Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 17

Yehova Adzakuthandizani Kupirira Mavuto Osayembekezereka

Yehova Adzakuthandizani Kupirira Mavuto Osayembekezereka

“Masoka a munthu wolungama ndi ochuluka, koma Yehova amamupulumutsa ku masoka onsewo.”​—SAL. 34:19.

NYIMBO NA. 44 Pemphero la Munthu Wovutika

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi sitikayikira chiyani?

 MONGA anthu a Yehova, timadziwa kuti iye amatikonda ndipo amafuna kuti tizisangalala ndi moyo wabwino kwambiri panopa. (Aroma 8:35-39) Sitikayikiranso kuti nthawi zonse tikamatsatira mfundo za m’Baibulo, zinthu zimatiyendera bwino. (Yes. 48:17, 18) Koma bwanji ngati takumana ndi mavuto omwe sitimayembekezera?

2. Kodi tingakumane ndi mavuto otani, nanga angachititse kuti tizidzifunsa mafunso ati?

2 Atumiki onse a Yehova amakumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, wachibale wathu angatikhumudwitse, tingadwale matenda aakulu omwe angachititse kuti tisamachite zambiri potumikira Yehova, kapenanso tingakumane ndi zotsatirapo za ngozi zam’chilengedwe. Tingathenso kuzunzidwa chifukwa cha zimene timakhulupirira. Tikakumana ndi mavuto ngati amenewa tingamadzifunse kuti: ‘N’chifukwa chiyani zimenezi zikundichitikira? Kodi ndalakwitsa chinachake? Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova sakundidalitsa?’ Kodi munayamba mwamvapo chonchi? Ngati ndi choncho musataye mtima. Atumiki ambiri okhulupirika a Yehova anamvaponso choncho.​—Sal. 22:1, 2; Hab. 1:2, 3.

3. Kodi tikuphunzira chiyani pa lemba la Salimo 34:19?

3 Werengani Salimo 34:19. Taonani mfundo ziwiri zofunika zomwe tikupeza mu salimoli: (1) Anthu olungama amakumana ndi mavuto. (2) Yehova amatipulumutsa tikamakumana ndi mayesero. Ndiye kodi iye amatipulumutsa bwanji? Njira imodzi ndi kutithandiza kuti tiziona zinthu moyenera m’dzikoli. Ngakhale kuti Yehova amatilonjeza kuti tizisangalala tikamamutumikira, sanena kuti sitizikumana ndi mavuto panopa. (Yes. 66:14) Iye amatilimbikitsa kuti tiziganizira za nthawi imene tidzakhale ndi moyo umene amafuna kuti tidzasangalale nawo mpaka kalekale. (2 Akor. 4:16-18) Koma panopa iye amatithandiza kuti tipitirize kumutumikira tsiku lililonse.​—Maliro 3:22-24.

4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Tiyeni tikambirane zimene tingaphunzire pa zitsanzo za atumiki okhulupirika a Yehova otchulidwa m’Baibulo komanso a masiku ano. Monga momwe tionere, tingakumane ndi mavuto omwe sitimayembekezera. Koma ngati timadalira Yehova, iye sadzalephera kutithandiza. (Sal. 55:22) Tikamakambirana zitsanzo zimenezi muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikanatani ndikanakumana ndi zoterezi? Kodi zitsanzo zimenezi zikundithandiza bwanji kuti ndizidalira Yehova? Kodi ndi mfundo ziti zimene ndingagwiritse ntchito pa moyo wanga?’

ANTHU OTCHULIDWA M’BAIBULO

Kwa zaka 20, Yehova anadalitsa Yakobo pamene ankagwira ntchito mwakhama kwa amalume ake a Labani, omwe anali achinyengo (Onani ndime 5)

5. Kodi Yakobo anakumana ndi mavuto otani chifukwa cha Labani? (Onani chithunzi chapachikuto.)

5 Atumiki a Yehova otchulidwa m’Baibulo ankakumana ndi mavuto omwe sankawayembekezera. Taganizirani chitsanzo cha Yakobo. Bambo ake anamulamula kuti akwatire mmodzi wa ana aakazi a Labani, wachibale wawo yemwe ankalambira Yehova ndipo iwo anamutsimikizira kuti Yehova adzamudalitsa kwambiri. (Gen. 28:1-4) Choncho Yakobo anachita zinthu zoyenera. Iye anachoka ku Kanani kupita kwawo kwa Labani, yemwe anali ndi ana aakazi awiri, Leya ndi Rakele. Yakobo anakonda Rakele mwana wamng’ono wa Labani ndipo anavomera kuti agwirira ntchito bambo akewo zaka 7 kuti amukwatire. (Gen. 29:18) Koma zinthu sizinachitike mmene Yakobo ankaganizira. Labani anamupusitsa pomupatsa mwana wake wamkulu Leya kuti amukwatire. Labani analola kuti Yakobo akwatire Rakele patatha mlungu umodzi koma ngati angamugwirirenso ntchito zaka zina 7. (Gen. 29:25-27) Labani sankachitanso zinthu mwachilungamo ndi Yakobo. Iye anachitira Yakobo zinthu zopanda chilungamozi kwa zaka 20.​—Gen. 31:41, 42.

6. Kodi ndi mavuto ena ati omwe Yakobo anapirira?

6 Yakobo anapirira mavuto enanso. Iye anali ndi banja lalikulu koma si nthawi zonse pamene ana ake ankagwirizana. Iwo anafika mpaka pogulitsa m’bale wawo Yosefe ku ukapolo. Awiri mwa ana a Yakobo, Simiyoni ndi Levi anachititsa manyazi banja lawo komanso ananyozetsa dzina la Yehova. Kuwonjezera pamenepo mkazi wokondedwa wa Yakobo, Rakele, anamwalira pamene ankabereka mwana wawo wachiwiri. Komanso chifukwa cha njala yaikulu, Yakobo anakakamizika kusamukira ku Iguputo ali wokalamba.​—Gen. 34:30; 35:16-19; 37:28; 45:9-11, 28.

7. Kodi Yehova anamusonyeza bwanji Yakobo kuti ankasangalala naye?

7 Pa zinthu zonse zomwe zinamuchitikira, Yakobo sanasiye kukhulupirira Yehova komanso malonjezo ake. Nayenso Yehova anamusonyeza kuti ankasangalala naye. Mwachitsanzo, ngakhale kuti Labani anamuchitira zinthu zopanda chilungamo, Yehova anadalitsa Yakobo pomupatsa chuma chambiri. Ndipo tangoganizani mmene iye anayamikirira Yehova atakumananso ndi Yosefe mwana wake, yemwe ankaganiza kuti anafa kalekale. Yakobo ankakwanitsa kupirira mavuto omwe ankakumana nawo chifukwa anali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Gen. 30:43; 32:9, 10; 46:28-30) Ngati ifenso titakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, tingathe kupirira mavuto osayembekezereka amene tingakumane nawo.

8. Kodi Mfumu Davide inkafuna kuchita chiyani?

8 Mfumu Davide sikanakwanitsa kuchita zonse zomwe inkafuna potumikira Yehova. Mwachitsanzo, Davide ankafunitsitsa kumangira Mulungu wake kachisi. Iye anafotokozera mneneri Natani zimene ankafuna kuchitazo. Poyankha Natani anati: “Chitani chilichonse chimene chili mumtima mwanu, chifukwa Mulungu woona ali nanu.” (1 Mbiri 17:1, 2) Mawu amenewa ayenera kuti anamulimbikitsa kwambiri Davide. N’kutheka kuti nthawi yomweyo iye anayamba kukonzekera ntchito yaikuluyo.

9. Kodi Davide anatani atamva nkhani yokhumudwitsa?

9 Pasanapite nthawi, mneneri wa Yehova uja anabwera ndi nkhani yokhumudwitsa. “Usiku umenewo,” Yehova anauza mneneri Natani kuti Davide si amene adzamange kachisi koma mmodzi wa ana ake. (1 Mbiri 17:3, 4, 11, 12) Kodi Davide anatani atamva uthengawu? Anasintha pang’ono zimene ankafuna kuchita. Anayamba kusonkhanitsa chuma komanso zinthu zomwe mwana wake Solomo akanafunikira kuti amange kachisiyo.​—1 Mbiri 29:1-5.

10. Kodi Yehova anadalitsa bwanji Davide?

10 Atangouza kumene Davide kuti si iye amene adzamange kachisi, Yehova anachita naye pangano. Iye analonjeza Davide kuti mmodzi mwa ana obadwira mumzere wake adzalamulira mpaka kalekale. (2 Sam. 7:16) Tangoganizani mmene Davide adzasangalalire m’dziko latsopano kudziwa kuti akusangalala ndi moyo mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu, Mfumu yochokera m’banja lake. Nkhaniyi ikutithandiza kuona kuti ngakhale kuti sitingathe kuchita zonse zomwe tikufuna potumikira Yehova, Mulungu wathu angatisungire madalitso ena omwe sitimawayembekezera.

11. Kodi Akhristu a mu nthawi ya atumwi analimbikitsidwa bwanji ngakhale kuti Ufumu sunafike pa nthawi imene ankayembekezera? (Machitidwe 6:7)

11 Akhristu a mu nthawi ya atumwi ankakumana ndi mavuto osayembekezereka. Mwachitsanzo, iwo ankayembekezera mwachidwi kubwera kwa Ufumu wa Mulungu koma sankadziwa kuti ubwera liti. (Mac. 1:6, 7) Ndiye kodi anatani? Ankatanganidwa ndi ntchito yolalikira. Pamene uthenga wabwino unkafalikira, iwo anaona umboni wakuti Yehova akudalitsa khama lawo.​—Werengani Machitidwe 6:7.

12. Kodi Akhristu a mu nthawi ya atumwi anachita chiyani kutagwa njala?

12 Pa nthawi ina kunagwa njala yaikulu “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mac. 11:28) Zimenezi zinakhudzanso Akhristu oyambirira. Tangoganizani mmene anavutikira chifukwa cha njala yaikuluyo. N’zosakayikitsa kuti mitu ya mabanja inkadera nkhawa kuti izipezera bwanji zofunika mabanja awo. Nanga bwanji za achinyamata omwe anali ndi zolinga zofuna kuwonjezera utumiki wawo? Kodi mwina iwo anayamba kuona kuti aimitse kaye zolinga zawo? Ngakhale kuti panali mavutowa, Akhristuwo anasintha zinthu mogwirizana ndi mmene zinalili pa moyo wawo. Iwo anapitiriza kulalikira mmene akanathera ndipo anasangalala kugawira Akhristu anzawo a ku Yudeya zinthu zomwe anali nazo.​—Mac. 11:29, 30.

13. Kodi Akhristu anaona madalitso otani pa nthawi yanjala?

13 Kodi Akhristu anaona madalitso otani pa nthawi yanjala? Omwe anapatsidwa zinthu zofunika anaona kuti Yehova akuwathandiza. (Mat. 6:31-33) Iwo ayenera kuti anayamba kugwirizana kwambiri ndi Akhristu omwe anawathandizawo. Ndipo amene anapereka zinthu zawo kapena kugwira nawo ntchito yothandizayo, anapeza chimwemwe chimene chimabwera chifukwa cha kupatsa. (Mac. 20:35) Yehova anawadalitsa onsewa chifukwa chochita zinthu mogwirizana ndi mmene zinasinthira pa moyo wawo.

14. Kodi n’chiyani chimene chinachitikira Baranaba ndi mtumwi Paulo, nanga zotsatirapo zake zinali zotani? (Machitidwe 14:21, 22)

14 Nthawi zambiri Akhristu a mu nthawi ya atumwi ankazunzidwa mwinanso pa nthawi yomwe samayembekezera. Taganizirani zimene zinachitikira Baranaba ndi mtumwi Paulo pamene ankalalikira ku Lusitala. Poyamba iwo analandiridwa bwino ndi anthu omwe ankawamvetsera. Koma pambuyo pake otsutsa “anakopa anthuwo” ndipo ena mwa iwo anaponya Paulo miyala n’kumusiya atatsala pang’ono kufa. (Mac. 14:19) Koma Baranaba ndi Paulo anapitiriza kulalikira kudera lina. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Iwo anathandiza “anthu angapo kuti akhale ophunzira” ndipo zolankhula komanso chitsanzo chawo chinalimbikitsa Akhristu anzawo. (Werengani Machitidwe 14:21, 22.) Ambiri anapindula chifukwa chakuti Baranaba ndi Paulo sanabwerere m’mbuyo ngakhale pamene anazunzidwa mosayembekezereka. Ifenso tidzadalitsidwa ngati sitingasiye kugwira ntchito imene Yehova watiuza kuti tichite.

ANTHU A MU NTHAWI YATHU

15. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha M’bale A. H. Macmillan?

15 Chisanafike chaka cha 1914, anthu a Yehova ankayembekezera mwachidwi kuti pachitika zinazake. Mwachitsanzo, taganizirani zomwe zinachitikira M’bale A. H. Macmillan. Mofanana ndi ambiri pa nthawiyo, M’bale Macmillan ankaganiza kuti posakhalitsa alandira mphoto yawo yomwe ndi kupita kumwamba. Munkhani yomwe anakamba mu September 1914, anati: “N’kutheka kuti imeneyi ndi nkhani yanga yomaliza kukamba.” Komabe imeneyi sinali nkhani yawo yomaliza. Pambuyo pake M’bale Macmillan analemba kuti: “N’kutheka kuti ambiri a ife tinapupuluma kuganiza kuti tipita kumwamba nthawi yomweyo.” Iwo anawonjezera kuti: “Chomwe tinkafunika kuchita ndi kutanganidwa ndi ntchito ya Ambuye.” M’bale Macmillan anatanganidwadi ndi ntchitoyi. Ankachita khama pa ntchito yolalikira. Anali ndi mwayi wolimbikitsa abale ambiri amene anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali. Nthawi zonse iwo ankapezeka pamisonkhano ya mpingo ngakhale m’zaka zawo za ukalamba. Kodi M’bale Macmillan anapindula bwanji chifukwa chakuti ankatanganidwa kutumikira Yehova pamene ankayembekezera kulandira mphoto yawo? Atatsala pang’ono kumwalira mu 1966, analemba kuti: “Chikhulupiriro changa sichinafookepo ngakhale pang’ono.” Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri chimene tonsefe tiyenera kutengera, makamaka ngati tapirira kwa nthawi yaitali kuposa mmene timayembekezerera.​—Aheb. 13:7.

16. Kodi M’bale Herbert Jennings ndi mkazi wake anakumana ndi vuto lotani mosayembekezereka? (Yakobo 4:14)

16 Atumiki ambiri a Yehova amakumana ndi mavuto okhudza thanzi lawo mosayembekezereka. Mwachitsanzo, munkhani yokhudza mbiri ya moyo wake, M’bale Herbert Jennings b anafotokoza mmene iye ndi mkazi wake ankasangalalira ndi utumiki wa umishonale ku Ghana. Komabe patapita nthawi, iye anapezeka ndi matenda a m’maganizo. Poganizira mawu a pa Yakobo 4:14, M’bale Jennings anatchula kuti zomwe zinamuchitikirazi “ndi ‘mawa’ lomwe sitinkayembekezera.” (Werengani.) Iye analemba kuti: “Tinkafunika kuvomereza, ndipo tinakonza zoti tisamuke ku Ghana, kusiya anzathu apamtima n’kupita ku Canada [kuti ndikalandire thandizo lamankhwala].” Yehova anathandiza M’bale Jennings ndi mkazi wake kuti apitirize kumutumikira mokhulupirika ngakhale ankakumana ndi mavuto.

17. Kodi chitsanzo cha M’bale Jennings chinathandiza bwanji Akhristu ena?

17 Zimene M’bale Jennings anafotokoza moona mtima mu mbiri ya moyo wake zinakhudza kwambiri anthu ena. Mlongo wina analemba kuti: “Sindinakhudzidwepo kwambiri ngati mmene ndinachitira nditawerenga nkhaniyi. . . . Kuwerenga mmene M’bale Jennings anachitira posiya utumiki wawo kuti akalandire thandizo lamankhwala kunandithandiza kuti ndiziona zinthu moyenera pa moyo wanga.” M’bale wina analembanso kuti: “Nditatumikira monga mkulu mumpingo kwa zaka 10, ndinkafunika kusiya udindowu chifukwa cha matenda a maganizo. Ndinkangodziona ngati munthu wolephera ndipo ndinkada nkhawa kwambiri moti sindinkatha kuwerenga nkhani zofotokoza mbiri za moyo wa anthu ena. . . . Koma kupirira kwa M’bale Jennings kunandilimbikitsa kwambiri.” Zimenezi zikutikumbutsa kuti tikamapirira mavuto osayembekezereka, tingalimbikitse ena. Ngakhale kuti zinthu sizingachitike m’njira imene timayembekezera, tingathe kukhala chitsanzo kwa ena pa nkhani ya kukhulupirika komanso kupirira.​—1 Pet. 5:9.

Tikamadalira Yehova, mavuto osayembekezereka omwe tingakumane nawo angachititse kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba (Onani ndime 18)

18. Monga mmene tikuonera pa zithunzizi, kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira mlongo wamasiye wa ku Nigeria?

18 Mavuto adzidzidzi monga mliri wa COVID-19, akhudza atumiki ambiri a Yehova. Mlongo wina wamasiye ku Nigeria anatsala ndi chakudya komanso ndalama zochepa kwambiri. M’mawa wa tsiku lina mwana wake wamkazi anamufunsa kuti adya chiyani, popeza anali atangophika kapu yomaliza ya mpunga womwe anali nawo. Mlongo wathuyo anauza mwana wake wakeyo kuti analibe ndalama komanso chakudya chilichonse choncho ankangofunika kutsanzira mkazi wamasiye wa ku Zarefati pokonza chakudya chomaliza chomwe anali nacho n’kumadalira Yehova. (1 Maf. 17:8-16) Asanayambe n’komwe kuganizira kuti adya chiyani masana a tsikulo, iwo analandira thandizo la zinthu zomwe ankafunikira kuchokera kwa Akhristu anzawo. Pa zinthuzo panali chakudya chokwanira kudya kwa milungu yoposa iwiri. Mlongoyo ananena kuti sankadziwa kuti Yehova ankamvetsera zimene ankalankhula ndi mwana wakeyo. Kunena zoona, tikamadalira Yehova, mavuto omwe tingakumane nawo angatithandize kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba.​—1 Pet. 5:6, 7.

19. Kodi M’bale Aleksey Yershov anazunzika motani?

19 M’zaka za posachedwapa abale ndi alongo athu ambiri akhala akupirira kuzunzidwa kumene samayembekezera. Taganizirani zomwe zinachitikira M’bale Aleksey Yershov amene amakhala ku Russia. Anthu a Yehova m’dzikoli anali pa ufulu pa nthawi imene M’bale Yershov ankabatizidwa mu 1994. Komabe m’zaka zotsatira zinthu zinasintha ku Russia. Mu 2020, apolisi anakalowa komanso kufufuza nyumba ya M’bale Yershov ndipo analanda zinthu zambiri. Patapita miyezi ingapo, boma linamutsegulira milandu. Zinthu zinaipa kwambiri pamene munthu wina yemwe ankanamizira kuphunzira Baibulo kwa nthawi yoposa chaka, anaonetsa vidiyo yomwe ankajambula ngati umboni pa mlanduwu. Zimenezitu zinali zoipa kwambiri.

20. Kodi M’bale Yershov anatani kuti apitirize kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova?

20 Kodi panakhala zotsatirapo zabwino zilizonse chifukwa cha kupirira kwa M’bale Yershov? Inde. Ubwenzi wake ndi Yehova unalimba kwambiri. Iye ananena kuti: “Panopa ine ndi mkazi wanga timapemphera limodzi pafupipafupi. Ndimadziwa kuti sindikanatha kupirira popanda kuthandizidwa ndi Yehova.” Anawonjezera kuti: “Kuphunzira pandekha kwandithandiza kuti ndisafooke. Ndimaganizira mozama zitsanzo za atumiki okhulupirika akale. Pali nkhani zambiri zotchulidwa m’Baibulo, zosonyeza kufunika kokhala osatekeseka komanso kudalira Yehova.”

21. Kodi taphunzira chiyani munkhaniyi?

21 Kodi taphunzira chiyani munkhaniyi? Nthawi zina tingakumane ndi mavuto osayembekezereka m’dzikoli. Ngakhale zili choncho, nthawi zonse Yehova amathandiza atumiki ake akamamudalira. Monga mmene lemba limene likutsogolera nkhaniyi lanenera, “masoka a munthu wolungama ndi ochuluka, koma Yehova amamupulumutsa ku masoka onsewo.” (Sal. 34:19) M’malo momangoganizira mavuto amene takumana nawo, tiyeni tipitirize kuganizira mmene Yehova amatipatsira mphamvu kuti tithe kuwapirira. Tikatero mofanana ndi mtumwi Paulo tidzanena kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”​—Afil. 4:13.

NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa

a Ngakhale kuti m’dzikoli tingakumane ndi mavuto osayembekezereka, tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzathandiza atumiki ake okhulupirika. Ndiye kodi Yehova anathandiza bwanji atumiki ake m’mbuyomo? Nanga kodi amatithandiza bwanji masiku ano? Kukambirana zitsanzo za anthu otchulidwa m’Baibulo komanso a masiku ano kungatithandize kuti tizimudalira kwambiri kuti nafenso adzatithandiza.