa mlungu, tingayankhe pambali ya Mfundo Zothandiza, Phunziro la Baibulo la Mpingo komanso mbali zina zofunika kukambirana.

3. Kodi tingakumane ndi mavuto ati, nanga lemba la Aheberi 10:24, 25, lingatithandize bwanji?

3 Tonsefe timafuna kutamanda Yehova komanso kulimbikitsa Akhristu anzathu. Koma pa nkhani yopereka ndemanga, tingakumane ndi mavuto ena. Tingamachite mantha kuyankha, kapena tingamafunitsitse kuyankha koma mwina sitingapatsidwe mwayi woyankha monga mmene timafunira. Ndiye kodi tingatani pa mavuto amenewa? Timapeza yankho m’kalata imene mtumwi Paulo analembera Aheberi. Pofotokoza kufunika kosonkhana, iye ananena kuti tiziganizira kwambiri ‘zolimbikitsana.’ (Werengani Aheberi 10:24, 25.) Tikazindikira kuti ena angalimbikitsidwe ngakhale ndi yankho lachidule losonyeza chikhulupiriro chathu, sitingachite mantha kuyankha. Ndipo ngakhale kuti sitingapatsidwe mwayi woyankha pafupipafupi, tingakhale osangalala kuti enanso mumpingo akhala ndi mwayi wopereka ndemanga.​—1 Pet. 3:8.

4. Kodi tikambirana mfundo zitatu ziti munkhaniyi?

4 Munkhaniyi, choyamba tikambirana zimene tingachite kuti tizilimbikitsana mumpingo waung’ono, momwe simukhala anthu ambiri oyankha. Kenako tikambirana zomwe tingachite kuti tizilimbikitsana mumpingo waukulu, momwe anthu ambiri amaimika manja kuti ayankhe. Pomaliza tikambirana zomwe tingachite kuti mayankho athu azikhaladi olimbikitsa kwa ena.

TIZILIMBIKITSANA MUMPINGO WAUNG’ONO

5. Kodi tingalimbikitsane bwanji ngati tasonkhana anthu ochepa?

5 Mumpingo waung’ono kapena kagulu sipakhala anthu ambiri oimika manja kuti ayankhe. Nthawi zina wochititsa amafunika kuyembekezera kwa kanthawi munthu wina asanakweze dzanja kuti ayankhe. Zikatere misonkhano sisangalatsa kwenikweni ndipo sizingakhale zolimbikitsa. Ndiye kodi muyenera kuchita chiyani? Muzikhala wofunitsitsa kuimika dzanja pafupipafupi. Mukamachita zimenezi mungalimbikitse ena kuti nawonso aziyankha pafupipafupi.

6-7. Kodi mungachepetse bwanji mantha omwe mungakhale nawo pa nkhani yopereka ndemanga?

6 Koma bwanji ngati mumachita mantha kupereka ndemanga? Anthu ambirinso amamva choncho. Komabe kuti muzilimbikitsa kwambiri abale ndi alongo anu, bwanji osapeza njira zimene zingakuthandizeni kuchepetsa mantha pa nkhaniyi. Ndiye kodi mungachite bwanji zimenezi?

7 Mungapeze mfundo zina zimene zingakuthandizeni mu Nsanja za Olonda b za m’mbuyomu. Mwachitsanzo, muzikonzekera bwino. (Miy. 21:5) Mukamaidziwa bwino nkhaniyo, sizingakhale zovuta kuti muyankhepo. Komanso ndemanga zanu zizikhala zachidule. (Miy. 15:23; 17:27) Simungamachite mantha kwambiri kupereka ndemanga yachidule. Ndemanga yachidule, mwinanso yokhala ndi chiganizo chimodzi kapena ziwiri, ingakhale yosavuta kumvetsa kwa abale ndi alongo anu kusiyana ndi ndemanga yaitali yokhala ndi mfundo zambiri. Mukamayankha mwachidule komanso m’mawu anuanu, mumasonyeza kuti mwakonzekera bwino komanso mwamvetsa zimene mukuphunzirazo.

8. Kodi Yehova amaona bwanji zonse zomwe timayesetsa kuchita?

8 Bwanji ngati mwayesa kutsatira ena mwa malangizowa koma mukuona kuti mukuchitabe mantha kupereka ndemanga kawiri kapena kuposerapo? Musamakayikire kuti Yehova amayamikira kuti mukuyesetsa kuchita zomwe mungathe. (Luka 21:1-4) Komatu kuchita zomwe mungathe sikutanthauza kudzipanikiza. (Afil. 4:5) Muziona zimene mungakwanitse kuchita, muzidziikira cholinga choti muchite zimenezo ndipo muzipemphera kuti musachite mantha. Mungayambe ndi cholinga choti muzipereka ndemanga imodzi yachidule.

TIZILIMBIKITSANA MUMPINGO WAUKULU

9. Kodi ndi vuto liti lomwe tingakumane nalo mumpingo waukulu?

9 Ngati mpingo wanu uli ndi ofalitsa ambiri mungakumane ndi vuto lina. N’kutheka kuti abale ndi alongo ambiri amakonda kuyankha moti nthawi zambiri mukakweza dzanja sakulozani. Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Danielle amasangalala kupereka ndemanga pamisonkhano. c Iye amaona kuti imeneyi ndi mbali ya kulambira kwake, ndi njira yolimbikitsira ena komanso zimamuthandiza kuti mfundo za choonadi zikhazikike mumtima mwake. Koma atasamukira mumpingo waukulu sankapatsidwa mwayi woyankha pafupipafupi, ndipo nthawi zina misonkhano inkatheramo osayankha. Iye anati: “Ndinakhumudwa kwambiri ndipo ndinkaona kuti ndikuphonya mwayi winawake waukulu. Ndipo zikamachitika mobwerezabwereza umayamba kuona kuti mwina wochititsayo akuchitira dala.”

10. Kodi tingatani kuti tikhale ndi mwayi woyankha pamisonkhano?

10 Kodi munamvapo ngati mmene ankamvera Danielle? Ngati ndi choncho, mwina mungaganize kuti bola kungosiya kuyankha, n’kumangomvetsera misonkhanoyo. Koma simuyenera kusiya kuyesetsa kuti muyankhe pamisonkhano. Ndiye kodi mungatani? Mungachite bwino kumakonzekera ndemanga zingapo pamsonkhano uliwonse. Choncho ngati simunalozedwe kuti muyankhe kumayambiriro kwa phunziro, mungakhalebe ndi mwayi woyankha mkati mwa misonkhanoyo. Mukamakonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda, muziganizira mmene ndime iliyonse ikugwirizanirana ndi mutu wa nkhaniyo. Mukamachita zimenezo mungakhale ndi mfundo zoti muyankhe m’phunziro lonselo. Mungakonzekere kuti mukayankhe pa ndime zimene zikufotokoza mfundo zozama za choonadi, zomwe ndi zovuta kuzifotokoza. (1 Akor. 2:10) Chifukwa chiyani? Chifukwa mwina pangakhale anthu ochepa oimika manja kuti ayankhe pa mbali imeneyi. Koma bwanji ngati pambuyo potsatira malangizo amenewa pamisonkhano ingapo mwaonabe kuti simunapatsidwe mwayi woyankha? Misonkhano isanayambe mungauze amene akuchititsa phunzirolo funso limene mukufuna kuyankha.

11. Kodi lemba la Afilipi 2:4 limatilimbikitsa kuti tizichita chiyani?

11 Werengani Afilipi 2:4. Mouziridwa, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti aziganiziranso zofuna za ena. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji malangizo amenewa pamisonkhano? Tizikumbukira kuti mofanana ndi ifeyo, enanso akufuna kuyankha.

Monga mmene timaperekera mwayi kwa ena kuti nawonso azilankhulapo tikamacheza, tizilola enanso kupereka ndemanga pamisonkhano (Onani ndime 12)

12. Kodi ndi njira yabwino iti yomwe tingalimbikitsire ena pamisonkhano? (Onaninso chithunzi.)

12 Taganizirani izi: Pamene mukucheza ndi anzanu, kodi mumangolankhula nokha osawapatsako mpata woti alankhulepo? Ayi, simungachite zimenezo. Mumafuna kuti nawonso azilankhulapo. Mofanana ndi zimenezi, pamisonkhano timafuna kuti anthu ambiri azipereka ndemanga. Ndipotu imodzi mwa njira zabwino kwambiri zolimbikitsira abale ndi alongo athu ndi kuwapatsa mpata woti afotokoze zokhudza chikhulupiriro chawo. (1 Akor. 10:24) Tiyeni tione mmene tingachitire zimenezi.

13. Kodi tingatani kuti tipatse anthu ambiri mpata woyankha?

13 Mwa zina, tingapereke ndemanga yachidule, zomwe zingapereke mpata kwa ena kuti ayankhepo. Akulu ndi ofalitsa ena odziwa zambiri angapereke chitsanzo pa nkhaniyi. Ngakhale pamene yankho lanu lili lalifupi, muzipewa kutchula mfundo zambiri. Ngati mutatchula mfundo zonse za mundime, anthu ena angasowe zoti alankhulepo. Mwachitsanzo, mundime ino mwatchulidwa mfundo ziwiri, zomwe ndi kupereka ndemanga zachidule komanso kupewa kufotokoza mfundo zambirimbiri. Choncho ngati mukhale woyamba kupereka ndemanga pa ndimeyi, bwanji osangotchula mfundo imodzi yokha?

Kodi ndi pa nthawi iti pamisonkhano pomwe tingasankhe kuti tisakweze dzanja lathu? (Onani ndime 14) f

14. N’chiyani chingatithandize kudziwa kuti tikufunika kukweza dzanja pafupipafupi motani? (Onaninso chithunzi.)

14 Muzichita zinthu mozindikira pofuna kusankha kuti muyankhe pafupipafupi motani. Ngati titamakweza dzanja lathu pafupipafupi, wochititsayo angamakakamizike kuti atitchule mobwerezabwereza ngakhale kuti ena sanayankhe. Zimenezi zingachititse kuti anthu ena asiye kuimika manja.​—Mlal. 3:7.

15. (a) Kodi tiyenera kutani ngati sitinapatsidwe mwayi woyankha? (b) Kodi wochititsa phunziro angasonyeze bwanji kuti amaganizira aliyense? (Onani bokosi lakuti, “ Ngati Mukuchititsa.”)

15 Ofalitsa ambiri akakweza manja kuti ayankhe pa phunziro, sitingamakhale ndi mwayi woti tiziyankha pafupipafupi ngati mmene timafunira. Ndipotu nthawi zina wochititsa sangatiloze. Zimenezi zingakhale zokhumudwitsa komabe sitiyenera kukhumudwa tikapanda kutchulidwa.​—Mlal. 7:9.

16. Kodi tingalimbikitse bwanji ena amene apereka ndemanga?

16 Ngati simunakwanitse kupereka ndemanga maulendo angapo ngati mmene mumafunira, bwanji osamvetsera mwatcheru ena akamayankha n’cholinga choti muwayamikire pambuyo pamisonkhano? Abale ndi alongo anu angalimbikitsidwe mukawayamikira ngati mmene akanalimbikitsidwira ndi ndemanga zanu. (Miy. 10:21) Kuyamikirana ndi njira imene timalimbikitsirana.

NJIRA ZINA ZOLIMBIKITSIRANA

17. (a) Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti akonzekere ndemanga zoyenera? (b) Mogwirizana ndi vidiyo, kodi ndi mfundo 4 ziti zomwe zingatithandize tikamakonzekera kukapereka ndemanga? (Onaninso mawu a mmunsi.)

17 Kodi ndi njira zinanso ziti zomwe tingalimbikitsirane pamisonkhano? Ngati ndinu makolo, muzithandiza ana anu kukonzekera ndemanga zogwirizana ndi msinkhu wawo. (Mat. 21:16) Nthawi zina pamisonkhano timaphunzira nkhani zikuluzikulu monga zokhudza mavuto a m’banja kapena makhalidwe. Komabe pangathe kukhala ndime imodzi kapena ziwiri zomwe mwana akhoza kuyankhapo. Komanso muzithandiza ana anu kumvetsa chifukwa chake sangalozedwe nthawi iliyonse yomwe akweza dzanja. Kuwafotokozera zimenezi kungawathandize kuti asamakhumudwe ena akalozedwa m’malo mwa iwowo.​—1 Tim. 6:18. d

18. Popereka ndemanga, kodi tingapewe bwanji kuchititsa ena kuti aziganizira kwambiri zokhudza ifeyo? (Miyambo 27:2)

18 Tonsefe tingakonzekere ndemanga zomwe zingalemekeze Yehova komanso zingalimbikitse Akhristu anzathu. (Miy. 25:11) Ngakhale kuti nthawi zina tingafotokoze mwachidule zimene zinatichitikirapo, tizipewa kulankhula kwambiri zokhudza ifeyo. (Werengani Miyambo 27:2; 2 Akor. 10:18) M’malomwake, tiziyesetsa kuganizira kwambiri zokhudza Yehova, Mawu ake komanso anthu ake monga gulu. (Chiv. 4:11) Komabe nthawi zina funso la ndime lingafune kuti tifotokoze zinthu zokhudza ifeyo ndipo sikulakwa kutero. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene tione mundime yotsatirayi.

19. (a) Kodi zotsatirapo zake zingakhale zotani tikamaganizira ena tikakhala pamisonkhano? (Aroma 1:11, 12) (b) Kodi inuyo n’chiyani chimakusangalatsani pa nkhani yopereka ndemanga pamisonkhano?

19 Ngakhale kuti palibe malamulo okhudza mmene tiyenera kuperekera ndemanga, tonsefe tingayesetse kuti ndemanga zathu zizikhala zolimbikitsa. Zimenezi zingatanthauze kuti nthawi zina tingafunike kuti tizipereka ndemanga pafupipafupi. Kapenanso zingatanthauze kukhala okhutira ndi mwayi wopereka ndemanga umene wapezeka komanso kumasangalala kuti ena apeza mwayi wopereka ndemanga. Tikamaganiziranso zofuna za ena tikakhala pamisonkhano, tonsefe ‘tingalimbikitsane.’​—Werengani Aroma 1:11, 12.

NYIMBO NA. 93 Mudalitse Msonkhano Wathu

a Timalimbikitsana tikamayankha pamisonkhano. Komabe ena amachita mantha kupereka ndemanga. Ena amakonda kupereka ndemanga koma amafuna kuti azitchulidwa pafupipafupi. Mulimonse mmene zingakhalire, kodi tingasonyeze bwanji kuti timaganizirana n’cholinga choti aliyense azilimbikitsidwa? Nanga kodi tingatani kuti tizipereka ndemanga zomwe zingalimbikitse abale ndi alongo athu pa chikondi ndi ntchito zabwino? Nkhaniyi ifotokoza zimenezi.

b Kuti mupeze mfundo zina zowonjezereka, onani Nsanja ya Olonda ya January 2019 tsamba 8-13, komanso ya September 1, 2003, tsamba 19-22.

c Dzina lasinthidwa.

f MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale yemwe waperekapo kale ndemanga yake akupatsa mwayi ena kuti ayankhepo.